Machitidwe a Atumwi 14 – CCL & HHH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 14:1-28

Ku Ikoniya

1Ku Ikoniya, Paulo ndi Barnaba analowanso mʼsunagoge ya Ayuda. Kumeneko iwo anaphunzitsa momveka bwino kotero kuti anthu ambiri Achiyuda ndi anthu a mitundu ina anakhulupirira. 2Koma Ayuda amene anakana kukhulupirira anawutsa anthu a mitundu ina nawononga maganizo awo kutsutsana ndi abale. 3Ndipo Paulo ndi Barnaba anakhala kumeneko nthawi yayitali, nalalikira molimba mtima za Ambuye amene anawapatsa mphamvu yochitira zozizwitsa ndi zizindikiro zodabwitsa pochitira umboni mawu a chisomo. 4Anthu a mu mzindamo anagawikana; ena anali mbali ya Ayuda, ena mbali ya atumwi. 5Pamenepo anthu a mitundu ina ndi Ayuda, pamodzi ndi atsogoleri awo anakonza chiwembu choti azunze atumwiwo ndi kuwagenda ndi miyala. 6Koma atazindikira zimenezi, anathawira ku Lusitra ndi Derbe, mizinda ya ku Lukaoniya, ndiponso ku dziko lozungulira mizindayo, 7kumene anapitiriza kulalikira Uthenga Wabwino.

Ku Lusitra ndi ku Derbe

8Ku Lusitra kunali munthu wolumala miyendo, amene sanayendepo chibadwire chake. 9Iyeyu, amamvetsera pamene Paulo amayankhula. Paulo anamuyangʼanitsitsa ndipo anaona kuti anali ndi chikhulupiriro choti achiritsidwe nacho. 10Ndipo Paulo anamuyitana mofuwula nati, “Imirira!” Atamva zimenezi, munthuyo anayimirira, nayamba kuyenda.

11Gulu la anthu litaona zimene Paulo anachitazi, linafuwula mʼChilukaoniya kuti, “Milungu yatitsikira yooneka ngati anthu!” 12Barnaba anamutcha Zeusi ndipo Paulo anamutcha Herimesi chifukwa ndiye amatsogolera kuyankhula. 13Wansembe wa Zeusi amene nyumba yopembedzera Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo, anabweretsa ngʼombe yayimuna yovekedwa nkhata za maluwa pa chipata cha mzindawo chifukwa iyeyo pamodzi ndi anthu ena onse aja amafuna kudzipereka nsembe kwa Paulo ndi Barnaba.

14Koma Barnaba ndi Paulo atamva zimenezi, anangʼamba zovala zawo, nathamangira pakati pa gulu la anthuwo, akufuwula kuti, 15“Anthu inu, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Ife takubweretserani Uthenga Wabwino, kuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo. 16Kale Iye analola anthu a mitundu ina yonse kutsata njira zawozawo. 17Komabe wakhala akudzichitira yekha umboni: Iye amaonetsa kukoma mtima kwake pogwetsa mvula kuchokera kumwamba ndi zipatso pa nyengo yake. Amakupatsani chakudya chambiri ndipo amadzaza mitima yanu ndi chimwemwe.” 18Ngakhale ndi mawu awa, anavutika kuletsa gulu la anthu kuti asapereke nsembe kwa iwo.

19Kenaka kunabwera Ayuda ena kuchokera ku Antiokeya ndi Ikoniya nakopa gulu la anthu lija. Iwo anamugenda miyala Paulo namukokera kunja kwa mzindawo, kuganiza kuti wafa. 20Koma ophunzira atamuzungulira, Pauloyo anayimirira nalowanso mu mzindawo. Mmawa mwake iye ndi Barnaba anachoka ndi kupita ku Derbe.

Paulo ndi Barnaba Abwerera ku Antiokeya wa ku Siriya

21Iwo analalikira Uthenga Wabwino mu mzindawo ndipo anthu ambiri anatembenuka mtima ndi kukhala ophunzira. Kenaka anabwerera ku Lusitra, ku Ikoniya ndi ku Antiokeya. 22Kumeneko analimbikitsa mitima ya ophunzira ndi kuwapatsa mphamvu kuti akhalebe woona mʼchikhulupiriro. Iwo anati, “Ife tiyenera kudutsa mʼmasautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.” 23Paulo ndi Barnaba anasankha akulu ampingo pa mpingo uliwonse, ndipo atapemphera ndi kusala kudya anawapereka kwa Ambuye amene anamukhulupirira. 24Atadutsa Pisidiya, anafika ku Pamfiliya. 25Atalalikira Mawu ku Perga, anapita ku Ataliya.

26Ku Ataliyako, anakwera sitima ya pamadzi kubwerera ku Antiokeya kumene anayitanidwa mwachisomo cha Mulungu kuti agwire ntchito imene tsopano anali atayitsiriza. 27Atangofika ku Antiokeya, anasonkhanitsa pamodzi mpingo ndipo anafotokoza zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo ndiponso mmene Iye anatsekulira a mitundu ina njira ya chikhulupiriro. 28Ndipo anakhala kumeneko ndi ophunzira nthawi yayitali.

