Maliro 3 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Maliro 3:1-66

1Ine ndine munthu amene ndaona masautso

ndi ndodo ya ukali wake.

2Wandipititsa kutali ndipo wandiyendetsa

mu mdima osati mʼkuwala;

3zoonadi anandikantha ndi dzanja lake

mobwerezabwereza tsiku lonse.

4Wakalambitsa khungu langa ndi mnofu wanga,

ndipo waphwanya mafupa anga.

5Wandizinga ndi kundizungulira

ndi zowawa ndi zolemetsa.

6Wandikhazika mu mdima

ngati amene anafa kale.

7Wandimangira khoma kotero kuti sindingathawe,

wandimanga ndi maunyolo.

8Ngakhale pamene ndifuwula kapena kupempha chithandizo,

amakana pemphero langa.

9Wanditsekera njira yanga ndi miyala yosema;

ndipo wakhotetsa tinjira tanga.

10Wandidikirira ngati chimbalangondo,

wandibisalira ngati mkango.

11Wandikokera pambali ndi kundingʼambangʼamba,

ndipo wandisiya wopanda thandizo.

12Wakoka uta wake

ndipo walunjikitsa mivi yake pa ine.

13Walasa mtima wanga

ndi mivi ya mʼphodo mwake.

14Ndinakhala choseketsa cha anthu anga onse;

amandinyodola mʼnyimbo zawo tsiku lonse.

15Wandidyetsa zowawa

ndipo wandimwetsa ndulu.

16Wathyola mano anga ndi miyala;

wandiviviniza mʼfumbi;

17Wandichotsera mtendere;

ndayiwala kuti kupeza bwino nʼchiyani.

18Choncho ndikuti, “Ulemerero wanga wachoka

ndi zonse zimene ndimayembekeza kwa Yehova.”

19Kukumbukira masautso anga ndi kusowa pokhala,

zili ngati zowawa ndi ndulu.

20Ine ndikuzikumbukira bwino izi,

ndipo moyo wanga wathedwa mʼkati mwanga.

21Komabe ndimakumbukira zimenezi,

nʼchifukwa chake ndili ndi chiyembekezo.

22Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu,

ndi chifundo chake ndi chosatha.

23Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse;

kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.

24Mu mtima mwanga ndimati, “Yehova ndiye zanga zonse;

motero ndimamuyembekezera.”

25Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye,

kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo;

26nʼkwabwino kudikira chipulumutso cha

Yehova modekha.

27Nʼkwabwino kuti munthu asenze goli

pamene ali wamngʼono.

28Akhale chete pa yekha,

chifukwa Yehova wamusenzetsa golilo.

29Abise nkhope yake mʼfumbi

mwina chiyembekezo nʼkukhalapobe.

30Apereke tsaya lake kwa iye amene angamumenye,

ndipo amuchititse manyazi.

31Chifukwa Ambuye satayiratu

anthu nthawi zonse.

32Ngakhale amabweretsa zowawa, Iye adzawachitira chifundo,

chifukwa chikondi chake ndi chosatha.

33Pakuti sabweretsa masautso mwadala,

kapena zowawa kwa ana a anthu.

34Kuphwanya ndi phazi

a mʼndende onse a mʼdziko,

35kukaniza munthu ufulu wake

pamaso pa Wammwambamwamba,

36kumana munthu chiweruzo cholungama—

kodi Ambuye saona zonsezi?

37Kodi ndani angayankhule zinthu nʼkuchitika

ngati Ambuye sanavomereze?

38Kodi zovuta ndi zabwino sizituluka

mʼkamwa mwa Wammwambamwamba?

39Kodi nʼchifukwa chiyani munthu aliyense wamoyo amadandaula

akalangidwa chifukwa cha machimo ake?

40Tiyeni tisanthule ndi kuyesa njira zathu,

ndipo tiyeni tibwerere kwa Yehova.

41Tiyeni tikweze mitima yathu ndi manja athu

kwa Mulungu kumwamba ndipo tinene kuti:

42“Ife tachimwa ndi kuwukira

ndipo inu simunakhululuke.

43“Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola ndipo

mwatitha mopanda chifundo.

44Mwadzikuta mu mtambo

kotero mapemphero athu sakukufikani.

45Mwatisandutsa zinyatsi ndi zinyalala

pakati pa mitundu ya anthu.

46“Adani anthu atitsekulira pakamwa.

47Ife tadzazidwa ndi mantha pakuti tagwa mʼdzenje,

tapasuka ndi kuwonongedwa.”

48Misozi mʼmaso mwanga ikungoti mbwembwembwe

chifukwa anthu anga akuwonongedwa.

49Misozi idzatsika kosalekeza,

ndipo sidzasiya,

50mpaka Yehova ayangʼane pansi

kuchokera kumwamba ndi kuona.

51Mtima wanga ukupweteka poona zimenezi

chifukwa cha akazi onse a mu mzinda.

52Akundisaka ngati mbalame,

amene anali adani anga, popanda chifukwa.

53Ayesa kundipha pondiponya mʼdzenje

ndi kundiponya miyala;

54madzi anamiza mutu wanga

ndipo ndinkaganiza kuti imfa yayandikira.

55Ndinayitana dzina lanu Inu Yehova,

kuchokera mʼdzenje lozama.

56Inu munamva kudandaula kwanga. “Mundimvere

kulira kwanga kopempha thandizo.”

57Munafika pafupi pamene ndinakuyitanani,

ndipo munati, “Usaope.”

58Inu Ambuye munandiwombola ku mlandu wanga;

munapulumutsa moyo wanga.

59Yehova, mwaona zoyipa zimene andichitira.

Mundiweruzire ndinu!

60Mwaona kuzama kwa kubwezera kwawo,

chiwembu chawo chonse pa ine.

