Masalimo 136 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 136:1-26

Salimo 136

1Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino.

Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

2Yamikani Mulungu wa milungu.

Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

3Yamikani Ambuye wa ambuye,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

4Iye yekhayo amene amachita zodabwitsa zazikulu,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

5Amene mwachidziwitso chake anapanga mayiko akumwamba,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

6Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

7Amene anapanga miyuni ikuluikulu,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

8Dzuwa lilamulire usana,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

9Mwezi ndi nyenyezi zilamulire usiku,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

10Amene anakantha ana woyamba kubadwa a Igupto,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

11Natulutsa Israeli pakati pawo,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

12Ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

13Amene anagawa Nyanja Yofiira pakati,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

14Nadutsitsa Israeli pakati pa nyanjayo,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

15Koma anakokolola Farao ndi ankhondo ake mʼNyanja Yofiira,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

16Amene anatsogolera anthu ake mʼchipululu

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

17Amene anakantha mafumu akuluakulu,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

18Napha mafumu amphamvu,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

19Siloni mfumu ya Aamori,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

20Ogi mfumu ya Basani,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

21Napereka dziko lawo ngati cholowa,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

22Cholowa cha mtumiki wake Israeli;

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

23Amene anatikumbukira ife anthu opeputsidwa,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

24Amene anatimasula kwa adani athu,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

25Amene amapereka chakudya kwa cholengedwa chilichonse,

pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

26Yamikani Mulungu wakumwamba,