Habrit Hakhadasha/Haderekh

מעשי השליחים 14:1-28

1גם באיקניון הלכו פולוס ובר־נבא לבית־הכנסת. הם הטיפו את דבר ה׳ בעוצמה כה רבה, עד שיהודים וגויים רבים האמינו באדון.

2אולם היהודים שדחו את בשורת אלוהים הסעירו את רגשות הגויים, ועוררו בלבם אי־אמון בפולוס ובר־נבא. 3למרות זאת נשארו שם השניים זמן רב למדי, כשהם מבשרים את דבר ה׳ באומץ, ואלוהים אישר שאכן הם שליחיו על־ידי הניסים והנפלאות שחולל באמצעותם. 4תושבי העיר היו חלוקים בדעותיהם: חלקם תמכו במנהיגים היהודים, וחלקם – בפולוס ובר־נבא.

5‏-6כאשר נודע לשני השליחים שהגויים, היהודים ומנהיגיהם תכננו להתנכל להם ולרגום אותם באבנים, מיהרו להימלט על נפשם. הם הגיעו לערי חבל לוקוניה: לוסטרה, דרבי וסביבותיהן, 7וגם שם בישרו את הבשורה. 8בלוסטרה הם ראו אדם שלא התהלך מעולם; רגליו היו משותקות מלידה. 9פולוס שם לב לכך שהנכה מקשיב לדבריו בדריכות ובעניין רב, וכאשר גילה שיש בו אמונה להירפא, 10קרא אליו: ”קום על רגליך!“ כהרף־עין קפץ האיש על רגליו והחל ללכת.

11כשראה קהל הנוכחים את הנס שפולוס חולל, החלו כולם לקרוא בלשון הליקאונית: ”אנשים אלה הם אלים בדמות בני־אדם!“ 12הם החליטו שבר־נבא הוא האל זאוס, ואילו פולוס, שהיה הדובר העיקרי – האל הרמס. 13הכהן של זאוס, שמקדשו היה בפרבר העיר, הביא זרי פרחים ושוורים, כדי להקריבם בשער העיר לעיני ההמונים.

14אולם כאשר הבינו פולוס ובר־נבא את מה שעומד להתרחש, קרעו את בגדיהם ורצו בתוך הקהל בצעקות: 15”אנשים, מה אתם עושים? אנחנו בני־אדם בדיוק כמוכם! באנו לבשר לכם את הבשורה, כדי שאתם תפסיקו לסגוד לאלילים, ובמקום זאת להשתחוות לאלוהים האחד האמיתי, אשר ברא את השמים, את הארץ, את הים ואת כל אשר בם. 16אמנם בימי קדם הרשה ה׳ לגויים לחיות כרצונם, 17אולם הוא תמיד העיד על עצמו במעשיו הטובים ובאהבתו אלינו: הוא שולח לנו, למשל, גשם ותבואות מבורכות; הוא מספק לנו אוכל וממלא את לבנו שמחה.“

18על אף דבריהם אלה הצליחו השניים רק בקושי רב לשכנע את הקהל שלא להקריב להם קורבנות.

19ימים ספורים לאחר מכן הגיעו ללוסטרה יהודים אחדים מאנטיוכיה ומאיקניון, והפכו את קהל המעריצים להמון פרוע וצמא־דם, אשר רגם את פולוס באבנים. ההמונים חשבו שפולוס מת, ולכן גררו אותו אל מחוץ לעיר. 20אולם לאחר שהתקבצו המאמינים סביבו הוא התאושש, קם על רגליו וחזר העירה.

למחרת יצאו פולוס ובר־נבא לדרבי. 21לאחר שבישרו שם את דבר ה׳ ועשו תלמידים רבים, חזרו השניים ללוסטרה, לאיקניון ולאנטיוכיה. 22בערים אלה הם חיזקו את המאמינים, ועודדו אותם לדבוק באמונתם למרות הצרות והרדיפות. ”רק דרך צרות רבות נוכל להיכנס למלכות האלוהים“, הזכירו להם. 23כמו כן מינו פולוס ובר־נבא זקני־קהילה בכל קהילה, ובצום ותפילה הפקידו אותם בידי האלוהים שבו בטחו.

24לאחר מכן המשיכו השניים במסעם חזרה, ועברו דרך פיסידיה ופמפוליה.

25הם הטיפו שוב בפרגי, והמשיכו לאטליה.

26לבסוף הפליגו בספינה לאנטיוכיה – העיר שממנה יצאו למסע, ואשר בה הופקדו בידי אלוהים לבצע את המלאכה שזה עתה סיימו.

27בהגיעם לאנטיוכיה כינסו את כל המאמינים, ומסרו להם דיווח מפורט על מסעם: כיצד ה׳ פעל באמצעותם, וכיצד פתח את שער האמונה גם לגויים. 28פולוס ובר־נבא נשארו עם המאמינים באנטיוכיה זמן ממושך.