Maliro 5 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Maliro 5:1-22

1Inu Yehova, kumbukirani zimene zinatichitikira;

yangʼanani ndipo muone kunyozeka kwathu.

2Apereka cholowa chathu kwa obwera,

nyumba zathu kwa alendo.

3Takhala amasiye ndi wopanda abambo,

amayi athu ali ngati akazi amasiye.

4Tiyenera kugula madzi amene timamwa,

nkhuni zathunso nʼzogula.

5Otilondola atigwira pakhosi;

tafowoka ndipo sakutilola kupumula.

6Tinadzipereka kwa Aigupto ndi kwa Asiriya

kuti tipeze chakudya.

7Makolo athu anachimwa ndipo anafa kale,

koma chilango chawo chili pa ife.

8Akapolo akutilamulira,

ndipo palibe ndi mmodzi yemwe angatimasule mʼdzanja lawo.

9Timapeza chakudya chathu poyika miyoyo yathu pa chiswe

chifukwa cha lupanga mʼchipululu.

10Khungu lathu latentha ngati uvuni mʼngʼanjo,

chifukwa cha kuwawa kwa njala.

11Amayi agwiriridwa mu Ziyoni,

ndi anamwali mʼmizinda ya Yuda.

12Akalonga athu akuwapachika pomangirira manja awo,

akuluakulu sakuwalemekeza.

13Achinyamata akukakamizidwa kupera tirigu;

anyamata akudzandira ndi mitolo ya nkhuni.

14Akuluakulu anachokapo pa chipata cha mzinda;

achinyamata aleka nyimbo zawo.

15Chimwemwe chachoka mʼmitima yathu;

kuvina kwathu kwasanduka maliro.

16Chipewa chathu chaufumu chagwa pamutu pathu.

Tsoka kwa ife, chifukwa tachimwa!

17Mitima yathu yakomoka chifukwa cha zimenezi,

chifukwa cha zinthu zimenezi maso athu sakuona bwino,

18pakuti phiri la Ziyoni, limene lasanduka bwinja,

nkhandwe zikungoyendayendapo.

19Inu Yehova, lamulirani kwamuyaya;

mpando wanu waufumu udzakhalabe ku mibadomibado.

20Chifukwa chiyani mumatiyiwala nthawi zonse?

Chifukwa chiyani mwatitaya nthawi yayitali chotere?

21Yehova mutitembenuzire kwa Inu, kuti tibwerere;

mukonzenso masiku athu akhale monga akale,

22pokhapokha ngati mwatitaya kotheratu,

ndi kuti mwatikwiyira kobzola muyeso.