Masalimo 108 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 108:1-13

Salimo 108

Nyimbo. Salimo la Davide.

1Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu;

ndidzayimba nyimbo, inde ndidzayimba nyimbo zotamanda ndi moyo wanga wonse.

2Dzukani, zeze ndi pangwe!

Ine ndidzadzutsa mʼbandakucha.

3Ndidzakutamandani Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina;

ndidzayimba za Inu pakati pa anthu a mitundu ina.

4Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kutalika kwake kuposa kumwamba;

kukhulupirika kwanu kumafika mlengalenga.

5Kwezekani Inu Mulungu, kuposa mayiko akumwamba,

ndipo ulemerero wanu uphimbe dziko lonse lapansi.

6Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja

kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.

7Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika:

“Mwachipambano Ine ndidzagawa Sekemu

ndipo ndidzayesa chigwa cha Sukoti.

8Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso;

Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera,

Yuda ndi ndodo yanga yaufumu.

9Mowabu ndi mbale yanga yosambiramo

ndidzaponya nsapato zanga pa Edomu;

ndidzafuwula mopambana pa Filisitiya.”

10Ndani adzandifikitsa ku mzinda wotetezedwa?

Ndani adzanditsogolera ku Edomu?

11Kodi sindinu Mulungu, Inu amene mwatikana

ndipo simuperekezanso magulu athu ankhondo?

12Tithandizeni ife kulimbana ndi mdani,

pakuti thandizo la munthu ndi lopanda pake.

13Chifukwa cha Mulungu wathu, ife tidzapeza chipambano,

ndipo adzapondereza pansi adani athu.