Machitidwe a Atumwi 11 – CCL & HHH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 11:1-30

Petro Afotokozera Mpingo

1Atumwi ndi abale a ku Yudeya konse anamva kuti anthu a mitundu ina analandiranso Mawu a Mulungu. 2Tsono Petro atafika ku Yerusalemu, abale amene anali a mdulidwe anamutsutsa iye, 3ndipo anati, “Iwe unalowa mʼnyumba ya anthu osachita mdulidwe ndi kudya nawo.”

4Koma Petro anayamba kuwafotokozera zonse mwatsatanetsatane momwe zinachitikira kuti, 5“Ine ndimapemphera mu mzinda wa Yopa ndipo ndili ngati wokomoka ndinaona masomphenya. Ndinaona chinthu chokhala ngati chinsalu chachikulu chikutsika kuchokera kumwamba chogwiridwa msonga zake zinayi, ndipo chinatsikira pa ine. 6Ine ndinayangʼana mʼkati mwake ndipo ndinaona nyama za miyendo inayi za mʼdziko lapansi, zirombo, zokwawa, ndi mbalame zamlengalenga. 7Kenaka ine ndinamva mawu akuti, ‘Petro, Imirira. Ipha, nudye.’

8“Ine ndinayankha kuti, ‘Ayi, Ambuye! Pakuti chinthu chodetsedwa ndi chonyansa sindinadyepo pakamwa pangapa.’

9“Mawu ochokera kumwamba ananenanso kachiwiri kuti, ‘Chimene Mulungu wachiyeretsa usanene kuti ndi chodetsedwa.’ 10Zimenezi zinachitika katatu ndipo kenaka zonse zinatengedwa kupita kumwamba.

11“Nthawi yomweyo anthu atatu amene anatumidwa kuchokera ku Kaisareya anayima pa nyumba yomwe ndimakhalayo. 12Mzimu anandiwuza kuti ndisakayike, koma ndipite nawo. Abale asanu ndi mmodzi awa anapitanso nane ndipo tinalowa mʼnyumba ya munthuyo. 13Iye anatiwuza mmene anaonera mngelo atayimirira mʼnyumba mwake ndi kumuwuza kuti, ‘Tumiza anthu ku Yopa kuti akayitane Simoni wotchedwa Petro. 14Iye adzakuwuza uthenga umene udzapulumutsa iwe ndi a pa banja ako.’

15“Nditangoyamba kuyankhula, Mzimu Woyera anafika pa iwo monga momwe anafikira pa ife poyamba paja. 16Kenaka ndinakumbukira zimene Ambuye ananena kuti, ‘Yohane anabatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.’ 17Tsono ngati Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyo imene anatipatsa ife, amene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti nditsutsane ndi Mulungu?”

18Iwo atamva zimenezi analibenso chonena ndipo anayamika Mulungu nati, “Potero Mulungu wapatsa anthu a mitundu ina mwayi wotembenuka mtima ndi kulandira moyo.”

Mpingo wa ku Antiokeya

19Tsopano amene anabalalika chifukwa cha mazunzo amene anayamba ataphedwa Stefano, anapita mpaka ku Foinike, ku Kupro ndi ku Antiokeya, ndipo ankalalikira kwa Ayuda okha. 20Komabe, ena pakati pawo ochokera ku Kupro ndi ku Kurene anapita ku Antiokeya ndipo iwo anayamba kuyankhulanso kwa Agriki, nawawuza za Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu. 21Mphamvu ya Ambuye inali nawo ndipo anthu ambiri anakhulupirira natembenukira kwa Ambuye.

22Mbiri imeneyi inamveka ku mpingo wa ku Yerusalemu ndipo iwo anatumiza Barnaba ku Antiokeya. 23Atafika ndi kuona chisomo cha Mulungu pa iwo, anakondwa ndi kuwalimbikitsa anthu onsewo kuti apitirire kukhala woona mu mtima mwa Ambuye. 24Barnabayo anali munthu wabwino, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro ndipo gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Ambuye.

25Kenaka Barnaba anapita ku Tarisisi kukafuna Saulo, 26ndipo pamene anamupeza anabwera naye ku Antiokeya. Barnaba ndi Saulo anasonkhana ndi mpingo kwa chaka chimodzi naphunzitsa anthu ambirimbiri. Okhulupirirawo anayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya.

27Masiku amenewo ku Antiokeya kunafika aneneri ena ochokera ku Yerusalemu. 28Mmodzi wa iwo dzina lake Agabu, anayimirira ndipo Mzimu anamutsogolera kunenera zamʼtsogolo kuti padzakhala njala yayikulu pa dziko lonse lapansi. (Izi zinachitikadi nthawi ya ulamuliro wa Klaudiyo). 29Ophunzirawo, aliyense monga mwakupata kwake, anatsimikiza kuthandiza abale okhala ku Yudeya. 30Izi anazichitadi ndipo anatuma Barnaba ndi Saulo kukapereka mphatsozo kwa akulu a mpingo.

