Machitidwe a Atumwi 1 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 1:1-26

Lonjezo la Mzimu Woyera

1Mʼbuku langa loyamba, ndinakulembera iwe Teofilo zonse zimene Yesu anayamba kuchita ndi kuphunzitsa, 2mpaka tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba, mwamphamvu ya Mzimu Woyera, atawalangiza atumwi amene anawasankha. 3Zitatha zowawa zake Yesu anadzionetsa kwa ophunzira ake, ndi kuonetsanso maumboni ambiri kuti anali wamoyo. Iye anadzionetsera kwa iwo ndi kuwaphunzitsa za ufumu wa Mulungu pa masiku makumi anayi. 4Nthawi ina atasonkhana nawo pamodzi, Yesu analamulira ophunzira ake kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate anga analonjeza yomwe ndinakuwuzani. 5Pakuti Yohane anakubatizani ndi madzi, koma posachedwapa inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.”

Yesu Akwera Kumwamba

6Atumwi atasonkhana pamodzi, iwo anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi nthawi ino mubwezeretsa ufumu kwa Israeli?”

7Yesu anawawuza kuti, “Sikofunika kuti mudziwe za nthawi kapena masiku amene Atate ayika mwa ulamuliro wawo. 8Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”

9Atatha kuyankhula zimenezi, Yesu anatengedwa kupita kumwamba ophunzira ake akuona, ndipo anabisika mʼmitambo.

10Yesu akukwera kumwamba, ophunzira ake anayangʼanitsitsa ndi chidwi mʼmitambo. Mwadzidzidzi anaona anthu awiri ovala zoyera atayimirira pambali pawo. 11Iwo anati, “Inu, anthu a ku Galileya, chifukwa chiyani mukuyima ndi kumayangʼana mʼmitambo? Yesu amene wachotsedwa pakati panu ndi kupita kumwamba, adzabweranso mʼnjira yomweyi mwamuona akupita kumwamba.”

Matiyasi Alowa Mʼmalo mwa Yudasi Isikarioti

12Pamenepo atumwi anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku phiri la Olivi, mtunda wosakwana kilomita kuchokera mu mzindamo. 13Atafika mu mzindamo, analowa mʼchipinda chammwamba kumene amakhala. Amene analipo anali awa: Petro, Yohane, Yakobo ndi Andreya; Filipo ndi Tomasi, Bartumeyu ndi Mateyu; Yakobo mwana wa Alifeyo ndi Simoni Zelote ndi Yuda mwana wa Yakobo. 14Onsewa ndi mtima umodzi anapitiriza kupemphera pamodzi ndi amayi, ndi Mariya amayi ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.

15Pa nthawi imeneyo Petro anayimirira pakati pa okhulupirira (gulu la anthu pafupifupi 120). 16Iye anati, “Abale anga, Malemba anayenera kukwaniritsidwa omwe Mzimu Woyera anayankhula kalekale kudzera mwa Davide za Yudasi, amene anatsogolera amene anamugwira Yesu. 17Iye anali mmodzi wa gulu lathu ndipo anatumikira pamodzi ndi ife.”

18(Yudasi anagula munda ndi ndalama zimene anazipeza pochita zoyipa zija; kumeneko, iye anagwa chamutu, naphulika pakati ndipo matumbo ake wonse anakhuthuka. 19Aliyense mu Yerusalemu anamva zimenezi, kotero anatcha mundawo mʼchiyankhulo chawo kuti Akeledama, kutanthauza, Munda wa Magazi).

20Petro anati, “Pakuti kwalembedwa mʼbuku la Masalimo kuti,

“Nyumba yake isanduke bwinja,

ndipo pasakhale wogonamo.

Ndiponso,

“Wina atenge ntchito yake yautsogoleri.

