Marko 1 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Marko 1:1-45

Yohane Mʼbatizi Akonza Njira

1Chiyambi cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, 2monga zalembedwera mʼbuku la mneneri Yesaya:

“Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu,

amene adzakonza njira yanu,”

3“Mawu a wofuwula mʼchipululu,

‘Konzani njira ya Ambuye,

wongolani njira zake.’ ”

4Ndipo Yohane anabwera mʼmadera a mʼchipululu nabatiza, ndi kulalikira za ubatizo wa kutembenuka mtima ndi wa chikhululukiro cha machimo. 5Madera onse a ku Yudeya ndi anthu onse a ku Yerusalemu anatuluka napita kwa iye. Akavomereza machimo awo, amawabatiza mu mtsinje wa Yorodani. 6Yohane amavala zovala zopangidwa ndi ubweya wangamira, ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake, ndipo amadya dzombe ndi uchi wamthengo. 7Ndipo uthenga wake unali uwu: “Pambuyo panga pakubwera wina wondiposa ine mphamvu. Ine si woyenera kuwerama ndi kumasula zingwe za nsapato zake. 8Ine ndikubatizani ndi madzi, koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.”

Kubatizidwa ndi Kuyesedwa kwa Yesu

9Pa nthawi imeneyo Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu mtsinje wa Yorodani. 10Pamene Yesu ankatuluka mʼmadzi, anaona kumwamba kukutsekuka ndipo Mzimu Woyera akutsikira pa Iye ngati nkhunda. 11Ndipo Mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndipo ndikondwera nawe.”

12Nthawi yomweyo Mzimu Woyera anamutumiza Iye ku chipululu, 13ndipo anali mʼchipululumo masiku makumi anayi, akuyesedwa ndi Satana. Anali pakati pa nyama zakuthengo; ndipo angelo anamutumikira.

Yesu Alengeza za Uthenga Wabwino

14Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati, 15“Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”

Yesu Ayitana Ophunzira ake Oyamba

16Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja, popeza anali asodzi. 17Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 18Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.

19Atapita patsogolo pangʼono, anaona Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo, ali mʼbwato akukonza makoka awo. 20Mosataya nthawi anawayitana, ndipo anasiya abambo awo Zebedayo ndi anyamata aganyu ali mʼbwatomo, namutsata Iye.

Yesu Atulutsa Mzimu Woyipa

21Iwo anapita ku Kaperenawo, ndipo tsiku la Sabata litafika, Yesu analowa mʼsunagoge nayamba kuphunzitsa. 22Anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, chifukwa anawaphunzitsa ngati munthu amene anali ndi ulamuliro, osati ngati aphunzitsi amalamulo. 23Pomwepo munthu wina mʼsunagogemo amene anali wogwidwa ndi mzimu woyipa anafuwula kuti, 24“Mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”

25Yesu anadzudzula chiwandacho mwamphamvu nati, “Khala chete! Tuluka mwa iye!” 26Mzimu woyipawo unamugwedeza mwamphamvu ndipo unatuluka mwa iye ukufuwula.

27Anthu anadabwa kwambiri kotero kuti anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Ichi nʼchiyani? Chiphunzitso chatsopano ndi ulamuliro! Iye akulamula, ngakhale mizimu yoyipa ikumumvera.” 28Mbiri yake inafalikira kudera lonse la Galileya mofulumira.

Yesu Achiritsa Anthu Ambiri

29Atangochoka mu sunagoge, Yesu pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane anakalowa mʼnyumba ya Simoni ndi Andreya. 30Mpongozi wa Simoni anali chigonere akudwala malungo, ndipo anamuwuza Yesu za iye. 31Ndipo Yesu anapita kwa iye, namugwira dzanja namuthandiza kudzuka. Malungo anachoka ndipo anayamba kuwatumikira.

32Madzulo omwewo dzuwa litalowa anthu anabweretsa kwa Yesu anthu onse odwala ndi ogwidwa ndi ziwanda. 33Anthu onse a mʼmudzimo anasonkhana pa khomo, 34Yesu anachiritsa ambiri amene anali ndi matenda osiyanasiyana, komanso anatulutsa ziwanda zambiri, ndipo sanalole kuti ziwandazo ziyankhule chifukwa zinkamudziwa Iye.

Yesu Apemphera Kumalo a Yekha

35Mmamawa, kukanali kamdima, Yesu anadzuka, nachoka pa nyumbapo kupita kumalo kwa yekha, kumene anakapemphera. 36Simoni ndi anzake anapita kokamufunafuna Iye, 37ndipo atamupeza, anamuwuza kuti, “Aliyense akukufunani!”

38Yesu anayakha kuti, “Tiyeni tipite kwina ku midzi ya pafupi kuti ndikalalikirenso kumeneko. Ichi ndi chifukwa chimene ndinabwerera.” 39Potero anayendayenda mu Galileya, kulalikira mʼmasunagoge awo ndi kutulutsa ziwanda.

