Masalimo 104 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 104:1-35

Salimo 104

1Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.

Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri;

mwavala ulemerero ndi ufumu.

2Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala;

watambasula miyamba ngati tenti

3ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake.

Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake,

ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo.

4Amapanga mphepo kukhala amithenga ake,

malawi amoto kukhala atumiki ake.

5Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake;

silingasunthike.

6Munaliphimba ndi nyanja yozama ngati chovala;

madzi anayimirira pamwamba pa mapiri.

7Koma pakudzudzula kwanu madzi anathawa,

pa mkokomo wa bingu lanu iwo anamwazika;

8Inu munamiza mapiri,

iwo anatsikira ku zigwa

kumalo kumene munawakonzera.

9Inu munayika malire ndipo sangathe kudutsa,

iwo sadzamizanso dziko lapansi.

10Iye achititsa akasupe kutulutsa madzi kupita ku zigwa;

madziwo amayenda pakati pa mapiri.

11Iwo amapereka madzi kwa zirombo zonse zakuthengo;

abulu akuthengo amapha ludzu lawo.

12Mbalame zamlengalenga zimayika zisa mʼmbali mwa madzi;

zimayimba pakati pa thambo.

13Iye amathirira mapiri kuchokera ku zipinda zake zapamwamba;

dziko lapansi limakhutitsidwa ndi chipatso cha ntchito yake.

14Amameretsa udzu kuti ngʼombe zidye,

ndi zomera, kuti munthu azilima

kubweretsa chakudya kuchokera mʼdziko lapansi:

15vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu,

mafuta amene amachititsa nkhope yake kuwala,

ndi buledi amene amapereka mphamvu.

16Mitengo ya Yehova ndi yothiriridwa bwino,

mikungudza ya ku Lebanoni imene Iye anadzala.

17Mbalame zimamanga zisa zawo;

kakowa ali ndi malo ake mʼmikungudzamo.

18Mapiri ataliatali ndi a mbalale;

mʼmingʼalu ya miyala ndi mobisalamo mbira.

19Mwezi umasiyanitsa nyengo

ndipo dzuwa limadziwa nthawi yake yolowera.

20Inu mumabweretsa mdima nukhala usiku,

ndipo zirombo zonse za ku nkhalango zimatuluka.

21Mikango imabangula kufuna nyama,

ndi kufunafuna chakudya chawo kuchokera kwa Mulungu.

22Dzuwa limatuluka ndipo iyo imapita kukabisala;

imabwerera kukagona pansi mʼmapanga awo.

23Pamenepo munthu amapita ku ntchito yake,

kukagwira ntchito yake mpaka madzulo.

24Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova!

Munazipanga zonse mwanzeru,

dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.

25Kuli nyanja yayikulu ndi yotambalala,

yodzaza ndi zolengedwa zosawerengeka,

zamoyo zanu zazikulu ndi zazingʼono zomwe.

26Kumeneko sitima zapamadzi zimayenda uku ndi uku,

ndiponso Leviyatani amene munamulenga kuti asewere kumeneko.

27Zonsezi zimayangʼana kwa Inu

kuti muzipatse chakudya chawo pa nthawi yake yoyenera.

28Mukazipatsa,

zimachisonkhanitsa pamodzi;

mukatsekula dzanja lanu,

izo zimakhutitsidwa ndi zinthu zabwino.

29Mukabisa nkhope yanu,

izo zimachita mantha aakulu;

mukachotsa mpweya wawo,

zimafa ndi kubwerera ku fumbi.

30Mukatumiza mzimu wanu,

izo zimalengedwa

ndipo mumakozanso maonekedwe a dziko lapansi.

31Ulemerero wa Yehova ukhalebe mpaka muyaya;

Yehova akondwere ndi ntchito ya manja ake;

32Iye amene amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera,

amene amakhudza mapiri ndipo amatuluka utsi.

33Ine ndidzayimbira Yehova moyo wanga wonse;

ndidzayimbira matamando Mulungu wanga nthawi yonse imene ndili ndi moyo.

34Zolingalira zanga zikhale zomukomera Iye,

pamene ndikusangalala mwa Yehova.

35Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansi

ndipo anthu oyipa asapezekenso.

Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga.

Tamandani Yehova.