Masalimo 111 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 111:1-10

Salimo 111

1Tamandani Yehova.

Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse

mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano.

2Ntchito za Yehova nʼzazikulu;

onse amene amakondwera nazo amazilingalira.

3Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu,

ndipo chilungamo chake ndi chosatha.

4Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike;

Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo.

5Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye;

amakumbukira pangano lake kwamuyaya.

6Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake,

kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina.

7Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama;

malangizo ake onse ndi odalirika.

8Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi,

ochitidwa mokhulupirika ndi molungama.

9Iyeyo amawombola anthu ake;

anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya

dzina lake ndi loyera ndi loopsa.

10Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru;

onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu.

Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.