Habrit Hakhadasha/Haderekh

מעשי השליחים 11:1-30

1עד מהרה נודע לשליחים ולשאר האחים ביהודה שגם הגויים נושעים על־ידי האמונה במשיח. 2כשחזר פטרוס לירושלים החלו היהודים המשיחיים למתוח עליו ביקורת.

3”אתה ביקרת בביתם של גויים, ואפילו אכלת איתם!“ טענו.

4ואז סיפר להם פטרוס את הסיפור כולו – מראשיתו ועד סופו:

5”יום אחד בשעה שהתפללתי ביפו ראיתי חזיון: סדין גדול, קשור בארבע קצותיו, הורד מן השמים. 6בתוך הסדין היו כל מיני חיות, זוחלים ועופות טרפים. 7לאחר מכן שמעתי קול מן השמים שקרא: ’קום, פטרוס, שחט ואכול!‘ “

8” ’חס וחלילה, אדוני!‘ עניתי. ’מעולם לא אכלתי אוכל בלתי כשר או טמא!‘

9”אולם אותו קול מן השמים חזר ואמר: ’אם אלוהים אומר שמשהו מסוים טהור, סימן שהוא טהור. אתה אל תקרא לו טמא!‘

10”חזיון זה חזר ונשנה שלוש פעמים, ולאחר מכן הועלה הסדין לשמים. 11באותה שעה הגיעו אל הבית שבו התארחתי שלושה אנשים שנשלחו מקיסריה, 12ורוח הקודש אמר לי ללכת איתם ללא היסוס, למרות היותם גויים! ששת האחים האלה הצטרפו אלי, וכעבור יום הגענו לקיסריה – לביתו של האדם ששלח את השלושה. 13הוא סיפר לנו שמלאך ה׳ נגלה אליו וציווה עליו לשלוח אנשים ליפו, כדי למצוא את שמעון פטרוס. 14’הוא יאמר לך ולבני ביתך כיצד תוכל להיוושע!‘ אמר לו המלאך.

15”כשהתחלתי לבשר להם צלח רוח הקודש על הנאספים, בדיוק כפי שצלח עלינו בתחילה. 16ואז נזכרתי בדברי האדון: ’יוחנן הטביל אתכם במים, אולם עוד זמן־מה תיטבלו ברוח הקודש‘. 17ואם אלוהים נתן לגויים האלה אותה המתנה שנתן לנו, כשהאמנו באדון ישוע המשיח, מי אני שאתווכח אתו?“

18דבריו של פטרוס השביעו את רצונם של היהודים המשיחיים, והם החלו להלל ולשבח את האלוהים. ”כן,“ אמרו, ”גם לגויים העניק אלוהים את הזכות לחזור בתשובה ולקבל חיי נצח!“

19המאמינים אשר נמלטו מירושלים, בעת הרדיפה שהחלה לאחר מותו של סטפנוס, הגיעו בינתיים עד צור וצידון, קפריסין ואנטיוכיה. בכל מקום הם הכריזו על הבשורה, אבל רק ליהודים. 20אך מאמינים אחדים, שנסעו מקפריסין וקוריניה לאנטיוכיה, סיפרו גם לכמה יוונים על האדון ישוע. 21האדון ברך את מאמציהם, וגויים רבים האמינו באדון ישוע.

22כששמעו על כך חברי הקהילה בירושלים, שלחו את בר־נבא לאנטיוכיה כדי לעזור למאמינים החדשים. 23כשהגיע בר־נבא לאנטיוכיה וראה את מעשיו הנפלאים של ה׳, הוא נמלא שמחה רבה ועודד את המאמינים לדבוק באדון בכל מחיר. 24בר־נבא היה אדם טוב לב, מלא רוח הקודש ובעל אמונה חזקה. באותה עת נוספו אנשים רבים לקהל המאמינים.

25לאחר מכן נסע בר־נבא לטרסוס כדי לחפש את שאול, 26וכשמצא אותו, חזר עמו לאנטיוכיה. השניים נשארו באנטיוכיה שנה שלמה ולימדו את המאמינים החדשים והרבים (שם, באנטיוכיה, החלו לכנות את תלמידי ישוע המשיח בשם ”משיחיים“).

27באותה תקופה באו לאנטיוכיה נביאים אחדים מירושלים. 28אחד מהם, אגבוס שמו, קם באחת האספות וניבא, בהשראת רוח הקודש, שרעב כבד יבוא על כל האימפריה הרומאית (נבואתו התגשמה בתקופת שלטונו של קלודיוס). 29משום כך החליטו המאמינים באנטיוכיה לשלוח עזרה כספית לאחיהם ביהודה, כל אחד כפי יכולתו. 30לאחר שאספו את התרומות מסרו אותן לבר־נבא ולשאול, כדי שיביאו אותן לזקני הקהילה בירושלים.