Masalimo 127 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 127:1-5

Salimo 127

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Solomoni.

1Yehova akapanda kumanga nyumba,

omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe.

Yehova akapanda kulondera mzinda,

mlonda akanangolondera pachabe.

2Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa

ndi kusagona msanga madzulo,

kuvutikira chakudya choti mudye,

pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.

3Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,

ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.

4Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja

mwa munthu wankhondo.

5Wodala munthu

amene motengera mivi mwake mwadzaza.

Iwo sadzachititsidwa manyazi

pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.