Masalimo 146 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 146:1-10

Salimo 146

1Tamandani Yehova.

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.

2Ndidzatamanda Yehova ndi moyo wanga wonse;

ndidzayimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.

3Musamadalire mafumu,

anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa.

4Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi;

zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo.

5Wodala ndi amene thandizo lake ndi

Mulungu wa Yakobo.

6Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,

nyanja ndi zonse zili mʼmenemo;

Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.

7Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa

ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala.

Yehova amamasula amʼndende,

8Yehova amatsekula maso anthu osaona,

Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,

Yehova amakonda anthu olungama.

9Yehova amasamalira alendo

ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye,

koma amasokoneza njira za anthu oyipa.

10Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya,

Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse.

Tamandani Yehova.