Malaki 3 – CCL & NIRV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Malaki 3:1-18

1Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndidzatuma mthenga wanga amene adzakonza njira pamaso panga. Kenaka mwadzidzidzi Ambuye amene mukumufunafuna adzafika ku Nyumba yake. Mthenga wapangano amene mukumuyembekezera adzabwera.”

2Koma ndani adzatha kupirira pa tsiku la kubwera kwake? Ndani adzatha kuyima pamene Iye wafika? Pakuti adzakhala ngati moto wa mmisiri wa pa ngʼanjo, kapenanso ngati sopo wa munthu wochapa. 3Iye adzachita kukhalira pansi ngati mmisiri woyenga ndi woyeretsa siliva. Iye adzayeretsa Alevi ndi kuwayenga ngati golide ndi siliva. Pamenepo Yehova adzakhala ndi anthu amene azidzabweretsa zopereka mwachilungamo, 4ndipo Yehova adzalandira zopereka za Yuda ndi Yerusalemu, ngati masiku akale, masiku amakedzana.

5Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Tsono ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni. Mosataya nthawi ndidzanena mawu otsutsa mfiti, achigololo, a umboni wonama, amene salipira bwino antchito awo, amene amazunza akazi ndi ana amasiye, amene saweruza alendo mwachilungamo, komanso amene sandiopa Ine.”

Kuba za Mulungu

6“Ine ndine Yehova, ndipo sindisintha. Choncho inu zidzukulu za Yakobo, simunawonongedwe. 7Kuyambira nthawi ya makolo anu mwakhala mukuphwanya malamulo anga ndipo simunawatsatire. Bwererani kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

“Koma inu mukufunsa kuti, ‘Tibwerere motani kwa Yehova?’

8“Kodi munthu angathe kuba za Mulungu? Komatu inu mumandibera.

“Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi timakuberani motani?’

“Pa zakhumi ndi pa zopereka. 9Mtundu wanu wonse ndinu otembereredwa, chifukwa mukundibera. 10Bweretsani chakhumi chathunthu ku nyumba yosungira, kuti mukhale chakudya mʼnyumba mwanga.” Akutero Yehova Wamphamvuzonse, “Tandiyesani, ndipo muone ngati sindidzatsekula zipata zakumwamba, ndi kukugwetserani madalitso ochuluka amene mudzasowe malo owayikamo. 11Ndidzaletsa tizirombo kuti tisawononge mbewu zanu, ndipo mpesa wa mʼminda mwanu zipatso zake sizidzayoyoka,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. 12“Motero anthu amitundu yonse adzakutchulani odala, pakuti dziko lanu lidzakhala lokondweretsa,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

13Yehova akuti, “Mwayankhula mawu owawa onena za Ine.

“Komabe inu mukufunsa kuti, ‘Kodi tanena chiyani chotsutsana nanu?’

14“Mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu nʼkosapindulitsa. Kodi timapindulanji pochita zofuna zake, ndi kumayenda ngati anamfedwa pamaso pa Yehova Wamphamvuzonse? 15Koma tsono ife timati anthu odzikuza ndiye odalitsika. Kunena zoona anthu oyipa ndiye amapeza bwino, ngakhale amene amanyoza Mulungu amapulumuka.’ ”

16Ndipo woopa Yehova anayamba kukambirana, ndipo Yehova anamvetsera. Buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, lonena za amene amaopa Yehova ndi kulemekeza dzina lake.

17Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu amenewo adzakhala anga, tsiku limene Ine ndidzachita izi, adzakhala angaanga. Ndidzawaleka osawalanga monga mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira. 18Pamenepo mudzaonanso kusiyana pakati pa anthu olungama ndi oyipa, pakati pa amene amatumikira Mulungu ndi amene satumikira Mulungu.”

New International Reader’s Version

Malachi 3:1-18

1The Lord who rules over all says, “I will send my messenger. He will prepare my way for me. Then suddenly the Lord you are looking for will come to his temple. The messenger of the covenant will come. He is the one you long for.”

2But who can live through the day when he comes? Who will be left standing when he appears? He will be like a fire that makes things pure. He will be like soap that makes things clean. 3He will act like one who makes silver pure. And he will purify the Levites, just as gold and silver are purified with fire. Then these men will bring proper offerings to the Lord. 4And the offerings of Judah and Jerusalem will be acceptable to him. It will be as it was in days and years gone by.

5“So I will come and put you on trial. I will be quick to bring charges against all of you,” says the Lord who rules over all. “I will bring charges against you sinful people who do not have any respect for me. That includes those who practice evil magic. It includes those who commit adultery and those who tell lies in court. It includes those who cheat workers out of their pay. It includes those who treat widows badly. It also includes those who mistreat children whose fathers have died. And it includes those who take away the rights of outsiders in the courts.

Breaking the Covenant by Stealing From God

6“I am the Lord. I do not change. That is why I have not destroyed you members of Jacob’s family. 7You have turned away from my rules. You have not obeyed them. You have lived that way ever since the days of your people of long ago. Return to me. Then I will return to you,” says the Lord who rules over all.

“But you ask, ‘How can we return?’

8“Will a mere human being dare to steal from God? But you rob me!

“You ask, ‘How are we robbing you?’

“By holding back your offerings. You also steal from me when you do not bring me a tenth of everything you produce. 9So you are under my curse. In fact, your whole nation is under my curse. That is because you are robbing me. 10Bring the entire tenth to the storerooms in my temple. Then there will be plenty of food. Test me this way,” says the Lord. “Then you will see that I will throw open the windows of heaven. I will pour out so many blessings that you will not have enough room to store them. 11I will keep bugs from eating up your crops. And your grapes will not drop from the vines before they are ripe,” says the Lord. 12“Then all the nations will call you blessed. Your land will be delightful,” says the Lord who rules over all.

Israel Speaks With Pride Against the Lord

13“You have spoken with pride against me,” says the Lord.

“But you ask, ‘What have we spoken against you?’

14“You have said, ‘It is useless to serve God. What do we gain by obeying his laws? And what do we get by pretending to be sad in front of the Lord? 15But now we call proud people blessed. Things go well with those who do what is evil. And God doesn’t even punish those who test him.’ ”

Those Who Respect the Lord

16Those who had respect for the Lord talked with one another. And the Lord heard them. A list of people and what they did was written in a book in front of him. It included the names of those who respected the Lord and honored him.

17“The day is coming when I will judge,” says the Lord who rules over all. “On that day they will be my special treasure. I will spare them just as a father loves and spares his son who serves him. 18Then once again you will see the difference between godly people and sinful people. And you will see the difference between those who serve me and those who do not.