Marko 3 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Marko 3:1-35

Yesu Achiritsa Wolumala Dzanja

1Nthawi inanso analowa mʼsunagoge, ndipo munthu wa dzanja lolumala anali momwemo. 2Ena a iwo anafunafuna chifukwa chakuti akamuneneze Yesu, potero anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angamuchiritse tsiku la Sabata. 3Yesu anati kwa munthu wolumala dzanjayo, “Imirira, bwera kuno kutsogolo.”

4Ndipo Yesu anawafunsa kuti, “Kodi chololedwa ndi chiyani pa tsiku la Sabata: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kupha?” Koma iwo anakhala chete.

5Yesu anawayangʼana ndi mkwiyo ndipo powawidwa mtima chifukwa cha mitima yawo yowuma anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola, ndipo dzanja lake linachira. 6Kenaka Afarisi anatuluka nayamba kukonza chiwembu ndi Aherode mmene angamuphere Yesu.

Magulu a Anthu Amutsata Yesu

7Yesu anachoka pamodzi ndi ophunzira ake napita ku nyanja, ndipo gulu lalikulu la anthu lochokera ku Galileya linamutsata. 8Atamva zonse zimene amachita, anthu ambiri anabwera kwa Iye kuchokera ku Yudeya, Yerusalemu, Idumeya ndi madera a ku tsidya kwa mtsinje wa Yorodani ndi ozungulira Turo ndi Sidoni. 9Chifukwa cha gulu la anthu, anawuza ophunzira ake kuti apezeretu bwato likhale, kuti anthu angamupanikize. 10Pakuti anachiritsa ambiri, kotero kuti iwo amene anali ndi matenda amakankhana kutsogolo kuti amukhudze. 11Nthawi iliyonse mizimu yoyipa ikamuona, imagwa pansi pamaso pake ndi kufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” 12Koma anayichenjeza mwamphamvu kuti isanene kuti Iye anali ndani.

Yesu Asankha Ophunzira Khumi ndi Awiri

13Yesu anakwera ku phiri ndipo anayitana amene anawafuna, ndipo anabwera kwa Iye. 14Iye anasankha khumi ndi awiri, nawayika akhale atumwi; pokhala ndi Iye aziwatuma kukalalikira 15ndi kuti akhale ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda. 16Awa ndi khumi ndi awiri amene anawasankha: Simoni (amene anapatsidwa dzina lakuti Petro); 17Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi mʼbale wake Yohane (iwowa anawapatsa dzina lakuti Bowanege, ndiye kuti ana a bingu); 18Andreya, Filipo, Bartumeyu, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Tadeyo, Simoni Zelote, 19ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye.

Yesu ndi Belezebabu

20Pambuyo pake Yesu analowa mʼnyumba, ndipo gulu la anthu linasonkhananso, kotero kuti Iye pamodzi ndi ophunzira ake sanapeze mpata kuti adye. 21Anthu a ku banja lake atamva zimenezi, anapita kuti akamutenga, pakuti ankanena kuti, “Wazungulira mutu.”

22Ndipo aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anati, “Iye wagwidwa ndi Belezebabu! Ndi ulamuliro wa mkulu wa ziwanda akutulutsa ziwanda.”

23Pamenepo Yesu anawayitana nawayankhula mʼmafanizo nati: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? 24Ngati ufumu ugawanikana mwa iwo okha, ufumu umenewo sungakhalitse. 25Ngati nyumba igawanikana mwa iyo yokha, nyumba imeneyo singathe kuyima. 26Ndipo ngati Satana adzitsutsa yekha sangathe kuyima; ulamuliro wake watha. 27Kunena zoona, palibe munthu angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kutenga katundu wake pokhapokha atayamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Pamenepo akhoza kumubera. 28Ndikukuwuzani zoona kuti machimo onse ndi zamwano zonse za anthu zidzakhululukidwa, 29koma aliyense amene achitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa pakuti wachita tchimo losatha.”

30Ananena izi chifukwa anati, “Ali ndi mzimu woyipa.”

Amayi ndi Abale ake a Yesu

31Pamenepo amayi ndi abale ake a Yesu anafika. Atayima kunja, anatuma wina kuti akamuyitane Iye. 32Gulu la anthu linakhala momuzungulira Iye, ndipo anamuwuza kuti, “Amayi ndi abale anu ali panja akukufunani.”

33Iye anafunsa kuti, “Amayi ndi abale anga ndi ndani?”

34Pamenepo anayangʼana anthu amene anakhala momuzungurira ndipo anati, “Awa ndi amayi anga ndi abale anga! 35Aliyense amene achita chifuniro cha Mulungu ndi mʼbale wanga ndi mlongo wanga ndi amayi anga.”