Luka 3 – CCL & HOF

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 3:1-38

Yohane Mʼbatizi Akonza Njira

1Mʼchaka cha 15 mu ulamuliro wa Tiberiyo Kaisara, Pontiyo Pilato ali bwanamkubwa wa Yudeya, Herode ankalamulira ku Galileya, mʼbale wake Filipo ankalamulira ku Iturea ndi ku dera la Trakoniti, ndipo Lusaniyo ankalamulira ku Abilene. 2Inalinso nthawi ya mkulu wa ansembe wa Anasi ndi Kayafa, pamene mawu a Mulungu anabwera kwa Yohane mwana wa Zakariya mʼchipululu. 3Iye anapita ku dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yorodani, nalalikira ubatizo wa kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo. 4Monga analembera mʼbuku la Yesaya mneneri kuti:

“Mawu a wofuwula mʼchipululu,

konzani njira ya Ambuye,

wongolani njira zake.

5Chigwa chilichonse chidzadzazidwa

ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzasalazidwa,

misewu yokhotakhota idzawongoledwa,

ndi njira zosasalala zidzasalazidwa.

6Ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.”

7Yohane anati kwa magulu a anthu amene amabwera kudzabatizidwa ndi iye, “Ana anjoka inu! Anakuchenjezani ndani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwera? 8Onetsani zipatso zakutembenuka mtima, ndipo musamanene mwa inu nokha kuti, ‘Tili nalo kholo lathu Abrahamu,’ pakuti ndikuwuzani kuti kuchokera ku miyala iyi, Mulungu akhoza kumuwutsira Abrahamuyo ana. 9Nkhwangwa ili kale pa muzu wamitengo, ndipo mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino udzadulidwa ndi kuponyedwa pa moto.”

10Gulu la anthuwo linafunsa kuti, “Nanga tsono tichite chiyani?”

11Yohane anayankha kuti, “Munthu amene ali ndi malaya awiri apatseko amene alibe, ndi amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi.”

12Amisonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa. Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, ife tichite chiyani?”

13Iye anawawuza kuti, “Musalandire moposa zimene muyenera.” 14Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?”

Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.”

15Anthu ankadikira ndi chiyembekezo ndipo ankasinkhasinkha mʼmitima mwawo kuti mwina Yohane nʼkukhala Khristu. 16Yohane anayankha onse kuti, “Ine ndikubatizani ndi madzi. Koma wina wondiposa ine mphamvu adzabwera amene sindili woyenera kumasula lamba wa nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto. 17Mʼdzanja lake muli chopetera kuti ayeretse powomberapo tirigu ndi kusonkhanitsa tirigu ndipo adzatentha zotsalira zonse ndi moto wosazimitsika.” 18Ndipo ndi mawu ena ambiri, Yohane anawachenjeza anthu ndi kuwalalikira Uthenga Wabwino.

19Koma pamene Yohane anadzudzula Herode wolamulirayo chifukwa chokwatira Herodia, mkazi wa mʼbale wake, ndi zoyipa zina zonse anazichita, 20Herode anawonjezanso choyipa ichi pa zonsezo: Anatsekera Yohane mʼndende.

Ubatizo wa Yesu

21Pamene anthu onse ankabatizidwa, Yesu anabatizidwanso. Ndipo akupemphera, kumwamba kunatsekuka. 22Mzimu Woyera anatsika pa Iye mumaonekedwe a nkhunda ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.”

Makolo a Yesu

23Ndipo Yesu anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ntchito yake. Monga mmene anthu ankaganizira, Iyeyo anali mwana wa Yosefe,

mwana wa Heli, 24mwana wa Matate,

mwana wa Levi, mwana wa Meliki,

mwana wa Yaneyi, mwana wa Yosefe

25mwana wa Matati, mwana wa Amosi,

mwana wa Naomi, mwana wa Esli,

mwana wa Nagai, 26mwana wa Maati,

mwana wa Matatiyo, mwana wa Simeoni,

mwana wa Yosefe, mwana wa Yoda

27mwana wa Yohanani, mwana wa Resa,

mwana wa Zerubabeli, mwana wa Salatieli,

mwana wa Neri, 28mwana wa Meliki,

mwana wa Adi, mwana wa Kosamu,

mwana wa Elmadama, mwana wa Ere,

29mwana wa Jose, mwana wa Eliezara,

mwana wa Yorimu, mwana wa Matati,

mwana wa Levi, 30mwana wa Simeoni,

mwana wa Yuda, mwana wa Yosefe,

mwana wa Yonamu, mwana wa Eliakimu,

31mwana wa Meleya, mwana wa Mena,

mwana wa Matata, mwana wa Natani,

mwana wa Davide, 32mwana wa Yese,

mwana wa Obedi, mwana wa Bowazi,

mwana wa Salimoni, mwana wa Naasoni,

33mwana wa Aminadabu, mwana wa Arni,

mwana wa Hezronu, mwana wa Perezi,

mwana wa Yuda, 34mwana wa Yakobo,

mwana wa Isake, mwana wa Abrahamu,

mwana wa Tera, mwana wa Nakoro,

35mwana wa Serugi, mwana wa Reu,

mwana wa Pelegi, mwana wa Eberi,

mwana wa Sela, 36mwana wa Kainane,

mwana wa Arfaksadi, mwana wa Semu,

mwana wa Nowa, mwana wa Lameki,

37mwana wa Metusela, mwana wa Enoki,

mwana wa Yaredi mwana wa Malaleeli,

mwana wa Kainane, 38mwana wa Enosi,

mwana wa Seti,

mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.

