Marko 11 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Marko 11:1-33

Yesu Alowa mu Yerusalemu Mwaulemerero

1Atayandikira ku Yerusalemu, anafika ku Betifage ndi Betaniya ku phiri la Olivi. Yesu anatuma awiri a ophunzira ake 2nati kwa iwo, “Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukamakalowa, mukapeza mwana wabulu atamangiriridwa pamenepo, amene wina aliyense sanakwerepo. Kamumasuleni ndi kubwera naye kuno. 3Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, ‘Mukuchita zimenezi chifukwa chiyani?’ Kamuwuzeni kuti, ‘Ambuye akumufuna ndipo akamutumiza kuno msanga.’ ”

4Anapita ndipo anakapeza mwana wabulu ali kunja mu msewu waukulu atamumangirira pa chipata. Pamene anamumasula, 5anthu ena amene anayima pomwepo anafunsa kuti, “Mukuchita chiyani, kumasula mwana wabuluyo?” 6Iwo anayankha monga mmene Yesu anawawuzira, ndipo anthu aja anawalola kuti apite. 7Atafika naye mwana wabulu kwa Yesu, nayika mikanjo yawo pa buluyo, Iye anakwerapo. 8Anthu ambiri anayala mikanjo yawo pa msewu, pamene ena anayala nthambi zomwe anadula mʼminda. 9Amene anatsogola ndi iwo amene ankatsatira ankafuwula kuti,

“Hosana!

“Odala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye!”

10“Odala ndi ufumu umene ukubwera wa abambo athu Davide!”

“Hosana Mmwambamwamba!”

11Yesu analowa mu Yerusalemu napita ku Nyumba ya Mulungu. Anayangʼana zonse, koma popeza kuti nthawi inali itapita, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.

Yesu Atemberera Mkuyu

12Mmawa mwake pamene amachoka ku Betaniya, Yesu anamva njala. 13Ataonera patali mtengo wamkuyu uli ndi masamba, anapita kuti akaone ngati unali ndi chipatso chilichonse. Atafika, sanapezemo kanthu koma masamba, chifukwa sinali nthawi ya nkhuyu. 14Ndipo Iye anati kwa mtengo, “Palibe amene adzadyenso chipatso kuchokera kwa iwe.” Ndipo ophunzira ake anamva Iye akunena izi.

Yesu Ayeretsa Nyumba ya Mulungu

15Atafika ku Yerusalemu, Yesu analowa mʼbwalo lakunja la Nyumba ya Mulungu ndipo anayamba kupirikitsa anthu amene amagula ndi kugulitsa mʼmenemo. Anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda, 16ndipo Iye sanalole aliyense kugulitsa malonda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu. 17Ndipo pamene ankawaphunzitsa, Iye anati, “Kodi sikunalembedwe kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero kwa anthu a mitundu yonse?’ Koma inu mwayisandutsa ‘phanga la achifwamba.’ ”

18Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamva izi ndipo anayamba kufuna njira yoti amuphere Iye, pakuti amamuopa, chifukwa gulu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.

19Pofika madzulo, iwo anatuluka mu mzindamo.

Mkuyu Wofota

20Mmamawa, pamene ankayenda, anaona mtengo wamkuyu uja utafota kuyambira ku mizu. 21Petro anakumbukira nati kwa Yesu, “Aphunzitsi, taonani! Mtengo wamkuyu munawutemberera uja wafota!”

22Yesu anayankha kuti, “Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. 23Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo. 24Nʼchifukwa chake ndikukuwuzani kuti chilichonse chimene mupempha mʼpemphero, khulupirirani kuti mwalandira, ndipo chidzakhala chanu. 25Pamene muyimirira kupemphera, ngati muli ndi chifukwa ndi wina, mukhululukireni, kuti Atate anu akumwamba akukhululukireni machimo anu.” 26(Koma ngati simukhululukirana, ngakhale Atate anu akumwamba sadzakhululukira machimo anu).

Amufunsa Yesu za Ulamuliro Wake

27Iwo anafikanso ku Yerusalemu, ndipo pamene Yesu amayenda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anabwera kwa Iye. 28Iwo anafunsa kuti, “Mukuchita izi ndi ulamuliro wanji? Ndipo anakupatsani ulamuliro umenewu ndi ndani?”

29Yesu anayankha kuti, “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo ndikuwuzani ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira izi. 30Ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena kwa anthu? Ndiwuzeni.”

31Iwo anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Wochokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’ 32Koma ife tikati, ‘Wochokera kwa anthu.’ ” (Amaopa anthu, pakuti aliyense amakhulupirira kuti Yohane analidi mneneri).

33Ndipo anamuyankha Yesu kuti, “Sitikudziwa.”

Yesu anati, “Nanenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji ndichitira zimenezi.”