Machitidwe a Atumwi 4 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 4:1-37

Petro ndi Yohane ku Bwalo la Akulu

1Pamene Petro ndi Yohane amayankhula ndi anthu, kunabwera ansembe, mkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndiponso Asaduki. 2Iwo anakhumudwa kwambiri chifukwa atumwiwo amaphunzitsa anthu ndi kumalalikira za kuuka kwa akufa mwa Yesu. 3Iwo anagwira Petro ndi Yohane, popeza kunali kutada, anawayika mʼndende mpaka mmawa mwake. 4Koma anthu ambiri amene anamva uthenga anakhulupirira, ndipo chiwerengero cha anthu chinakwana 5,000.

5Mmawa mwake olamulira, akulu ndi aphunzitsi a malamulo anasonkhana mu Yerusalemu. 6Panali Anasi, Mkulu wa ansembe, Kayafa, Yohane ndi Alekisandro ndi ana a banja la mkulu wa ansembe. 7Iwo anayimiritsa Petro ndi Yohane patsogolo pawo nayamba kuwafunsa kuti, “Kodi munachita zimenezi ndi mphamvu yanji kapena mʼdzina la yani?”

8Petro wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anawawuza kuti, “Inu olamulira ndi akulu! 9Ngati ife tikufunsidwa lero chifukwa cha ntchito yabwino imene yachitika pa munthu wolumala miyendo ndi mmene iye anachiritsidwira, 10tsono dziwani izi inu ndi aliyense mu Israeli: munthuyu akuyima pamaso panu, wochiritsidwa kwathunthu, ndi chifukwa cha dzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti amene munamupachika koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa. 11Iye ndi

“ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana,

umenewo wasanduka mwala wa pa ngodya!’

12Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”

13Ataona kulimba mtima kwa Petro ndi Yohane ndi kuzindikira kuti anali osaphunzira, anthu wamba, anadabwa kwambiri ndipo anazindikira kuti anthuwa anakhala pamodzi ndi Yesu. 14Koma popeza iwo amamuona munthu amene anachiritsidwa atayima pamodzi ndi iwo, palibe chimene akananena. 15Chifukwa chake anawalamula kuti atuluke mʼbwalo la milandu ndipo akulu abwalowo anayamba kukambirana. 16Iwo anafunsana kuti, “Kodi anthuwa tichite nawo chiyani? Pakuti aliyense okhala mu Yerusalemu akudziwa kuti achita chodabwitsachi, ndipo ife sitingathe kukana. 17Koma kuti mbiriyi isapitirire kuwanda pakati pa anthu, ife tiwachenjeze anthu amenewa kuti asayankhulenso kwa wina aliyense mʼdzina la Yesu.”

18Pamenepo anawayitananso ndipo anawalamula kuti asayankhule kapena kuphunzitsa konse mʼdzina la Yesu. 19Koma Petro ndi Yohane anayankha kuti, “Weruzani nokha ngati nʼkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu. 20Ife sitingaleke kuyankhula za zimene tinaziona ndi kuzimva.”

21Atawonjeza kuwaopseza anawamasula. Sanathe kugwirizana njira yowalangira, chifukwa anthu onse amayamika Mulungu chifukwa cha zimene zinachitika. 22Ndipo munthu amene anachiritsidwayo anali ndi zaka makumi anayi.

Okhulupirira Apemphera

23Atamasulidwa Petro ndi Yohane anapita kwa anzawo ndipo anawafotokozera zonse zimene akulu a ansembe ndi akulu anawawuza. 24Anthu atamva zimenezi anafuwula ndi mtima umodzi napemphera kwa Mulungu. Iwo anati, “Ambuye wolamulira zonse, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndiponso zonse zili mʼmenemo. 25Inu munayankhula mwa Mzimu Woyera kudzera pakamwa pa Davide kholo lathu, mtumiki wanu kuti,

“ ‘Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu,

ndipo akonzekera kuchita zopandapake?

26Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo;

ndipo olamulira asonkhana pamodzi

kulimbana ndi Ambuye

ndi wodzozedwa wakeyo.’

27Zoonadi, Herode ndi Pontiyo Pilato anasonkhana pamodzi ndi amitundu ndiponso Aisraeli, mu mzinda muno, kupanga zolimbana ndi mtumiki wanu woyera Yesu, amene Inu munamudzoza. 28Iwo anachita zimene munakonzeratu mwachifuniro chanu ndi mphamvu yanu kuti zichitike. 29Tsopano, Ambuye taonani kuti atiopseza, tithandizeni ife atumiki anu, kuti tiyankhule mawu anu molimba mtima. 30Tambasulani dzanja lanu kuchiritsa anthu ndipo kuti, zizindikiro zodabwitsa zichitike mʼdzina la mtumiki wanu woyera Yesu.”

31Iwo atatha kupemphera, malo amene anasonkhanapo anagwedezeka. Ndipo iwo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo anayankhula Mawu a Mulungu molimba mtima.

