Machitidwe a Atumwi 23 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 23:1-35

1Paulo anayangʼanitsitsa anthu a Bwalo Lalikulu nati, “Abale anga, ndakhala ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu mpaka lero lino.” 2Chifukwa cha mawu amenewa, mkulu wa ansembe Ananiya analamulira amene anali pafupi ndi Paulo kuti amumenye pakamwa. 3Pamenepo Paulo anamuwuza kuti, “Mulungu adzakukantha, iwe munthu wachiphamaso! Wakhala pamenepo kuti undiweruze ine monga mwalamulo, koma iweyo ukuphwanya lamulolo polamulira kuti andimenye!”

4Anthu amene anayimirira pafupi ndi Paulo anati, “Bwanji ukunyoza mkulu wa ansembe wa Mulungu?”

5Paulo anayankha nati, “Abale, ine sindinazindikire kuti ndi mkulu wa ansembe; pakuti kunalembedwa kuti, ‘Usayankhule zoyipa kwa mtsogoleri wa anthu ako.’ ”

6Paulo atazindikira kuti ena mwa iwo anali Asaduki ndiponso ena anali Afarisi, anafuwula mʼbwalo muja kuti, “Abale anga, ine ndine Mfarisi, mwana wa Mfarisi. Ndikuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo cha kuuka kwa akufa.” 7Iye atanena zimenezi, mkangano unabuka pakati pa Afarisi ndi Asaduki mpaka anthu kugawikana. 8Asaduki amati kulibe kuuka kwa akufa, kulibenso ngakhale angelo kapena mizimu, koma Afarisi amakhulupirira zonsezi.

9Panali phokoso lalikulu, ndipo aphunzitsi ena amalamulo amene anali a gulu la Afarisi anayimirira natsutsa kwambiri. Iwo anati, “Ife sitikupeza cholakwa ndi munthu uyu, chifukwa mwina ndi mzimu kapena mngelo amene wayankhula naye.” 10Mkangano unakula kwambiri kotero kuti mkulu wa asilikali anachita mantha kuti mwina anthu angakhadzule Paulo. Iye analamulira asilikali ake apite kukamuchotsa pakati pawo mwamphamvu ndi kubwera naye ku malo a asilikaliwo.

11Usiku omwewo Ambuye anayimirira pambali pa Paulo nati, “Limba mtima! Monga wandichitira Ine umboni mu Yerusalemu, moteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.”

Ayuda Achita Chiwembu Paulo

12Kutacha Ayuda ena anakonza chiwembu ndipo analumbira kuti sadya kapena kumwa mpaka atapha Paulo. 13Anthu amene anakonza chiwembuchi analipo makumi anayi. 14Iwo anapita kwa akulu a ansembe ndi akuluakulu a Ayuda nakawawuza kuti, “Ife talumbira kolimba kuti sitidya kalikonse mpaka titapha Paulo. 15Tsopano inu pamodzi ndi akuluakulu a Bwalo Lalikulu mupemphe mkulu wa asilikali kuti akubweretsereni Paulo ngati kuti mukufuna kudziwa bwino za mlandu wake. Ife takonzeka kudzamupha asanafike kumeneko.”

16Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo atamva za chiwembuchi, anapita ku malo a asilikali aja namufotokozera Paulo.

17Paulo anayitana mmodzi wa wolamulira asilikali 100 aja, namuwuza kuti, “Pita naye mnyamatayu kwa mkulu wa asilikali. Iyeyu ali ndi mawu oti akamuwuze.” 18Anamutengadi mnyamatayo napita naye kwa mkulu wa asilikali uja, nati, “Wamʼndende uja Paulo anandiyitana, nandipempha kuti ndibweretse mnyamatayu kwa inu chifukwa ali ndi kanthu koti akuwuzeni.”

19Mkulu wa asilikali uja anagwira dzanja mnyamatayo napita naye paseli ndipo anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuti undiwuze chiyani?”

20Mnyamatayo anati, “Ayuda agwirizana zoti akupempheni kuti mawa mubwere ndi Paulo ku Bwalo Lalikulu, ngati kuti akufuna kudziwa bwino za iye. 21Inu musawamvere, chifukwa pali anthu opitirira makumi anayi amene akumudikirira pa njira. Iwo alumbira kuti sadya kapena kumwa mpaka atapha Paulo. Panopa ndi okonzeka kale, akungodikira kuti muwavomere pempho lawo.”

22Mkulu wa asilikaliyo anawuza mnyamatayo kuti apite koma anamuchenjeza kuti, “Usawuze munthu aliyense kuti wandifotokozera zimenezi.”

Paulo Apita ku Kaisareya

23Kenaka mkulu wa asilikaliyo anayitana awiri a asilikali olamulira asilikali 100 nawalamula kuti, “Uzani asilikali 200, asilikali 70 okwera pa akavalo ndi 200 onyamula mikondo kuti akonzeke kupita ku Kaisareya usiku omwe uno nthawi ya 9 koloko. 24Mumukonzerenso Paulo akavalo woti akwerepo kuti akafike bwino kwa bwanamkubwa Felike.”

25Iye analemba kalata iyi:

26Ine Klaudiyo Lusiya,

Kwa wolemekezeka, bwanamkubwa Felike:

Ndikupereka moni.

