Masalimo 121 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 121:1-8

Salimo 121

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Ndikweza maso anga ku mapiri;

kodi thandizo langa limachokera kuti?

2Thandizo langa limachokera kwa Yehova,

wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

3Sadzalola kuti phazi lako literereke;

Iye amene amakusunga sadzawodzera.

4Taonani, Iye amene amasunga Israeli

sadzawodzera kapena kugona.

5Yehova ndiye amene amakusunga;

Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.

6Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana,

kapena mwezi nthawi ya usiku.

7Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;

adzasunga moyo wako.

8Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;

kuyambira tsopano mpaka muyaya.