Marko 7 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Marko 7:1-37

Miyambo ya Makolo ya Ayuda

1Afarisi ndi ena mwa aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anasonkhana momuzungulira Yesu ndipo 2iwo anaona ophunzira ake akudya chakudya ndi mʼmanja mwakuda kapena kuti mʼmanja mosasamba. 3(Afarisi ndi Ayuda onse sadya pokhapokha atasamba mʼmanja, kusunga mwambo wa makolo awo. 4Akabwera kuchokera ku msika samadya pokhapokha atasamba. Ndipo amasunga miyambo ina yambiri monga, kutsuka zikho, mitsuko ndi maketulo).

5Choncho Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anafunsa Yesu kuti, “Nʼchifukwa chiyani ophunzira anu satsatira mwambo wa makolo, mʼmalo mwake amangodya chakudya ndi mʼmanja mwakuda?”

6Iye anayankha kuti, “Yesaya ananena zoona pamene ananenera za inu achiphamaso; monga kunalembedwa kuti:

“Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo,

koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.

7Amandilambira Ine kwachabe;

ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.

8Mwasiya malamulo a Mulungu ndipo mwagwiritsitsa miyambo ya anthu.”

9Ndipo anawawuzanso kuti, “Inu muli ndi njira yabwino yokankhira kumbali malamulo a Mulungu kuti mukatsatire miyambo yanuyo! 10Pakuti Mose anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako,’ ndipo, ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’ 11Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukanayenera kulandira kuchokera kwa ine ndi Korobani’ (kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa kwa Mulungu), 12pamenepo inu simumalola kuti achitire kanthu kalikonse abambo kapena amayi ake. 13Potero mumachepetsa mawu a Mulungu kukhala wopanda mphamvu ndi miyambo yanu imene mumapatsirana. Ndipo mumachita zinthu zina zambiri monga zimenezi.”

14Yesu anayitananso gulu la anthu ndipo anati, “Tandimverani nonsenu, ndipo zindikirani izi. 15Palibe kanthu kunja kwa munthu kamene kakalowa mwa iye kangamusandutse wodetsedwa. Koma zimene zituluka mwa munthu ndizo zimupanga kukhala wodetsedwa.” 16(Ngati wina ali ndi makutu akumva amve).

17Atalisiya gulu la anthu ndi kulowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa za fanizoli 18Iye anawafunsa kuti, “Kodi nanunso simumvetsetsa? Kodi simukuona kuti palibe kanthu kamene kakalowa mwa munthu kochokera kunja kakhoza kumudetsa? 19Pakuti sikalowa mu mtima wake koma mʼmimba mwake, ndipo kenaka kamatuluka kunja.” (Ndi mawu amenewa, Yesu anayeretsa zakudya zonse).

20Anapitiriza kuti, “Chimene chichokera mwa munthu ndi chomwe chimamudetsa. 21Pakuti kuchokera mʼkati mwa mitima ya anthu, mumatuluka maganizo oyipa, chiwerewere, kuba, kupha, chigololo, 22dyera, nkhwidzi, chinyengo, machitidwe onyansa, kaduka, chipongwe, kudzikuza ndi kupusa. 23Zoyipa zonsezi zimatuluka mʼkati ndipo zimadetsa munthu.”

Chikhulupiriro cha Mayi wa ku Siriya Fonisia

24Yesu anachoka kumalo amenewo napita ku madera a Turo. Iye analowa mʼnyumba ndipo sanafune wina kuti adziwe zimenezi; komabe sanathe kudzibisa. 25Kunena zoona, amayi amene kamwana kawo kakakazi kanali kogwidwa ndi mzimu woyipa, atangomva za Iye, anabwera nagwada pa mapazi ake. 26Mayiyu anali Mhelene, wobadwira ku Fonisia wa ku Siriya. Anamupempha Yesu kuti atulutse chiwanda mwa mwana wake.

27Iye anamuwuza kuti, “Choyamba asiye ana adye zimene akuzifuna, pakuti si kwabwino kutenga buledi wa ana ndi kuponyera agalu awo.”

28Mayiyo anayankha kuti, “Inde Ambuye, koma ngakhale agalu amadya zomwe zimagwa pansi kuchokera pa tebulo la ana.”

29Ndipo Iye anamuwuza kuti, “Chifukwa cha yankholi, ukhoza kupita; chiwanda chachoka mwa mwana wako wamkazi.”

30Atapita kwawo anakapeza mwana wake aligone pa bedi, chiwanda chitatuluka.

Kuchiritsidwa kwa Munthu Wosamva ndi Wosayankhula

31Ndipo Yesu anachoka ku dera la Turo nadutsa pakati pa Sidoni, kutsikira ku nyanja ya Galileya kupita ku dera la Dekapoli. 32Kumeneko anthu ena anabweretsa kwa Iye munthu amene anali wosamva ndi wosayankhula, ndipo anamupempha kuti asanjike dzanja pa iye.

33Atamutengera iye pambali, patali ndi gulu la anthu, Yesu analowetsa zala zake mʼmakutu a munthuyo. Kenaka anapaka malovu pachala ndi kukhudza lilime la munthuyo. 34Iye anayangʼana kumwamba ndipo ndi mawu otsitsa moyo, anati kwa iye, “Efataa!” (Kutanthauza kuti, “Tsekuka!”) 35Atachita izi, makutu a munthuyo anatsekuka komanso lilime lake linamasuka ndipo anayamba kuyankhula momveka bwino.

36Yesu anawalamula kuti asawuze wina aliyense. Koma pamene anapitiriza kuwaletsa, iwo anapitiriza kuyankhula za izi. 37Anthu anadabwa kwambiri. Iwo anati, “Wachita zonse bwino, ngakhale Iyenso atsekula makutu a osamva ndi osayankhula kuti ayankhule.”