Masalimo 131 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 131:1-3

Salimo 131

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Davide.

1Inu Yehova, mtima wanga siwodzikuza,

maso anga siwonyada;

sinditengeteka mtima

ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa.

2Koma moyo wanga ndawutontholetsa

ndi kuwukhalitsa chete ngati mwana amene amayi ake amuletsa kuyamwa,

moyo wanga mʼkati mwanga uli ngati mwana amene amuletsa kuyamwa.

3Yembekeza Yehova, iwe Israeli,

kuyambira tsopano mpaka muyaya.