Masalimo 103 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 103:1-22

Salimo 103

Salimo la Davide.

1Tamanda Yehova, iwe moyo wanga;

ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.

2Tamanda Yehova, iwe moyo wanga,

ndipo usayiwale zabwino zake zonse.

3Amene amakhululuka machimo ako onse

ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,

4amene awombola moyo wako ku dzenje

ndi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu,

5amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino,

kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.

6Yehova amachita chilungamo

ndipo amaweruza molungama onse opsinjika.

7Iye anadziwitsa Mose njira zake,

ntchito zake kwa Aisraeli.

8Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima,

wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka.

9Iye sadzatsutsa nthawi zonse,

kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya;

10satichitira molingana ndi machimo athu,

kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu.

11Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi,

koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa;

12monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo,

koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.

13Monga bambo amachitira chifundo ana ake,

choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;

14pakuti Iye amadziwa momwe tinawumbidwira,

amakumbukira kuti ndife fumbi.

15Kunena za munthu, masiku ake ali ngati udzu,

amaphuka ngati duwa la mʼmunda;

16koma mphepo imawombapo ndipo silionekanso

ndipo malo ake sakumbukirikanso.

17Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya

chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa,

ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo;

18iwo amene amasunga pangano lake

ndi kukumbukira kumvera malangizo ake.

19Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba

ndipo ufumu wake umalamulira onse.

20Tamandani Yehova, inu angelo ake,

amphamvu inu amene mumachita zimene amalamula,

amene mumamvera mawu ake.

21Tamandani Yehova, zolengedwa zonse zakumwamba,

inu atumiki ake amene mumachita chifuniro chake.

22Tamandani Yehova, ntchito yake yonse

kulikonse mu ulamuliro wake.

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.