Masalimo 22 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 22:1-31

Salimo 22

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa “Mbawala yayikazi ya Mmawa.” Salimo la Davide.

1Mulungu wanga, Mulungu wanga, nʼchifukwa chiyani mwandisiya?

Chifuwa chiyani simukundithandiza ndi pangʼono pomwe?

Nʼchifukwa chiyani simukumva mawu a kudandaula kwanga?

2Inu Mulungu wanga, ine ndimalira masana, koma simuyankha,

usikunso, ndipo sindikhala chete.

3Inu ndinu Woyera, wokhala pa mpando waufumu;

ndinu matamando a Israeli.

4Pa inu makolo athu anadalira;

iwo anadalira ndipo Inu munawapulumutsa.

5Analirira kwa inu ndipo munawapulumutsa.

Iwo anakhulupirira Inu ndipo simunawakhumudwitse.

6Koma ine ndine nyongolotsi osati munthu,

wosekedwa ndi wonyozedwa ndi anthu onse.

7Onse amene amandiona amandiseka;

amandiyankhulira mawu achipongwe akupukusa mitu yawo kunena kuti

8“Iyeyu amadalira Yehova,

musiyeni Yehovayo amulanditse.

Musiyeni Yehova amupulumutse

popeza amakondwera mwa Yehovayo.”

9Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga.

Munachititsa kuti ndizikudalirani

ngakhale pa nthawi imene ndinkayamwa.

10Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu;

kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga.

11Musakhale kutali ndi ine,

pakuti mavuto ali pafupi

ndipo palibe wina wondipulumutsa.

12Ngʼombe zazimuna zandizungulira;

ngʼombe zazimuna zamphamvu za ku Basani zandizinga.

13Mikango yobangula pokadzula nyama,

yatsekula kwambiri pakamwa pawo kulimbana nane.

14Ine ndatayika pansi ngati madzi

ndipo mafupa anga onse achoka mʼmalo mwake.

Mtima wanga wasanduka phula;

wasungunuka mʼkati mwanga.

15Mphamvu zanga zauma ngati phale,

ndipo lilime langa lamamatira ku nsagwada;

mwandigoneka mʼfumbi la imfa.

16Agalu andizungulira;

gulu la anthu oyipa landizinga.

Alasa manja ndi mapazi anga.

17Ine nditha kuwerenga mafupa anga onse;

anthu amandiyangʼanitsitsa ndi kundidzuma.

18Iwo agawana zovala zanga pakati pawo

ndi kuchita maere pa zovala zangazo.

19Koma Inu Yehova, musakhale kutali;

Inu mphamvu yanga, bwerani msanga kuti mudzandithandize.

20Pulumutsani moyo wanga ku lupanga,

moyo wanga wopambanawu ku mphamvu ya agalu.

21Ndilanditseni mʼkamwa mwa mikango;

pulumutseni ku nyanga za njati.

22Ine ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga;

ndidzakutamandani mu msonkhano.

23Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni!

Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni!

Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli!

24Pakuti Iye sanapeputse kapena kunyoza

kuvutika kwa wosautsidwayo;

Iye sanabise nkhope yake kwa iye.

Koma anamvera kulira kwake kofuna thandizo.

25Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira.

Ndidzakwaniritsa lonjezo langa pamaso pa amene amaopa Inu.

26Osauka adzadya ndipo adzakhuta;

iwo amene amafunafuna Yehova adzamutamanda.

Mitima yanu ikhale ndi moyo mpaka muyaya!

27Malekezero onse a dziko lapansi

adzakumbukira Yehova ndi kutembenukira kwa Iye,

ndipo mabanja a mitundu ya anthu

adzawerama pamaso pake,

28pakuti ulamuliro ndi wake wa Yehova

ndipo Iye amalamulira anthu a mitundu yonse.

29Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira;

onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake;

iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo.

30Zidzukulu zamʼtsogolo zidzamutumikira Iye;

mibado ya mʼtsogolo idzawuzidwa za Ambuye.

31Iwo adzalengeza za chilungamo chake

kwa anthu amene pano sanabadwe

pakuti Iye wachita zimenezi.

New Russian Translation

Псалтирь 22:1-6

Псалом 22

1Псалом Давида.

Господь – Пастырь мой;

я ни в чем не буду нуждаться.

2Он покоит меня на зеленых пастбищах

и водит меня к тихим водам.

3Он душу мою оживляет

и ведет меня по путям праведности

ради имени Своего.

4Пусть пойду в темноте долины смерти,

не устрашусь я зла,

потому что Ты со мной;

Твой жезл и Твой посох –

они успокаивают меня.

5Ты приготовил мне пир

на виду у моих врагов,

умастил мне голову маслом,

и чаша моя полна.

6Так, благо и милость да будут со мною

все дни моей жизни,

и пребуду я в доме Господнем многие дни.