Masalimo 24 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 24:1-10

Salimo 24

Salimo la Davide.

1Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo,

dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo;

2pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanja

ndi kulikhazika pamwamba pa madzi.

3Ndani angakwere phiri la Yehova?

Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika?

4Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera,

amene sapereka moyo wake kwa fano

kapena kulumbira mwachinyengo.

5Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehova

ndipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.

6Umenewo ndiwo mʼbado wa amene amafunafuna Yehova;

amene amafunafuna nkhope yanu, Inu Mulungu wa Yakobo.

Sela

7Tukulani mitu yanu inu zipata;

tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,

kuti Mfumu yaulemerero ilowe.

8Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?

Yehova Wamphamvuzonse,

Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo.

9Tukulani mitu yanu, inu zipata;

tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,

kuti Mfumu yaulemerero ilowe.

10Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?

Yehova Wamphamvuzonse,

Iye ndiye Mfumu yaulemerero.

Sela