Marko 8 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Marko 8:1-38

Yesu Adyetsa Anthu 4,000

1Mʼmasiku amenewo gulu lina lalikulu la anthu linasonkhana. Popeza iwo analibe chakudya, Yesu anayitana ophunzira ake nati kwa iwo, 2“Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala ali ndi Ine masiku atatuwa ndipo alibe chakudya. 3Ngati nditawawuza kuti apite kwawo ali ndi njala, iwo adzakomoka mʼnjira chifukwa ena a iwo achokera kutali.”

4Ophunzira ake anayankha nati, “Kodi ndi kuti kuthengo kuno kumene munthu angapeze buledi okwanira kuwadyetsa?”

5Yesu anafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati?”

Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.”

6Iye anawuza gulu la anthu kuti likhale pansi. Atatenga malofu a buledi asanu ndi awiri, anayamika, nawanyema ndipo anapatsa ophunzira ake kuti agawire anthu, ndipo iwo anatero. 7Analinso ndi tinsomba tochepa; Iye anayamikanso chifukwa cha nsombazo. Ndipo anawuza ophunzira kuti awagawire. 8Anthu anadya ndipo anakhuta. Atamaliza, ophunzira anatola buledi ndi nsomba zotsalira ndi kudzaza madengu asanu ndi awiri. 9Panali amuna pafupifupi 4,000. Ndipo atawawuza kuti apite kwawo, 10analowa mʼbwato pamodzi ndi ophunzira ake napita ku dera la Dalamanuta.

11Afarisi anabwera nayamba kumufunsa Yesu. Pomuyesa Iye, anamufunsa za chizindikiro chochokera kumwamba. 12Ndipo anatsitsa moyo nati, “Nʼchifukwa chiyani mʼbado uno ukufuna chizindikiro chodabwitsa? Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe chizindikiro chidzapatsidwa kwa iwo.” 13Ndipo anawasiya, nalowanso mʼbwato ndi kuwolokera tsidya lina.

Yisiti wa Afarisi ndi Herode

14Ophunzira anayiwala kutenga buledi, kupatula buledi mmodzi yekha amene anali naye mʼbwato. 15Yesu anawachenjeza kuti, “Samalani ndipo onetsetsani yisiti wa Afarisi ndi wa Herode.”

16Iwo anakambirana wina ndi mnzake ndipo anati, “Ndi chifukwa choti tilibe buledi.”

17Yesu atadziwa zokambirana zawo anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukukambirana kuti mulibe buledi? Kodi inu simukuonabe kapena kuzindikira? Kodi mitima yanu ndi yowumitsidwa? 18Kodi muli ndi maso ndipo simukuona, ndi makutu ndipo mukulephera kumva? Kodi simukukumbukira? 19Pamene ndinagawa malofu asanu a buledi kwa anthu 5,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”

Iwo anayankha kuti, “Khumi ndi awiri.”

20“Ndipo pamene ndinagawa malofu asanu ndi awiri a buledi, kwa anthu 4,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”

Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.”

21Iye anawafunsa kuti, “Kodi simumvetsetsabe?”

Kuchiritsidwa kwa Munthu Wosaona ku Betisaida

22Iwo anafika ku Betisaida, ndipo anthu ena anabweretsa munthu wosaona ndipo anamupempha Yesu kuti amukhudze. 23Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo napita naye kunja kwa mudzi. Atalavulira mʼmaso a munthuyo ndi kumusanjika manja, Yesu anafunsa kuti, “Kodi ukuona kalikonse?”

24Iye anakweza maso nati, “Ndikuona anthu; akuoneka ngati mitengo imene ikuyendayenda.”

25Kenakanso Yesu anayika manja ake mʼmaso a munthuyo. Ndipo maso ake anatsekuka, naonanso, ndipo anaona zonse bwinobwino. 26Yesu anamuwuza kuti apite kwawo nati, “Usapite mʼmudzimo.”

Petro Avomereza Khristu

27Yesu ndi ophunzira ake anapita ku midzi yozungulira Kaisareya wa Filipo. Ali panjira, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati ndine yani?”

28Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneri.”

29Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu, mumati ndine yani?”

Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu.”

30Yesu anawachenjeza kuti asawuze wina aliyense za Iye.

Yesu Aneneratu za Imfa Yake

31Iye anayamba kuwaphunzitsa kuti, “Mwana wa Munthu ayenera kumva zowawa zambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe, ndi aphunzitsi a malamulo, ndi kuti ayenera kuphedwa ndipo patatha masiku atatu adzaukanso.” 32Izi anaziyankhula momveka bwino, ndipo Petro anamutengera pambali ndipo anayamba kumudzudzula.