21Chifukwa chake ndi kofunika kusankha mmodzi wa anthu amene akhala nafe nthawi yonse imene Ambuye Yesu ankayenda nafe, 22kuyambira pa nthawi ya ubatizo wa Yohane mpaka nthawi imene Yesu anatengedwa pakati pathu. Pakuti mmodzi wa anthu awa ayenera kukhala mboni pamodzi ndi ife zakuuka kwake.”

23Pamenepo anasankha anthu awiri, Yosefe wotchedwa Barsaba (wodziwikanso kuti Yusto) ndi Matiyasi. 24Kenaka iwo anapemphera nati, “Ambuye mukudziwa mtima wa aliyense. Tionetseni amene mwamusankha mwa awiri awa 25kuti atenge ntchito iyi ya utumwi, imene Yudasi anasiya napita kumalo womuyenera.” 26Tsono anachita maere, ndipo maerewo anagwera Matiyasi. Tsono iye anawonjezedwa pa gulu la atumwi khumi ndi mmodziwo.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

使徒行傳 1:1-26

應許聖靈降臨

1提阿非羅啊,在前一封信中,我從耶穌的生平和教導開始, 2一直談到祂藉著聖靈吩咐了自己選立的使徒,然後被接回天上。 3祂受難後用許多確鑿的證據證實自己活著,在四十天之內屢次向使徒顯現,與他們談論上帝的國。 4有一次,耶穌和他們在一起吃飯的時候,叮囑他們:「你們不要離開耶路撒冷,要在那裡等候我對你們說過的天父的應許。 5因為從前約翰用水給你們施洗,但再過幾天,你們要受聖靈的洗。」

6他們跟耶穌在一起的時候問祂:「主啊,你要在這時候復興以色列國嗎?」 7耶穌回答說:「天父照祂的權柄定下的時間、日期不是你們可以知道的。 8但聖靈降臨在你們身上後,你們必得到能力,在耶路撒冷猶太全境和撒瑪利亞,直到地極,作我的見證人。」

9耶穌說完這番話,就在他們眼前被提升天,被一朵雲彩接去,離開了他們的視線。 10祂上升時,他們都定睛望著天空,忽然有兩個身穿白衣的人站在他們身旁, 11說:「加利利人啊!你們為什麼站在這裡望著天空呢?這位離開你們被接到天上的耶穌,你們看見祂怎樣升天,將來祂還要怎樣回來。」

選立新使徒

12於是,他們從橄欖山回到耶路撒冷。橄欖山距離耶路撒冷不遠,約是安息日允許走的路程1·12 按猶太人的傳統,在安息日只能走約一公里遠。13他們進城後,來到樓上自己住的房間。當時有彼得約翰雅各安得烈腓力多馬巴多羅買馬太亞勒腓的兒子雅各、激進黨人西門雅各的兒子猶大14他們和耶穌的母親瑪麗亞、耶穌的弟弟們及幾個婦女在一起同心合意地恆切禱告。

15那時,約有一百二十人在聚會,彼得站起來說: 16「弟兄們,關於帶人抓耶穌的猶大,聖靈藉著大衛的口早已預言,這經文必須要應驗。 17這人原本是我們中間的一員,與我們同擔使徒的職分。」

18猶大用作惡得來的錢買了一塊田,他頭朝下栽倒在那裡,肚破腸流。 19這消息很快傳遍了耶路撒冷,當地人稱那塊田為「亞革大馬」,就是「血田」的意思。

20彼得繼續說:「詩篇上寫道,『願他的家園一片荒涼,無人居住』,又說,『願別人取代他的職位。』 21-22所以,我們必須另選一個人代替猶大,與我們一同為主耶穌的復活做見證。他必須是從主耶穌接受約翰的洗禮起一直到主升天,始終與我們在一起的人。」

23被提名的有別號巴撒巴又叫猶士都約瑟馬提亞兩個人。 24-25大家便禱告說:「主啊!你洞悉人的內心,求你指明這兩個人中你要揀選哪一個來擔負使徒的職分。猶大丟棄了這職分,去了他該去的地方。」 26然後,他們抽籤,抽中了馬提亞,就把他列入十一使徒中。