27Munthuyo Ayuda anamugwira ndipo anali pafupi kumupha, koma ine ndinapita ndi asilikali nʼkukamulanditsa pakuti ndinamva kuti ndi nzika ya Chiroma. 28Ndinkafuna kudziwa mlandu umene anapalamula, choncho ndinapita naye ku Bwalo lawo Lalikulu. 29Ine ndinapeza kuti amamuyimba mlandu wa nkhani ya malamulo awo, koma panalibe mlandu woyenera kumuphera kapena kumuyika mʼndende. 30Nditawuzidwa kuti amukonzera chiwembu munthuyu, ine ndamutumiza kwa inu msanga. Ine ndalamulanso amene akumuyimba mlanduwo kuti abwere kwa inu kudzafotokoza nkhaniyo.

31Pamenepo asilikali aja anatenga Paulo monga anawalamulira napita naye ku Antipatri usiku. 32Mmawa mwake iwo anabwerera ku malo a asilikali nasiya okwera pa akavalo kuti apitirire ndi Paulo. 33Asilikali okwera pa akavalowo atafika ku Kaisareya anapereka kalatayo kwa bwanamkubwa, namuperekanso Paulo. 34Bwanamkubwayo anawerenga kalatayo ndipo anamufunsa Paulo za dera limene amachokera. Atazindikira kuti amachokera ku Kilikiya, 35iye anati, “Ndidzamva mlandu wako okuyimba mlandu akabwera kuno.” Ndipo analamulira kuti asilikali adzimulondera Paulo ku nyumba ya mfumu Herode.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

使徒行传 23:1-35

1保罗注视着公会的人,说:“弟兄们,我在上帝面前行事为人一向问心无愧。” 2大祭司亚拿尼亚一听,就命那些站在旁边的人打保罗的嘴。 3保罗亚拿尼亚说:“你这伪君子23:3 伪君子”希腊文是“粉饰的墙”。,上帝要击打你!你坐在那里不是应当依法审问我吗?你怎么违法叫人打我?”

4站在旁边的人说:“你竟敢辱骂上帝的大祭司?” 5保罗说:“弟兄们,我不知道他是大祭司。我知道圣经上说,‘不可咒诅百姓的官长。’”

6保罗发现他们一些是法利赛人,一些是撒都该人,就在公会中高声说:“弟兄们,我是法利赛人,也是法利赛人的子孙。我因为盼望死人复活,才在这里受审!” 7这句话立刻引起法利赛人和撒都该人之间的争论,公会分成了两派。 8因为撒都该人认为没有复活,也没有天使和灵,而法利赛人认为这些都有。

9众人大声喧嚷,有几个法利赛派的律法教师站起来争辩说:“我们找不出这人有什么错处,也许真的有灵或天使跟他说过话。” 10争论越来越激烈,千夫长怕保罗会被他们扯碎了,就派人把他从人群中救出来,带回军营。

11当天晚上,主站在保罗身旁对他说:“要勇敢!正如你在耶路撒冷为我做了见证,你也必须在罗马为我做见证。”

阴谋杀害保罗

12天亮后,犹太人设下阴谋,并起誓说:“不杀保罗,誓不吃喝!” 13有四十多人参与了这个阴谋。 14他们去见祭司长和长老,说:“我们已经发了誓,不杀保罗不吃饭。 15请你们和公会出面通知千夫长,请他把保罗押到你们这里来,就说要进一步审讯他。我们准备在他到达之前杀掉他!”

16保罗的外甥听到这一阴谋,就去军营通知保罗17保罗请来一位百夫长,说:“请赶快带这青年去见千夫长,他有要事禀告!” 18百夫长领那青年去见千夫长,说:“那囚犯保罗叫我带这青年来,说有要事禀告。”

19千夫长就拉着那青年的手走到一旁,私下问他:“你有什么事要告诉我?” 20他说:“那些犹太人约好了,要请求你明天带保罗到公会受审,假装要详细审问他的事。 21你不要答应他们,因为他们有四十多个人会埋伏在半路,并且还起誓说,‘不杀保罗就不吃不喝’。他们现在已经准备就绪,就等你答应了。”

22千夫长听后,就叫他回去,并叮嘱道:“你向我禀告的事,不要告诉别人。”

保罗被押往凯撒利亚

23于是,千夫长召来两名百夫长,吩咐道:“预备二百名步兵、七十名骑兵、二百名长枪手,今晚九时出发去凯撒利亚24要给保罗预备坐骑,护送他安全抵达腓利斯总督那里。”

25千夫长写了公文给腓利斯总督,内容如下: 26克劳狄·吕西亚敬问腓利斯总督大人安。 27这人被犹太人抓住,险些被他们杀害。我得知他是罗马公民,便带兵去救了他。 28为了弄清楚他们控告他的缘由,我押他到犹太人的公会受审, 29发现他被控告与他们的律法有关,他并没有犯该被监禁或处死的罪。 30我得知有人准备暗杀他,便立即护送他到你那里,并通知他的控告者去你那里告他。”

31军兵奉命行事,连夜护送保罗安提帕底32第二天,由骑兵继续护送,其余军兵返回军营。 33他们到了凯撒利亚,将公文呈交总督,把保罗交给他。 34总督看过公文,便问保罗是哪省的人,得知保罗基利迦人,就说: 35“等告你的人来了,我会审理你的案子。”于是下令把保罗关在希律的王府里。