Maliro 4 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Maliro 4:1-22

1Haa! Golide wathimbirira,

golide wosalala wasinthikiratu!

Amwazamwaza miyala yokongola ya kumalo opatulika

pamphambano ponse pa mzinda.

2Haa! Ana a Ziyoni amtengowapatali

amene kale anali ngati golide,

tsopano ali ngati miphika ya dothi,

ntchito ya owumba mbiya!

3Ngakhale nkhandwe zimapereka bere

kuyamwitsa ana ake,

koma anthu anga asanduka ankhanza

ngati nthiwatiwa mʼchipululu.

4Lilime la mwana lakangamira kukhosi

chifukwa cha ludzu,

ana akupempha chakudya,

koma palibe amene akuwapatsa.

5Iwo amene kale ankadya zonona

akupemphetsa mʼmisewu ya mu mzinda.

Iwo amene kale ankavala zokongola

tsopano akugona pa phulusa.

6Kuyipa kwa anthu anga kunali kwakukulu

kuposa anthu a ku Sodomu,

amene anawonongedwa mʼkamphindi kochepa

popanda owathandiza.

7Akalonga ake anali owala koposa chisanu chowundana

ndi oyera kuposa mkaka.

Matupi awo anali ofiira kuposa miyala ya rubi,

maonekedwe awo ngati miyala ya safiro.

8Koma tsopano maonekedwe awo ndi akuda kuposa mwaye;

palibe angawazindikire mʼmisewu ya mu mzinda.

Khungu lawo lachita makwinyamakwinya pa mafupa awo;

lawuma gwaa ngati nkhuni.

9Amene anaphedwa ndi lupanga aliko bwino kuposa

amene anafa ndi njala;

chifukwa chosowa chakudya cha mʼmunda

iwowa ankafowoka ndi njala mpaka kufa.

10Amayi achifundo afika

pophika ana awo enieni,

ndiwo anali chakudya chawo pamene anthu

anga anali kuwonongeka.

11Yehova wakwaniritsa ukali wake;

wagwetsa pansi mkwiyo wake woopsa.

Ndipo wayatsa moto mʼZiyoni

kuti uwononge maziko ake.

12Mafumu a pa dziko lapansi sanakhulupirire,

kapena wina aliyense wokhala pa dziko lonse,

kuti adani kapena ankhondo akhoza kulowa

pa zipata za Yerusalemu.

13Koma izi zinachitika chifukwa cha kuchimwa kwa aneneri ake

ndi mphulupulu za ansembe ake,

amene ankapha anthu osalakwa pakati pawo.

14Tsopano akungoyendayenda mʼmisewu ya mu mzinda

ngati anthu osaona.

Iwo ndi odetsedwa kwambiri ndi magazi

palibe yemwe angayerekeze nʼkukhudza komwe chovala chawo.

15Anthu akuwafuwulira kuti, “Chokani! Inu anthu odetsedwa!”

“Chokani! Chokani! Musatikhudze ife!”

Akamathawa ndi kumangoyendayenda,

pakati pa anthu a mitundu yonse amati,

“Asakhalenso ndi ife.”

16Yehova mwini wake wawabalalitsa;

Iye sakuwalabadiranso.

Ansembe sakulandira ulemu,

akuluakulu sakuwachitira chifundo.

17Ndiponso maso athu atopa nʼkuyangʼana,

chithandizo chosabwera nʼkomwe,

kuchokera pa nsanja zathu tinadikirira mtundu

wa anthu umene sukanatipulumutsa.

18Anthu ankalondola mapazi athu,

choncho sitikanayenda mʼmisewu yathu mu mzinda.

Chimaliziro chathu chinali pafupi, masiku athu anali owerengeka,

chifukwa chimaliziro chathu chinali chitafika.

19Otilondola akuthamanga kwambiri

kuposa ziwombankhanga mu mlengalenga;

anatithamangitsa mpaka ku mapiri

ndi kutibisalira mʼchipululu.

20Wodzozedwa wa Yehova, mpweya wathu wotipatsa moyo,

anakodwa mʼmisampha yawo.

Tinaganiza kuti tidzakhala pansi pa mthunzi wake

pakati pa mitundu ya anthu.

21Kondwera ndi kusangalala, mwana wamkazi wa Edomu.

Iwe amene umakhala mʼdziko la Uzi.

Koma iwenso chikho chidzakupeza;

udzaledzera mpaka kukhala maliseche.

22Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, chilango chako chidzatha;

Iye sadzatalikitsa nthawi yako ya ukapolo.

Koma Yehova adzalanga machimo ako, iwe mwana wamkazi wa Edomu,

ndi kuyika poyera mphulupulu zako.