Masalimo 18 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 18:1-50

Salimo 18

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide mtumiki wa Yehova. Iye anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli.

1Davide anati: Ine ndimakukondani Inu Yehova, mphamvu zanga.

2Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga;

Mulungu wanga ndi thanthwe langa mʼmene ndimathawiramo.

Chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa, ndi linga langa.

3Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,

ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.

4Zingwe za imfa zinandizinga;

mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.

5Anandimanga ndi zingwe za ku manda;

misampha ya imfa inalimbana nane.

6Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;

ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize.

Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga;

kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.

7Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi,

ndipo maziko a mapiri anagwedezeka;

ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.

8Mʼmphuno mwake munatuluka utsi;

moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake,

makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.

9Iye anangʼamba thambo natsika pansi;

pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda.

10Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka;

nawuluka ndi mphepo mwaliwiro.

11Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake,

chophimba chake chomuzungulira chinali mitambo yakuda ya mlengalenga.

12Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake munkachokera matalala,

makala amoto ndi ziphaliwali zongʼanima.

13Yehova anabangula kumwamba ngati bingu,

mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.

14Iye anaponya mivi yake nabalalitsa adani ake,

ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.

15Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera;

maziko a dziko lapansi anakhala poyera,

Yehova atabangula mwaukali,

pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwanu.

16Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira;

anandivuwula mʼmadzi ozama.

17Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,

adani anga, amene anali amphamvu kuposa ine.

18Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto,

koma Yehova anali thandizo langa.

19Iye anandipititsa kumalo otakasuka;

anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.

20Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa;

molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.

21Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova;

ndilibe mlandu wochoka pamaso Mulungu wanga.

22Malamulo ake onse ali pamaso panga;

sindinasiye malangizo ake.

23Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake

ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.

24Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa,

molingana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.

25Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu;

kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,

26kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu,

koma kwa achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.

27Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa,

koma anthu amtima odzikuza mumawatsitsa.

28Inu Yehova, sungani nyale yanga kuti iziyakabe;

Mulungu wanga wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.

29Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo;

ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.

30Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro;

mawu a Yehova alibe cholakwika.

Iye ndi chishango

kwa onse amene amathawira kwa Iye.

31Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova?

Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?

32Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu

ndi kulungamitsa njira yanga.

33Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi;

Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri.

34Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo;

manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo.

35Inu mumandipatsa chishango chachipambano,

ndipo dzanja lanu lamanja limandichirikiza;

mumawerama pansi kundikuza.

36Munakulitsa njira yoyendamo ine,

kuti mapazi anga asaguluke.

37Ndinathamangitsa adani anga ndi kuwapitirira;

sindinabwerere mpaka atawonongedwa.

38Ndinakantha adaniwo kotero kuti sanathenso kudzuka;

anagwera pa mapazi anga.

39Inu munandiveka ndi mphamvu yokachitira nkhondo,

munachititsa kuti ndigonjetse adani anga.

40Inu munachititsa adani anga kutembenuka, kuonetsa misana yawo pothawa,

ndipo ine ndinawononga adani angawo.

41Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa.

Analirira kwa Yehova koma sanawayankhe.

42Ine ndinawaperesa ngati fumbi lowuluka ndi mphepo.

Ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.

43Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa anthu;

mwandisandutsa kukhala mtsogoleri wa anthu a mitundu ina.

Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.

44Alendo amadzipereka okha pamaso panga;

akangomva za ine amandigonjera.

45Iwo onse anataya mtima;

anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.

46Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa!

Akuzike Mulungu Mpulumutsi wanga!

47Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango,

amene amagonjetsa anthu a mitundu yonse amene ali pansi pa ulamuliro wanga,

48amene amandipulumutsa mʼmanja mwa adani anga.

Inu munandikuza kuposa adani anga;

munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.

49Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa anthu a mitundu ina, Inu Yehova;

ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.

50Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake;

amaonetsa chikondi chosasinthika kwa wodzozedwa wake,

kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.

New Russian Translation

Псалтирь 18:1-15

Псалом 18

1Дирижеру хора. Псалом Давида.

2Небеса провозглашают Божью славу,

о делах Его рук возвещает их свод;

3изо дня в день вещают они,

каждую ночь открывают знание.

4Хотя они не используют ни речи, ни слов,

и от них не слышно ни звука,

5их голос18:5 Так в некоторых древних переводах; в нормативном еврейском тексте: «черта». проходит по всей земле,

их слова – до краев света.

В небесах Он поставил шатер для солнца,

6и оно выходит, словно жених из спальни своей,

и, как бегун, радуется предстоящему забегу.

7Встает оно на одном краю небес

и совершает свой путь к другому краю,

и ничто от жара его не скрыто.

8Закон Господа совершенен,

обновляет душу.

Предписание Господа непреложно,

умудряет простых.

9Наставления Господа праведны,

радуют сердце.

Повеления Господа лучезарны,

просветляют глаза.

10Страх Господень чист,

пребывает вовеки.

Определения Господа истинны

и все праведны.

11Они желаннее золота,

даже множества золота чистого;

слаще, нежели мед,

нежели капли из сот.

12Слуга Твой ими храним,

в соблюдении их большая награда.

13Кто к ошибкам своим не слеп?

От невольных проступков меня очисти

14и от сознательных грехов удержи Своего слугу,

не дай им власти надо мной.

Тогда я буду непорочен

и чист от большого греха.

15Пусть слова моих уст и раздумья моего сердца

будут угодны Тебе, Господи,

моя Скала и мой Искупитель!