Machitidwe a Atumwi 8 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 8:1-40

1Ndipo Saulo anavomerezana nawo pa imfa ya Stefano.

Kuzunzika kwa Mpingo

Tsiku lomwelo, mpingo wa mu Yerusalemu unayamba kuzunzidwa, ndipo onse, kupatulapo atumwi, anabalalikira ku madera onse a Yudeya ndi Samariya. 2Anthu okonda Mulungu anayika maliro a Stefano ndipo anamulira kwambiri. 3Koma Saulo anayamba kuwononga mpingo. Amapita nyumba ndi nyumba, ndipo amagwira amuna ndi amayi ndi kukawatsekera ku ndende.

Filipo ku Samariya

4Okhulupirira amene anabalalika amalalikira konse kumene amapita. 5Filipo anapita ku mzinda wa ku Samariya ndipo analalikira za Khristu kumeneko. 6Gulu la anthu litamva Filipo akulalikira komanso kuona zizindikiro zozizwitsa zimene ankazichita, onse anamvetsetsa zimene iye amanena. 7Mizimu yoyipa inatuluka mwa anthu ambiri ikufuwula kwambiri ndipo ambiri amene anali akufa ziwalo ndi olumala anachiritsidwa. 8Kotero munali chimwemwe chachikulu mu mzindawo.

Simoni Wamatsenga

9Koma mu mzindawo munali munthu dzina lake Simoni, amene amachita za matsenga ndi kudabwitsa anthu a mu Samariya. Iye amadzitamandira kuti ndi wopambana, 10ndipo anthu onse, aakulu ndi aangʼono anamumvera ndi kunena kuti, “Munthu uyu ndi mphamvu ya Mulungu yotchedwa Mphamvu yayikulu.” 11Anthu amamutsata chifukwa kwa nthawi yayitali amawadabwitsa ndi matsenga akewo. 12Koma atakhulupirira Filipo akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ndiponso dzina la Yesu Khristu, anthuwo anabatizidwa amuna ndi amayi. 13Nayenso Simoni anakhulupirira ndipo anabatizidwa, natsatira Filipo kulikonse, ndipo anadabwa kwambiri pamene anaona zizindikiro zazikulu ndi zozizwitsa.

14Atumwi a ku Yerusalemu atamva kuti anthu a ku Samariya analandira Mawu a Mulungu, anatumiza Petro ndi Yohane. 15Atafika anawapempherera kuti alandire Mzimu Woyera, 16chifukwa Mzimu Woyera anali asanafike pa wina aliyense wa iwo; anali atangobatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu. 17Ndipo Petro ndi Yohane anasanjika manja awo pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.

18Simoni ataona kuti Mzimu anaperekedwa kwa iwo atumwi atawasanjika manja, iye anafuna kuwapatsa ndalama ndipo anati, 19“Inenso ndipatseni mphamvu imeneyi kuti aliyense amene ndimusanjika manja anga azilandira Mzimu Woyera.”

20Petro anayankha kuti, “Ndalama zako utayike nazo pamodzi, chifukwa unaganiza kuti ungathe kugula mphatso ya Mulungu ndi ndalama! 21Ulibe gawo kapena mbali pa utumikiwu, chifukwa mtima wako suli wolungama pamaso pa Mulungu. 22Lapa zoyipa zakozi ndipo upemphere kwa Ambuye. Mwina adzakukhululukira maganizo a mu mtima mwako. 23Pakuti ine ndikuona kuti ndiwe wowawidwa mtima ndiponso kapolo wa tchimo.”

24Ndipo Simoni anayankha, “Mundipempherere kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.”

25Atatha kuchitira umboni ndi kulalikira mawu a Ambuye, Petro ndi Yohane anabwerera ku Yerusalemu, atalalikira Uthenga Wabwino mʼmidzi yambiri ya Asamariya.

Filipo ndi Nduna ya Zachuma ya ku Etiopia

26Mngelo wa Ambuye anati kwa Filipo, “Nyamuka pita chakummwera, ku msewu wa ku chipululu wopita ku Gaza kuchokera ku Yerusalemu.” 27Ndipo ananyamuka napita, ndipo akuyenda anakumana ndi munthu wa ku Etiopia wa udindo waukulu woyangʼanira chuma cha Kandake, mfumu yayikazi ya ku Etiopia. Munthu ameneyu anapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu, 28ndipo akubwerera kwawo atakwera pa galeta lake amawerenga buku la mneneri Yesaya. 29Mzimu anamuwuza Filipo kuti, “Pita pa galeta ilo ndipo ukakhale pafupi nalo.”

30Pamenepo Filipo anathamangira ku galeta ndipo anamva munthuyo akuwerenga buku la mneneri Yesaya. Filipo anamufunsa kuti, “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazi?”

31Iye anayankha kuti, “Ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?” Ndipo iye anayitana Filipo kuti abwere ndikukhala naye mʼgaleta.

32Mawu amene ndunayo imawerenga anali awa:

“Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira,

kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta,

momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.

33Iye ananyozedwa ndipo panalibe chilungamo pa mlandu wake.

Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake

poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo?”

34Ndunayo inamufunsa Filipo kuti, “Chonde, uzeni, kodi mneneri akuyankhula za ndani, za iye mwini kapena za munthu wina?” 35Pamenepo Filipo anayambira pa malemba omwewo kumuwuza za Uthenga Wabwino wa Yesu.

