Masalimo 116 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 116:1-19

Salimo 116

1Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga;

Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo.

2Pakuti ananditchera khutu,

ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga.

3Zingwe za imfa zinandizinga,

zoopsa za ku dziko la anthu akufa zinandigwera;

ndinapeza mavuto ndi chisoni.

4Pamenepo ndinayitana dzina la Yehova:

“Inu Yehova, pulumutseni!”

5Yehova ndi wokoma mtima ndi wolungama

Mulungu wathu ndi wodzaza ndi chifundo.

6Yehova amateteza munthu wodzichepetsa mtima;

pamene ndinali ndi chosowa chachikulu, Iye anandipulumutsa.

7Pumula iwe moyo wanga,

pakuti Yehova wakuchitira zokoma.

8Pakuti Inu Yehova mwapulumutsa moyo wanga ku imfa,

maso anga ku misozi,

mapazi anga kuti angapunthwe,

9kuti ine ndiyende pamaso pa Yehova

mʼdziko la anthu amoyo.

10Ine ndinakhulupirira; choncho ndinati,

“Ndasautsidwa kwambiri.”

11Ndipo ndili mʼnkhawa yanga ndinati,

“Anthu onse ndi abodza.”

12Ndingamubwezere chiyani Yehova,

chifukwa cha zokoma zake zonse zimene wandichitira?

13Ndidzakweza chikho cha chipulumutso

ndipo ndidzayitana dzina la Yehova.

14Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova

pamaso pa anthu ake onse.

15Imfa ya anthu oyera mtima

ndi yamtengowapatali pamaso pa Yehova.

16Inu Yehova, zoonadi ndine mtumiki wanu:

ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu;

Inu mwamasula maunyolo anga.

17Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu

ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.

18Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova

pamaso pa anthu ake onse,

19mʼmabwalo a nyumba ya Yehova,

mʼkati mwako iwe Yerusalemu.

Tamandani Yehova.

New Russian Translation

Псалтирь 116:1-2

Псалом 116

1Славьте Господа, все народы!

Пойте хвалу Ему, все люди!

2Потому что велика Его милость к нам

и истина Его навеки.

Аллилуйя!