Masalimo 11 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 11:1-7

Salimo 11

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1Mwa Yehova ine ndimathawiramo.

Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti,

“Thawira ku phiri lako ngati mbalame.

2Pakuti taona oyipa akunga mauta awo;

ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta,

pobisala pawo kuti alase

olungama mtima.

3Tsono ngati maziko awonongeka,

olungama angachite chiyani?”

4Yehova ali mʼNyumba yake yoyera;

Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba.

Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu;

maso ake amawayesa.

5Yehova amayesa olungama,

koma moyo wake umadana ndi oyipa,

amene amakonda zachiwawa.

6Iye adzakhuthulira pa oyipa

makala amoto ndi sulufule woyaka;

mphepo yotentha idzakhala yowayenera.

7Pakuti Yehova ndi wolungama,

Iye amakonda chilungamo;

ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.