Okhulupirira Agawana Zinthu Zawo

32Okhulupirira onse anali a mtima umodzi, ndi maganizo amodzi. Palibe munthu amene amati zomwe anali nazo zinali zake zokha, koma amagawana chilichonse chimene anali nacho. 33Atumwi anapitirira kuchitira umboni mwa mphamvu zakuuka kwa Ambuye Yesu, ndipo pa iwo panali chisomo chochuluka. 34Panalibe anthu osowa kanthu pakati pawo. Pakuti amene anali ndi malo, kapena nyumba amagulitsa ndi kubweretsa ndalamazo 35ndi kuzipereka kwa atumwi, ndipo zimagawidwa kwa aliyense amene anali ndi chosowa.

36Yosefe, wa fuko la Levi, wochokera ku Kupro amene atumwi anamutcha Barnaba, kutanthauza kuti mwana wachilimbikitso, 37anagulitsa munda wake ndipo anadzapereka ndalamazo kwa atumwi.

King James Version

Acts 4:1-37

1And as they spake unto the people, the priests, and the captain of the temple, and the Sadducees, came upon them, 2Being grieved that they taught the people, and preached through Jesus the resurrection from the dead. 3And they laid hands on them, and put them in hold unto the next day: for it was now eventide. 4Howbeit many of them which heard the word believed; and the number of the men was about five thousand.

5¶ And it came to pass on the morrow, that their rulers, and elders, and scribes, 6And Annas the high priest, and Caiaphas, and John, and Alexander, and as many as were of the kindred of the high priest, were gathered together at Jerusalem. 7And when they had set them in the midst, they asked, By what power, or by what name, have ye done this? 8Then Peter, filled with the Holy Ghost, said unto them, Ye rulers of the people, and elders of Israel, 9If we this day be examined of the good deed done to the impotent man, by what means he is made whole; 10Be it known unto you all, and to all the people of Israel, that by the name of Jesus Christ of Nazareth, whom ye crucified, whom God raised from the dead, even by him doth this man stand here before you whole. 11This is the stone which was set at nought of you builders, which is become the head of the corner. 12Neither is there salvation in any other: for there is none other name under heaven given among men, whereby we must be saved.

13¶ Now when they saw the boldness of Peter and John, and perceived that they were unlearned and ignorant men, they marvelled; and they took knowledge of them, that they had been with Jesus. 14And beholding the man which was healed standing with them, they could say nothing against it. 15But when they had commanded them to go aside out of the council, they conferred among themselves, 16Saying, What shall we do to these men? for that indeed a notable miracle hath been done by them is manifest to all them that dwell in Jerusalem; and we cannot deny it. 17But that it spread no further among the people, let us straitly threaten them, that they speak henceforth to no man in this name. 18And they called them, and commanded them not to speak at all nor teach in the name of Jesus. 19But Peter and John answered and said unto them, Whether it be right in the sight of God to hearken unto you more than unto God, judge ye. 20For we cannot but speak the things which we have seen and heard. 21So when they had further threatened them, they let them go, finding nothing how they might punish them, because of the people: for all men glorified God for that which was done. 22For the man was above forty years old, on whom this miracle of healing was shewed.

23¶ And being let go, they went to their own company, and reported all that the chief priests and elders had said unto them. 24And when they heard that, they lifted up their voice to God with one accord, and said, Lord, thou art God, which hast made heaven, and earth, and the sea, and all that in them is: 25Who by the mouth of thy servant David hast said, Why did the heathen rage, and the people imagine vain things? 26The kings of the earth stood up, and the rulers were gathered together against the Lord, and against his Christ. 27For of a truth against thy holy child Jesus, whom thou hast anointed, both Herod, and Pontius Pilate, with the Gentiles, and the people of Israel, were gathered together, 28For to do whatsoever thy hand and thy counsel determined before to be done. 29And now, Lord, behold their threatenings: and grant unto thy servants, that with all boldness they may speak thy word, 30By stretching forth thine hand to heal; and that signs and wonders may be done by the name of thy holy child Jesus.

31¶ And when they had prayed, the place was shaken where they were assembled together; and they were all filled with the Holy Ghost, and they spake the word of God with boldness. 32And the multitude of them that believed were of one heart and of one soul: neither said any of them that ought of the things which he possessed was his own; but they had all things common. 33And with great power gave the apostles witness of the resurrection of the Lord Jesus: and great grace was upon them all. 34Neither was there any among them that lacked: for as many as were possessors of lands or houses sold them, and brought the prices of the things that were sold, 35And laid them down at the apostles’ feet: and distribution was made unto every man according as he had need. 36And Joses, who by the apostles was surnamed Barnabas, (which is, being interpreted, The son of consolation,) a Levite, and of the country of Cyprus, 37Having land, sold it, and brought the money, and laid it at the apostles’ feet.