33Koma Yesu atatembenuka ndi kuyangʼana ophunzira ake, anamudzudzula Petro nati, “Choka pamaso panga Satana! Suganizira zinthu za Mulungu koma za anthu.”

Njira ya Mtanda

34Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata. 35Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa. 36Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? 37Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake? 38Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

馬可福音 8:1-38

耶穌使四千人吃飽

1那時,又有一大群人聚在一起,他們沒有東西吃。耶穌就叫來門徒,說: 2「我憐憫這些人,他們跟我在一起已經三天,沒有任何吃的了。 3如果讓他們餓著肚子回家,他們在路上會體力不支,因為有些人是遠道而來的。」

4門徒說:「在這荒野,如何找到足夠的食物給這些人吃呢?」

5耶穌問:「你們有多少餅?」

門徒答道:「七個。」

6耶穌便吩咐大家坐在地上,然後拿著那七個餅祝謝了,掰開,遞給門徒,讓門徒分給大家,門徒就把餅分給大家。 7他們還有幾條小魚。耶穌祝謝了,叫門徒分給眾人。 8大家都吃了,並且吃飽了,剩下的零碎裝滿了七個筐子。 9吃的人約有四千。耶穌讓眾人回家後, 10隨即和門徒上船,來到大瑪努他地區。

11法利賽人出來盤問耶穌,要求祂從天上顯一個神蹟給他們看看,藉此試探祂。 12耶穌深深歎息道:「這世代的人為什麼總是要看神蹟呢?我實在告訴你們,沒有神蹟給這世代的人看。」 13然後,耶穌離開他們,乘船回對岸去了。

防備法利賽人和希律的酵

14門徒忘了帶餅,船上只有一個餅。 15耶穌警告他們:「你們要謹慎,要提防法利賽人和希律的酵!」

16他們彼此議論說:「老師這樣說,是不是因為我們沒有帶餅呢?」

17耶穌知道他們的心思,就說:「你們為什麼議論沒有帶餅的事呢?難道你們還不明白、不領悟嗎?你們的心還是愚頑嗎? 18你們有眼不會看,有耳不會聽嗎?你們不記得嗎? 19我掰開五個餅分給五千人吃的時候,你們撿了多少籃的零碎呢?」

門徒答道:「十二籃。」

20耶穌又說:「我用七個餅餵飽四千人的時候,你們撿了多少筐零碎呢?」

門徒答道:「七筐。」

21耶穌接著說:「你們還不明白嗎?」

治好伯賽大的瞎子

22他們到了伯賽大,有人帶來一個瞎子,求耶穌摸他。 23耶穌拉著瞎子的手帶他走到村外,吐唾沫在他的眼睛上,並把手按在他身上,問他:「你看見什麼了?」

24他抬頭看了看,說:「我看見人們好像一棵棵的樹,走來走去。」

25耶穌把手按在他的眼睛上,他定睛一看,便恢復了視力,什麼都看得清清楚楚。 26耶穌叫他回家,並對他說:「不要再進這個村子了。」

彼得宣告耶穌是基督

27耶穌和門徒前往凱撒利亞·腓立比境內的村莊。在路上,祂問門徒:「別人說我是誰?」

28他們說:「有人說你是施洗者約翰,有人說你是以利亞,有人說你是眾先知中的一位。」

29耶穌又問他們:「那麼,你們說我是誰?」

彼得回答說:「你是基督!」

30耶穌吩咐他們不要洩露祂的身分。

耶穌預言自己的受難和復活

31從此,耶穌便告訴他們,人子必須受許多苦,被長老、祭司長和律法教師棄絕,殺害,但必在三天之後復活。 32耶穌清楚地把這些事告訴了他們,彼得就把祂拉到一邊,勸阻祂。 33耶穌轉身看了看門徒,斥責彼得說:「撒旦,退到我後面去!因為你不考慮上帝的意思,只考慮人的意思。」

34祂叫眾人和門徒一起過來,對他們說:「如果有人要跟從我,就應當捨己,背起他的十字架跟從我。 35因為想救自己生命的,必失去生命;但為了我和福音而失去生命的,必得到生命。 36人就是賺得全世界,卻喪失自己的生命,又有什麼益處呢? 37他還能用什麼換回生命呢?

38「在這淫亂、罪惡的世代,如果有人以我和我的道為恥,人子在父的榮耀中與聖天使再來的時候,也要以他為恥。」