Masalimo 109 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 109:1-31

Salimo 109

Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Salimo la Davide.

1Mulungu amene ndimakutamandani,

musakhale chete,

2pakuti anthu oyipa ndi achinyengo

atsekula pakamwa pawo kutsutsana nane;

iwo ayankhula motsutsana nane ndi malilime abodza.

3Andizungulira ndi mawu audani,

amandinena popanda chifukwa.

4Mʼmalo mwa chikondi changa amandineneza,

koma ine ndine munthu wapemphero.

5Iwo amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino,

ndi udani mʼmalo mwa chikondi changa.

6Sankhani munthu woyipa kuti amutsutse iye;

lolani wotsutsa ayime ku dzanja lake lamanja.

7Pamene aweruzidwa, apezeke kuti ndi wolakwa,

ndipo mapemphero ake amutsutse.

8Masiku ake akhale owerengeka;

munthu wina atenge malo ake a utsogoleri.

9Ana ake akhale amasiye

ndipo mkazi wake akhale wopanda mwamuna.

10Ana ake akhale oyendayenda ndi opemphapempha;

apirikitsidwe kuchoka pa mabwinja a nyumba zawo.

11Wokongoza alande zonse zimene ali nazo;

alendo afunkhe ntchito za manja ake.

12Pasapezeke ndi mmodzi yemwe womukomera mtima

kapena kumvera chisoni ana ake amasiye.

13Zidzukulu zake zithe nʼkufa,

mayina awo afafanizidwe mu mʼbado wotsatirawo.

14Mphulupulu za makolo ake zikumbukiridwe pamaso pa Yehova;

tchimo la amayi ake lisadzafafanizidwe.

15Machimo awo akhale pamaso pa Yehova nthawi zonse,

kuti Iye achotse chikumbutso chawo pa dziko lapansi.

16Pakuti iye sanaganizirepo zochita chifundo,

koma anazunza mpaka kuwapha anthu osauka

ndi osweka mtima.

17Anakonda kutemberera,

matembererowo abwerere kwa iye;

sanakondwe nʼkudalitsa anthu ena,

choncho madalitso akhale kutali naye.

18Anavala kutemberera ngati chovala;

kutemberera kunalowa mʼthupi lake ngati madzi,

kulowa mʼmafupa ake ngati mafuta.

19Matemberero akhale ngati chofunda chodzikutira nacho,

ngati lamba wovala tsiku ndi tsiku.

20Awa akhale malipiro ochokera kwa Yehova pa onditsutsa anga,

kwa iwo amene amayankhula zoyipa za ine.

21Koma Inu Ambuye Wamphamvuzonse,

muchite nane molingana ndi dzina lanu,

chifukwa cha ubwino wa chikondi chanu, pulumutseni.

22Pakuti ndine wosauka ndi wosowa,

ndipo mtima wanga ukuwawa mʼkati mwanga.

23Ndikuzimirira ngati mthunzi wa kumadzulo,

ndapirikitsidwa ngati dzombe.

24Mawondo anga afowoka chifukwa cha kusala zakudya,

thupi langa lawonda ndi mutu wanga womwe.

25Ndine chinthu chotonzedwa kwa otsutsana nane;

akandiona, amapukusa mitu yawo.

26Thandizeni Inu Yehova Mulungu wanga;

pulumutseni molingana ndi chikondi chanu.

27Adaniwo adziwe kuti limeneli ndi dzanja lanu,

kuti Inu Yehova mwachita zimenezi.

28Angathe kutemberera, koma Inu mudzadalitsa;

pamene iwo andiputa adzachititsidwa manyazi,

koma mtumiki wanu adzasangalala.

29Onditsutsa adzavekedwa mnyozo,

ndipo adzadzifunditsa manyazi ngati chovala.

30Ndi pakamwa panga ndidzathokoza Yehova kwambiri;

ndidzamutamanda mʼgulu lalikulu la anthu.

31Popeza Iye amayima ku dzanja lamanja la munthu wosowayo,

kupulumutsa moyo wake kwa iwo amene agamula molakwa.