Masalimo 124 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 124:1-8

Salimo 124

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,

anene tsono Israeli,

2akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,

potiwukira anthuwo,

3iwo atatipsera mtima,

akanatimeza amoyo;

4chigumula chikanatimiza,

mtsinje ukanatikokolola,

5madzi a mkokomo

akanatikokolola.

6Atamandike Yehova,

amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo.

7Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame

yokodwa mu msampha wa mlenje;

msampha wathyoka,

ndipo ife tapulumuka.

8Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova

wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.