Yesu Achiritsa Wakhate

40Munthu wakhate anabwera kwa Iye, nagwada, namupempha kuti, “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”

41Yesu pomva naye chifundo, anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!” 42Nthawi yomweyo khate linachoka ndipo anachiritsidwa.

43Nthawi yomweyo Yesu anamuwuza kuti apite koma anamuchenjeza kuti, 44“Wonetsetsa kuti usawuze aliyense za zimenezi. Koma pita, kadzionetse wekha kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose analamulira zotsimikizira kuyeretsedwa kwanu, ngati umboni kwa iwo.” 45Mʼmalo mwake anapita nayamba kuyankhula momasuka, nafalitsa mbiriyo. Zotsatira zake, Yesu sanathe kulowa mʼmudzi moonekera, koma anakhala kunja kumalo kopanda anthu. Komabe anthu amabwera kwa Iye kuchokera kulikonse.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

马可福音 1:1-45

施洗者约翰预备道路

1有关上帝的儿子耶稣基督的福音是这样开始的。

2以赛亚先知书上说:

“看啊,

我要差遣我的使者在你前面为你预备道路。

3他在旷野大声呼喊,

‘预备主的道,

修直祂的路。’”

4果然,约翰出现了,他在旷野劝人悔改,接受洗礼,使罪得到赦免。 5犹太全境和耶路撒冷的居民都到约翰面前承认他们的罪,在约旦河里接受他的洗礼。

6约翰身穿骆驼毛的衣服,腰束皮带,吃的是蝗虫和野蜜。 7他传道说:“在我之后,有一位能力比我更大的要来,我连弯腰替祂解鞋带也不配。 8我是用水给你们施洗,但祂要用圣灵给你们施洗。”

耶稣受洗

9那时,耶稣从加利利拿撒勒约旦河接受约翰的洗礼。 10耶稣从水中一上来,就看见天开了,圣灵好像鸽子一样降在祂身上, 11从天上有声音说:“你是我的爱子,我甚喜悦你。”

耶稣受试探

12圣灵随即催促祂到旷野。 13祂在旷野受撒旦的试探四十天。祂与野兽在一起,有天使服侍祂。

呼召四渔夫

14约翰被捕后,耶稣来到加利利宣讲上帝的福音,说: 15“时候到了,上帝的国临近了,你们要悔改,相信福音。”

16耶稣沿着加利利湖边走,看见两个渔夫——西门和他的弟弟安得烈正在湖上撒网捕鱼。 17耶稣对他们说:“来跟从我!我要使你们成为得人的渔夫。” 18他们立刻抛下渔网,跟从了耶稣。

19耶稣往前走了不远,又看见西庇太的两个儿子雅各约翰正在船上补网, 20便立刻呼召他们。他们就辞别父亲和船上的工人,跟从了耶稣。

传道赶鬼

21他们到了迦百农,耶稣在安息日去会堂里讲道。 22那里的人都很吃惊,因为祂教导他们时像个有权柄的人,不像律法教师。 23当时会堂里有一个被污鬼附身的人喊道: 24拿撒勒的耶稣啊,我们和你有什么关系?你是来毁灭我们吗?我知道你是谁,你是上帝的圣者!”

25耶稣责备它说:“住口,从他身上出来!”

26污鬼使那人抽搐了一阵,大叫一声,就出来了。 27在场的人十分惊讶,彼此议论说:“这是怎么回事?真是充满权柄的新教导啊!竟然连污鬼都服从祂的命令。” 28于是,耶稣的名声立刻传遍了整个加利利

医病赶鬼

29耶稣同雅各约翰离开会堂,来到西门安得烈家。 30当时西门的岳母正发烧,躺在床上,他们立刻把这事告诉耶稣。 31耶稣走到她的床边,拉着她的手扶她起来,她的烧立刻退了,便起来服侍他们。

32日落之后,有人把病人和被鬼附身的人都带来见耶稣。 33全城的人都聚在门前。 34耶稣医好了许多患各种疾病的人,又赶出很多鬼。祂不准鬼说话,因为鬼认识祂。

在加利利传道

35第二天清早,天还没亮,耶稣就起来独自走到旷野去祷告。 36西门和同伴们四处寻找耶稣, 37找到了,便对祂说:“大家都在找你呢!”

38耶稣却回答说:“我们到附近的乡镇去吧,我也好在那里传道,因为我就是为这事来的。”

39于是,耶稣走遍加利利,在各会堂传道,赶鬼。

治好麻风病人

40有一次,一个患麻风病的人来到耶稣面前,跪下央求:“只要你肯,一定能使我洁净。”

41耶稣动了慈心,就伸手摸他,说:“我肯,你洁净了吧!” 42那人的麻风病立即消失了,他就洁净了。 43耶稣让他回去并郑重地叮嘱: 44“不要把这事告诉别人,要去让祭司察看你的身体,并照摩西的规定献祭,向众人证明你已经洁净了。”

45但那人离开之后,却到处传扬这件事,以致耶稣无法再公开进城。祂只能待在城外的旷野,可是人们仍从各处来找祂。