Masalimo 145 – CCL & CARST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 145:1-21

Salimo 145

Salimo la matamando la Davide.

1Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu yanga;

ndidzatamanda dzina lanu ku nthawi za nthawi.

2Ndidzakutamandani tsiku ndi tsiku

ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.

3Yehova ndi wamkulu ndi woyenera matamando onse;

ukulu wake palibe angawumvetsetse.

4Mʼbado wina udzayamikira ntchito yanu kwa mʼbado wina;

Iwo adzafotokoza za machitidwe anu amphamvu.

5Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu,

ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.

6Iwo adzafotokoza za mphamvu ya ntchito zanu zoopsa kwambiri,

ndipo ine ndidzalengeza za ntchito zanu zazikulu.

7Adzakondwerera kuchuluka kwa ubwino wanu,

ndi kuyimba mwachimwemwe za chilungamo chanu.

8Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo,

wosakwiya msanga ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika.

9Yehova ndi wabwino kwa onse;

amachitira chifundo zonse zimene anazipanga.

10Zonse zimene munazipanga zidzakutamandani, Inu Yehova;

oyera mtima adzakulemekezani.

11Iwo adzafotokoza za ulemerero wa ufumu wanu

ndi kuyankhula za mphamvu yanu,

12kuti anthu onse adziwe za machitidwe anu amphamvu

ndi ulemerero wokongola wa ufumu wanu.

13Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,

ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse.

Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse

ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.

14Yehova amagwiriziza onse amene akugwa

ndipo amakweza onse otsitsidwa.

15Maso a onse amayangʼana kwa Inu,

ndipo Inu mumawapatsa chakudya chawo pa nthawi yoyenera.

16Mumatsekula dzanja lanu

ndi kukwaniritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.

17Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse,

ndi wokonda zonse zimene anazipanga.

18Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana,

onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi.

19Iye amakwaniritsa zokhumba za iwo amene amamuopa;

amamva kulira kwawo ndi kuwapulumutsa.

20Yehova amayangʼana onse amene amamukonda

koma adzawononga anthu onse oyipa.

21Pakamwa panga padzayankhula zotamanda Yehova.

Cholengedwa chilichonse chitamande dzina lake loyera

ku nthawi za nthawi.

Священное Писание (Восточный перевод), версия для Таджикистана

Забур 145:1-10

Песнь 145

1Славьте Вечного!

Восхваляй, душа моя, Вечного!

2Всю свою жизнь буду восхвалять Вечного;

буду петь хвалу моему Богу, пока я жив.

3Не надейтесь на правителей,

они всего лишь люди и не могут вас спасти.

4Когда дух покидает их, и они возвращаются в землю,

в тот самый день исчезают и все их помышления.

5Благословен тот, кому помощник Бог Якуба,

кто надеется на Вечного, своего Бога,

6сотворившего небо и землю,

море и всё, что его наполняет, –

на Вечного, Который хранит Свою верность вовеки.

7Он защищает дело угнетённых,

даёт пищу голодным.

Вечный освобождает заключённых,

8Вечный открывает глаза слепым,

Вечный поднимает всех низверженных,

Вечный любит праведных.

9Вечный хранит чужеземцев,

поддерживает сирот и вдов,

а путь нечестивых искривляет.

10Вечный будет царствовать вовеки,

Твой Бог, Сион, – во все поколения.

Славьте Вечного!