Masalimo 105 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 105:1-45

Salimo 105

1Yamikani Yehova, itanani dzina lake;

lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.

2Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo;

fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.

3Munyadire dzina lake loyera;

mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.

4Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;

funafunani nkhope yake nthawi yonse.

5Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita,

zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,

6inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,

inu ana a Yakobo, osankhika ake.

7Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;

maweruzo ake ali pa dziko lonse lapansi.

8Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya,

mawu amene analamula kwa mibado yonse,

9pangano limene Iye anapanga ndi Abrahamu,

lumbiro limene analumbira kwa Isake.

10Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga zophunzitsa,

kwa Israeli monga pangano lamuyaya:

11“Ndidzapereka kwa iwe dziko la Kanaani

ngati gawo la cholowa chako.”

12Pamene iwo anali ngati anthu ochepa mʼchiwerengero,

ochepa ndithu, ndiponso alendo mʼdzikolo,

13ankayendayenda kuchoka ku mtundu wina wa anthu ndi kupita ku mtundu wina,

kuchoka mu ufumu wina kupita ku wina.

14Iye sanalole wina aliyense kuwapondereza;

anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo:

15“Musakhudze odzozedwa anga;

musachitire choyipa aneneri anga.”

16Iye anabweretsa njala pa dziko

ndipo anawononga chakudya chonse;

17Iyeyo anatumiza munthu patsogolo pawo,

Yosefe anagulitsidwa ngati kapolo.

18Iwo anavulaza mapazi ake ndi matangadza,

khosi lake analiyika mʼzitsulo,

19mpaka zimene Iye ananeneratu zitakwaniritsidwa,

mpaka mawu a Yehova ataonetsa kuti Iye ananena zoona.

20Mfumu inatuma munthu kukamumasula,

wolamulira wa mitundu ya anthu anamasula iyeyo.

21Anamuyika kukhala wolamulira nyumba yake,

wolamulira zonse zimene iye anali nazo,

22kulangiza ana a mfumu monga ankafunira

ndi kuphunzitsa nzeru akuluakulu.

23Tsono Israeli analowa mu Igupto;

Yakobo anakhala monga mlendo mʼdziko la Hamu.

24Yehova anachulukitsa anthu ake;

ndipo anachititsa kuti akhale ochuluka kwambiri kuposa adani awo;

25amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake,

kukonzera chiwembu atumiki ake.

26Yehova anatuma Mose mtumiki wake,

ndi Aaroni amene Iye anamusankha.

27Iwo anachita zizindikiro zozizwitsa pakati pawo,

zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.

28Yehova anatumiza mdima nasandutsa dziko kuti likhale la mdima.

Koma anthuwo anakaniratu mawu a Yehova.

29Yehova anasandutsa madzi awo kukhala magazi,

kuchititsa kuti nsomba zawo zife.

30Dziko lawo linadzaza ndi achule

amene analowa mʼzipinda zogona za olamulira awo.

31Iye anayankhula, ndipo kunabwera ntchentche zochuluka

ndi nsabwe mʼdziko lawo lonse.

32Iyeyo anatembenuza mvula yawo kukhala matalala,

ndi zingʼaningʼani mʼdziko lawo lonse;

33Anagwetsa mitengo yawo ya mpesa ndi mitengo yawo ya mkuyu,

nawononganso mitengo ina ya mʼdziko lawolo.

34Iye anayankhula, ndipo dzombe linabwera,

ziwala zosawerengeka;

35zinadya chilichonse chobiriwira cha mʼdziko lawo,

zinadya zonse zotuluka mʼnthaka yawo.

36Kenaka anakantha ana onse oyamba kubadwa a mʼdziko lawo,

zipatso zoyamba za umunthu wawo wonse.

37Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri,

ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.

38Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka,

pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo.

39Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo,

ndi moto owawunikira usiku.

40Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinziri

ndipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba.

41Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka;

ngati mtsinje anayenda mʼchipululu.

42Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limene

linaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake.

43Iye anatulutsa anthu ake akukondwera,

osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;

44Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina

ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,

45kuti iwo asunge malangizo ake

ndi kutsatira malamulo ake.

Tamandani Yehova.