36Akuyenda mu msewu anafika pamalo pamene panali madzi ndipo ndunayo inati, “Taonani madzi awa. Kodi pali chondiletsa kuti ndibatizidwe?” 37Filipo anati, “Ngati mukhulupirira ndi mtima wanu wonse mukhoza kubatizidwa.” Ndunayo inayankha kuti, “Ine ndikukhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu.” 38Ndipo analamulira galeta kuti liyime. Onse awiriwo, Filipo ndi Ndunayo anatsika ndi kulowa mʼmadzi ndipo Filipo anamubatiza. 39Pamene iwo anatuluka mʼmadzimo, Mzimu wa Ambuye anamukwatula Filipo, ndipo Ndunayo sinamuonenso, koma inapitiriza ulendo wake ikusangalala. 40Koma Filipo anapezeka kuti ali ku Azoto ndipo anazungulira konse, kulalikira Uthenga Wabwino mʼmizinda yonse mpaka anakafika ku Kaisareya.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

使徒行傳 8:1-40

教會受迫害

1當時,掃羅也贊成殺死司提凡。從那天起,耶路撒冷的教會開始遭到極大的迫害。除了使徒之外,門徒都分散到猶太撒瑪利亞各地。 2有些虔誠人將司提凡埋葬了,為他大聲痛哭。

3掃羅卻在摧毀教會,他挨家挨戶搜尋,把男女信徒抓進監裡。

腓利傳揚福音

4但那些逃往各地的信徒逃到哪裡,就將福音傳到哪裡。 5腓利來到撒瑪利亞城宣講基督。 6城裡的人耳聞目睹他所行的神蹟,都聚精會神地聽他講道。 7當時有許多人被污鬼附身,那些污鬼大聲喊叫著被趕了出來。還有不少癱子和瘸子也被醫好了。 8城裡洋溢著歡樂的氣氛。

術士歸主

9有個名叫西門的術士,向來妄自尊大,曾用邪術使撒瑪利亞人驚奇不已。 10無論貴賤,眾人都聽從他,稱他為「上帝的大能者」。 11他們聽從他,因為他長期用邪術迷惑他們。 12後來,他們相信了腓利所傳關於上帝的國度和耶穌基督的福音,男男女女都接受了洗禮。 13西門本人也信了基督,接受了洗禮,並常常追隨腓利左右。腓利所行的神蹟奇事令他非常驚奇。

14耶路撒冷的使徒聽說撒瑪利亞人接受了上帝的道,就派彼得約翰去那裡。 15二人到了,為那些信徒禱告,好讓他們領受聖靈, 16因為他們只是奉耶穌的名受了洗,聖靈還沒有降在他們身上。 17使徒把手按在他們身上,他們就領受了聖靈。

18西門看見使徒把手一按在人身上,就有聖靈賜下來,便拿錢給使徒, 19說:「請把這能力也給我吧,以便我把手按在誰身上,就使誰領受聖靈。」

20彼得責備他說:「你和你的錢都一同毀滅吧!因為你以為可以用錢買上帝的恩賜! 21你在上帝面前心術不正,休想在我們的事工上有份。 22你要悔改,離棄邪惡,向主禱告,或許主會赦免你心中的邪念。 23我看得出你正因為嫉妒而心裡充滿了苦澀,被罪惡捆綁。」

24西門說:「請為我求求主,免得我遭受你們所說的刑罰。」

25彼得約翰為主做見證,傳講主的道。之後,他們啟程回耶路撒冷,沿途又在撒瑪利亞各村莊傳揚福音。

太監歸主

26有一天,主的天使對腓利說:「起來,向南走,往耶路撒冷通往迦薩的路去。」那條路很荒涼。 27腓利立刻動身,結果在那條路上遇見一個衣索匹亞的太監。他是衣索匹亞女王甘大基手下的重臣,負責管理國庫。他剛從耶路撒冷參加敬拜回來, 28正坐在車上誦讀以賽亞先知的書。 29聖靈吩咐腓利:「趕上去,貼近那輛馬車!」

30腓利跑上前,聽見太監在誦讀以賽亞先知的書,就問:「你明白所讀的經文嗎?」

31他說:「沒有人為我解釋,我怎能明白呢?」他就請腓利上車和他一起坐。 32他剛才念的那段經文是:

「祂默然不語,

像被人牽去宰殺的羔羊,

又如在剪毛人手下一聲不吭的綿羊。

33祂忍受恥辱,

無人為祂主持公道,

誰能明白那個世代呢?

因為祂的生命竟然被奪去。」

34太監問腓利:「請問先知是在說誰?在說他自己還是在說別人?」 35腓利就從這段經文入手向他傳耶穌的福音。 36他們往前走的時候,經過一處有水的地方,太監說:「你看,這裡有水,我可以在這裡接受洗禮嗎?」 37腓利說:「只要你全心相信,當然可以。」太監說:「我相信耶穌基督是上帝的兒子!」

38於是,太監吩咐停車,二人一同下到水裡,腓利為他施洗。 39他們從水裡上來時,主的靈把腓利帶走了。太監看不見腓利了,就繼續前行,滿心歡喜。 40後來,腓利出現在亞鎖都。他走遍那裡,在各城各鄉傳揚福音,直到凱撒利亞