Masalimo 115 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 115:1-18

Salimo 115

1Kwa ife ayi Yehova, kwa ife ayi

koma ulemerero ukhale pa dzina lanu,

chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika ndiponso chifukwa cha kukhulupirika kwanu.

2Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akunena kuti,

“Mulungu wawo ali kuti?”

3Mulungu wathu ali kumwamba;

Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.

4Koma mafano awo ndi siliva ndi golide,

opangidwa ndi manja a anthu.

5Pakamwa ali napo koma sayankhula,

maso ali nawo koma sapenya;

6makutu ali nawo koma samva,

mphuno ali nazo koma sanunkhiza;

7manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu;

mapazi ali nawo koma sayenda;

kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu.

8Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo,

chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.

9Inu Aisraeli, dalirani Yehova;

Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.

10Iwe nyumba ya Aaroni, dalira Yehova;

Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.

11Inu amene mumaopa Iye, dalirani Yehova;

Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.

12Yehova watikumbukira ndipo adzatidalitsa:

adzadalitsa nyumba ya Israeli,

adzadalitsa nyumba ya Aaroni,

13adzadalitsa iwo amene amaopa Yehova;

aangʼono ndi aakulu omwe.

14Yehova akuwonjezereni madalitso;

inuyo pamodzi ndi ana anu.

15Mudalitsidwe ndi Yehova,

Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

16Kumwamba ndi kwa Yehova,

koma dziko lapansi Iye walipereka kwa anthu.

17Si anthu akufa amene amatamanda Yehova,

amene amatsikira kuli chete;

18ndi ife amene timatamanda Yehova,

kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Tamandani Yehova.