Masalimo 100 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 100:1-5

Salimo 100

Salimo. Nyimbo yothokoza.

1Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi.

2Mulambireni Yehova mosangalala;

bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero.

3Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.

Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake;

ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.

4Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko

ndi ku mabwalo ake ndi matamando;

muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.

5Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya;

kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.