Malaki 4 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Malaki 4:1-6

Tsiku la Yehova

1Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndithu tsiku likubwera; lidzayaka ngati ngʼanjo. Anthu onse odzikuza, ndi aliyense ochita zoyipa adzapsa ngati chiputu, ndipo pa tsiku limene likubweralo adzapserera ndi moto. Sipadzatsalira muzu kapena nthambi. 2Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola. 3Tsiku limenelo inu mudzapondereza anthu oyipa; adzakhala phulusa ku mapazi anu pa tsiku limene Ine ndidzachite zinthu zimenezi,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

4Kumbukirani zophunzitsa za mtumiki wanga Mose, malamulo ndi malangizo amene ndinamupatsa pa Horebu kuti awuze Aisraeli onse.

5“Taonani, ndidzakutumizirani mneneri Eliya lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. 6Iye adzabweza mitima ya makolo kwa ana awo, ndi mitima ya ana kwa makolo awo. Kupanda kutero ndidzabwera kudzakantha dziko lanu ndi temberero.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

瑪拉基書 4:1-6

耶和華的日子

1「萬軍之耶和華說,『那日要來臨了,就像燒紅的火爐,所有狂妄自大、作惡多端的人都要像碎稭一樣被火燒盡,連根帶枝,蕩然無存。 2但必有公義的太陽為你們這些敬畏我名的人升起,它的光芒有醫治的能力。你們必像欄中出來的牛犢一樣歡欣跳躍。 3到我所定的日子,你們必踐踏惡人,他們必成為你們腳下的塵土。』這是萬軍之耶和華說的。

4「你們要記住我僕人摩西的律法,就是我在何烈山藉著他傳給以色列人的律例和典章。

5「看啊,在耶和華那偉大而可畏的日子來臨以前,我必差遣以利亞先知到你們那裡。 6他必使父親的心轉向兒女,兒女的心轉向父親,免得我來用咒詛毀滅這地方。」