Masalimo 17 – CCL & NIV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 17:1-15

Salimo 17

Pemphero la Davide.

1Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo;

mverani kulira kwanga.

Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa

popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.

2Kusalakwa kwanga kuchokera kwa inu;

maso anu aone chimene ndi cholungama.

3Ngakhale Inu mutafufuza mtima wanga ndi kundisanthula usiku,

ngakhale mutandiyesa, simudzapeza kanthu;

Ine ndatsimikiza kuti pakamwa panga sipadzachimwa.

4Kunena za ntchito za anthu,

monga mwa mawu a pakamwa panu,

Ine ndadzisunga ndekha

posatsata njira zachiwawa.

5Mayendedwe anga akhazikika pa njira zanu;

mapazi anga sanaterereke.

6Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha;

tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa.

7Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu,

Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja

iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.

8Mundisunge ine ngati mwanadiso;

mundibise mu mthunzi wa mapiko anu,

9kuchoka kwa oyipa amene amandizinga ine,

kuchoka kwa anthu amene ndi adani anga, amene andizungulira ine.

10Iwo amatseka mitima yawo yopanda chifundo,

ndi pakamwa pawo amayankhula modzitamandira.

11Andisaka, tsopano andizungulira

ndi maso awo atcheru, kuti andigwetse pansi.

12Iwo ali ngati mkango wofuna nyama;

ngati mkango waukulu wokhala mobisala.

13Dzukani Yehova, mulimbane nawo ndipo muwagwetse pansi;

landitseni kuchoka kwa oyipa ndi lupanga lanu.

14Inu Yehova, pulumutseni ndi dzanja lanu kwa anthu otere,

kwa anthu a dziko lino amene mphotho yawo ili mʼmoyo uno.

Inu mumaletsa njala kwa amene asangalatsidwa nanu;

ana awo aamuna ali ndi zinthu zambiri,

ndipo iwo amasunga chuma cha ana awo.

15Ndipo ine mʼchilungamo ndidzaona nkhope yanu;

pamene ndidzadzuka, ndidzakondwera kwambiri poonana nanu.

New International Version

Psalms 17:1-15

Psalm 17

A prayer of David.

1Hear me, Lord, my plea is just;

listen to my cry.

Hear my prayer—

it does not rise from deceitful lips.

2Let my vindication come from you;

may your eyes see what is right.

3Though you probe my heart,

though you examine me at night and test me,

you will find that I have planned no evil;

my mouth has not transgressed.

4Though people tried to bribe me,

I have kept myself from the ways of the violent

through what your lips have commanded.

5My steps have held to your paths;

my feet have not stumbled.

6I call on you, my God, for you will answer me;

turn your ear to me and hear my prayer.

7Show me the wonders of your great love,

you who save by your right hand

those who take refuge in you from their foes.

8Keep me as the apple of your eye;

hide me in the shadow of your wings

9from the wicked who are out to destroy me,

from my mortal enemies who surround me.

10They close up their callous hearts,

and their mouths speak with arrogance.

11They have tracked me down, they now surround me,

with eyes alert, to throw me to the ground.

12They are like a lion hungry for prey,

like a fierce lion crouching in cover.

13Rise up, Lord, confront them, bring them down;

with your sword rescue me from the wicked.

14By your hand save me from such people, Lord,

from those of this world whose reward is in this life.

May what you have stored up for the wicked fill their bellies;

may their children gorge themselves on it,

and may there be leftovers for their little ones.

15As for me, I will be vindicated and will see your face;

when I awake, I will be satisfied with seeing your likeness.