Masalimo 128 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 128:1-6

Salimo 128

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Odala ndi onse amene amaopa Yehova,

amene amayenda mʼnjira zake.

2Udzadya chipatso cha ntchito yako;

madalitso ndi chuma zidzakhala zako.

3Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka

mʼkati mwa nyumba yako;

ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi

kuzungulira tebulo lako.

4Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa

amene amaopa Yehova.

5Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni

masiku onse a moyo wako;

uwone zokoma za Yerusalemu,

6ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako.

Mtendere ukhale ndi Israeli.