Masalimo 102 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 102:1-28

Salimo 102

Pemphero la munthu wosautsidwa, pamene walefuka, nakhuthulira pamaso pa Yehova kulira kwakeko.

1Yehova imvani pemphero langa;

kulira kwanga kopempha thandizo kufike kwa Inu.

2Musandibisire nkhope yanu

pamene ndili pa msautso.

Munditcherere khutu;

pamene ndiyitana ndiyankheni msanga.

3Pakuti masiku anga akupita ngati utsi;

mafupa anga akunyeka ngati nkhuni zoyaka.

4Mtima wanga wakanthidwa ndipo ukufota ngati udzu;

ndipo ndimayiwala kudya chakudya changa.

5Chifukwa cha kubuwula kwanga kofuwula

ndatsala chikopa ndi mafupa okhaokha.

6Ndili ngati kadzidzi wa ku chipululu,

monga kadzidzi pakati pa mabwinja.

7Ndimagona osapeza tulo; ndakhala

ngati mbalame yokhala yokha pa denga.

8Tsiku lonse adani anga amandichita chipongwe;

iwo amene amandinyoza, amagwiritsa ntchito dzina langa ngati temberero.

9Pakuti ndimadya phulusa ngati chakudya changa

ndi kusakaniza chakumwa changa ndi misozi

10chifukwa cha ukali wanu waukulu,

popeza Inu mwandinyamula ndi kunditayira kumbali.

11Masiku anga ali ngati mthunzi wa kumadzulo;

Ine ndikufota ngati udzu.

12Koma Inu Yehova, muli pa mpando wanu waufumu kwamuyaya;

kudziwika kwanu ndi kokhazikika ku mibado yonse.

13Inu mudzadzuka ndi kuchitira chifundo Ziyoni

pakuti ndi nthawi yoti muonetse kukoma mtima kwanu pa iyeyo;

nthawi yoyikika yafika.

14Pakuti miyala yake ndi yokondedwa kwa atumiki anu;

fumbi lake lokha limawachititsa kuti amve chisoni.

15Mitundu ya anthu idzaopa dzina la Yehova,

mafumu onse a dziko lapansi adzalemekeza ulemerero wanu.

16Pakuti Yehova adzamanganso Ziyoni

ndi kuonekera mu ulemerero wake.

17Iye adzayankha pemphero la anthu otayika;

sadzanyoza kupempha kwawo.

18Zimenezi zilembedwe chifukwa cha mibado ya mʼtsogolo,

kuti anthu amene sanabadwe adzatamande Yehova:

19“Yehova anayangʼana pansi kuchokera ku malo ake opatulika mmwamba,

kuchokera kumwamba anayangʼana dziko lapansi,

20kuti amve kubuwula kwa anthu a mʼndende,

kuti apulumutse amene anayenera kuphedwa.”

21Kotero dzina la Yehova lidzalengezedwa mu Ziyoni

ndi matamando ake mu Yerusalemu,

22pamene mitundu ya anthu ndi maufumu

adzasonkhana kuti alambire Yehova.

23Iye anathyola mphamvu zanga pa nthawi ya moyo wanga;

Iyeyo anafupikitsa masiku anga.

24Choncho Ine ndinati:

“Musandichotse, Inu Mulungu wanga, pakati pa masiku a moyo wanga;

zaka zanu zimakhalabe pa mibado yonse.

25Pachiyambi Inu munakhazikitsa maziko a dziko lapansi

ndipo mayiko akumwamba ndi ntchito ya manja anu.

26Izi zidzatha, koma Inu mudzakhalapo;

zidzatha ngati chovala.

Mudzazisintha ngati chovala

ndipo zidzatayidwa.

27Koma Inu simusintha,

ndipo zaka zanu sizidzatha.

28Ana a atumiki anu adzakhala pamaso panu;

zidzukulu zawo zidzakhazikika pamaso panu.”