61Inu Yehova mwamva kunyoza kwawo,

chiwembu chawo chonse pa ine,

62manongʼonongʼo a adani anga

ondiwukira ine tsiku lonse.

63Tawaonani! Kaya ali pansi kapena kuyimirira,

akundinyoza mu nyimbo zawo.

64Inu Yehova, muwabwezere chowayenera,

chifukwa cha zimene manja awo achita.

65Phimbani mitima yawo,

ndipo matemberero anu akhale pa iwo!

66Muwalondole mwaukali ndipo

muwawonongeretu pa dziko lapansi.

Священное Писание

Плач 3:1-66

Великая верность Всевышнего

1Я человек, испытавший горе,

потому что Вечный покарал меня

жезлом Своего гнева.

2Он погнал меня и ввёл

во тьму, а не в свет.

3Несомненно, Он обратил Свою руку против меня

и обращает её снова и снова в течение всего дня.

4Он состарил кожу мою и плоть мою,

сокрушил кости мои.

5Он осадил меня и окружил

горечью и тяготою.

6Погрузил меня во мрак,

как давно умерших.

7Окружил меня стеной, чтобы я не мог выйти,

заковал меня в тяжёлые цепи.

8Даже когда я взываю и прошу о помощи,

Он не обращает внимания на мою молитву.

9Камнями Он преградил мне путь,

искривил стези мои.

10Он подобен медведю в засаде

или затаившемуся льву.

11Сбил меня с пути и растерзал меня,

оставив без помощи.

12Натянул Он Свой лук

и сделал меня мишенью для стрел Своих.

13Он пронзил моё сердце

стрелами из Своего колчана.

14Стал я посмешищем для всего моего народа,

весь день в песнях насмехаются надо мной.

15Он напоил меня горькими травами

и насытил горечью.

16Камнями сокрушил зубы мои,

втоптал меня в пыль.

17Лишена душа моя мира,

я позабыл о благоденствии.

18И сказал я: «Исчезло величие моё

и надежда моя на Вечного».

19Помню лишь о страдании и скитании,

во мне лишь горечь и желчь.

20Сильна память об этом,

поникла душа моя.

21Но вот что говорю я себе,

вот что даёт мне надежду:

22«Милость Вечного никогда не иссякает3:22 Или: «По милости Вечного мы не исчезли, потому что…»,

сострадание Его не истощается.

23Они обновляются3:23 Или: «Оно обновляется». каждое утро;

велика верность Твоя!»

24Я сказал себе: «Вечный – часть моя,

потому я буду надеяться на Него».

25Благ Вечный к тем, кто уповает на Него,

к тем, кто ищет Его.

26Благо тому, кто молча ожидает

спасения от Вечного.

27Благо человеку, который несёт ярмо

в юности своей.

28Пусть сидит в уединении и молчании,

потому что бремя это возложил на него Вечный.

29Пусть склонится в смирении,

может быть, есть ещё надежда.

30Пусть подставляет щёку свою бьющему

и насыщается бесчестием,

31ведь Владыка не отвергает людей навеки!

32И хотя Он посылает страдания,

Он же потом и помилует

по Своей великой любви.

33Ведь не по изволению сердца Своего

Он приносит бедствие и горе людям.

34А когда топчут ногами

всех узников земли,

35лишают человека правосудия

перед лицом Высочайшего,

36притесняют человека на суде –

разве Владыка всего этого не видит?

37Кто может сказать – и исполнится,

если Владыка не повелит этому случиться?

38Не по слову ли Высочайшего

приходят бедствие и благо?

39Для чего жаловаться человеку,

ведь он остался жив, хоть и был наказан за грехи свои?

40Проверим же пути наши и испытаем их

и вернёмся к Вечному.

41Вознесём сердца наши и руки

к Всевышнему на небесах и скажем:

42«Мы согрешили и восстали против Тебя,

и Ты не простил нас.

43Ты покрыл Себя гневом и преследовал нас,

губя без пощады.

44Ты скрыл Себя облаком,

чтобы не доходила наша молитва.

45Ты сделал нас грязью и сором

среди народов.

46Все враги наши широко разинули

пасть свою на нас.

47Мы страдали от ужаса и западни,

опустошения и разорения».

48Ручьями слёзы текут из глаз моих,

потому что народ мой уничтожен.

49Слёзы мои будут течь,

не останавливаясь,

без перерыва,

50пока Вечный не посмотрит с небес

и не увидит.

51Я смотрю, и горечь наполняет душу мою

за всех дочерей моего города.

52Без причины враги мои пытались

поймать меня, словно птицу,

53бросили меня в яму

и камнями закидали меня.

54Воды сомкнулись над моей головой,

и я подумал: «Погиб я».

55Я воззвал к имени Твоему, о Вечный,

из ямы глубокой.

56Ты услышал голос мой;

не закрывай же ухо Своё

от моей мольбы и плача моего.

57Ты приближался, когда я взывал к Тебе,

и говорил: «Не бойся»3:57 Ср. Иер. 1:7-8..

58О Владыка, Ты защищал дело души моей,

искуплял жизнь мою.

59Ты видишь, Вечный, угнетение моё,

рассуди же тяжбу мою.

60Ты видишь всю их мстительность,

все их заговоры против меня.

61О Вечный, Ты слышишь их оскорбления,

все их заговоры против меня,

62как враги перешёптываются

обо мне весь день.

63Взгляни на них! Сидят ли они, стоят ли,

они насмехаются надо мною в своих песнях.

64Воздай им, Вечный,

по делам их рук.

65Мраком покрой их сердца,

и пусть проклятие Твоё будет на них.

66Преследуй их в гневе

и истреби их из поднебесья, о Вечный.