Hoffnung für Alle

Lukas 3:1-38

Jesus wird für seinen Dienst vorbereitet

(Kapitel 3,1–4,13)

Johannes der Täufer ruft: »Kehrt um zu Gott!«

(Matthäus 3,1‒12; Markus 1,1‒8)

1Es war im 15. Regierungsjahr von Kaiser Tiberius. Pontius Pilatus verwaltete als Statthalter die Provinz Judäa; Herodes3,1 Es handelt sich um Herodes Antipas. Vgl. »Herodes« im Biblischen Personen- und Ortsverzeichnis. herrschte über Galiläa, sein Bruder Philippus über Ituräa und Trachonitis, und Lysanias regierte in Abilene; 2Hannas und später Kaiphas waren die Hohenpriester. In dieser Zeit sprach Gott zu Johannes, dem Sohn von Zacharias, der in der Wüste lebte.

3Da machte sich Johannes auf den Weg und zog durch das ganze Gebiet am Jordan. Überall forderte er die Leute auf: »Kehrt um zu Gott und lasst euch von mir taufen! Dann wird er euch eure Sünden vergeben.«3,3 Wörtlich: Dabei verkündete er die Taufe der Umkehr zur Vergebung der Sünden. 4So erfüllte sich, was im Buch des Propheten Jesaja steht:

»Jemand ruft in der Wüste: ›Macht den Weg frei für den Herrn! Räumt alle Hindernisse weg! 5Jedes Tal soll aufgefüllt, jeder Berg und Hügel abgetragen werden, krumme Wege sollen begradigt und holprige Wege eben werden! 6Dann werden alle Menschen sehen, wie Gott Rettung bringt!‹«3,6 Jesaja 40,3‒5

7Die Menschen kamen in Scharen zu Johannes, um sich von ihm taufen zu lassen. Aber er hielt ihnen entgegen: »Ihr Schlangenbrut! Wer hat euch auf den Gedanken gebracht, ihr könntet dem kommenden Gericht Gottes entrinnen? 8Zeigt durch Taten, dass ihr wirklich zu Gott umkehren wollt! Bildet euch nur nicht ein, ihr könntet euch damit herausreden: ›Abraham ist unser Vater!‹ Ich sage euch: Gott kann selbst aus diesen Steinen hier Nachkommen für Abraham hervorbringen.

9Schon ist die Axt erhoben, um die Bäume an der Wurzel abzuschlagen. Jeder Baum, der keine guten Früchte bringt, wird umgehauen und ins Feuer geworfen.«

10Da wollten die Leute wissen: »Was sollen wir denn tun?« 11Johannes antwortete: »Wer zwei Hemden hat, soll dem eins geben, der keins besitzt. Und wer etwas zu essen hat, soll seine Mahlzeit mit den Hungrigen teilen.«

12Es kamen auch Zolleinnehmer, die sich taufen lassen wollten. Sie fragten: »Lehrer, und wir? Wie sollen wir uns verhalten?« 13Johannes wies sie an: »Verlangt nur so viel Zollgebühren, wie ihr fordern dürft!«

14»Und was sollen wir tun?«, erkundigten sich einige Soldaten. »Plündert nicht und erpresst niemand! Seid zufrieden mit eurem Sold«, antwortete ihnen Johannes.

15Die Leute ahnten, dass bald etwas geschehen würde, und alle fragten sich, ob nicht Johannes der Christus, der ersehnte Retter, sei. 16Doch Johannes erklärte öffentlich: »Ich taufe euch mit Wasser, aber nach mir wird ein anderer kommen, der viel mächtiger ist als ich. Ich bin nicht einmal würdig, ihm die Schuhe auszuziehen3,16 Das Ausziehen und Nachtragen der Schuhe gehörte zu den Aufgaben eines Sklaven für seinen Herrn.. Er wird euch mit dem Heiligen Geist und mit Feuer taufen.3,16 Es ist nicht klar, ob Johannes hier von zwei unterschiedlichen Taufen spricht (einer Taufe mit dem Heiligen Geist und einer Taufe mit dem Feuer des Gerichts) oder ob es um eine einzige Taufe geht und das Feuer ein Bild für das reinigende Wirken des Heiligen Geistes ist.

17Er hat schon die Schaufel in seiner Hand, mit der er die Spreu vom Weizen trennt. Den Weizen wird er in seine Scheune bringen, die Spreu aber wird er in einem Feuer verbrennen, das nie verlöscht.«

18So verkündete Johannes den Menschen die rettende Botschaft Gottes und ermahnte sie darüber hinaus mit vielen anderen Worten. 19Auch Herodes, den Herrscher von Galiläa, wies er scharf zurecht. Denn dieser lebte mit Herodias, der Frau seines Bruders, zusammen. Er schreckte vor keinem Verbrechen zurück. 20Am Ende ging er so weit, dass er Johannes ins Gefängnis werfen ließ.

Jesus lässt sich taufen

(Matthäus 3,13‒17; Markus 1,9‒11; Johannes 1,32)

21Als Johannes wieder einmal viele Menschen taufte, kam auch Jesus und ließ sich taufen. Während er betete, öffnete sich der Himmel, 22und der Heilige Geist kam wie eine Taube sichtbar auf ihn herab. Gleichzeitig sprach eine Stimme vom Himmel: »Du bist mein geliebter Sohn, über den ich mich von Herzen freue.«

Von Adam bis Jesus

(Matthäus 1,1‒17)

23Jesus trat zum ersten Mal öffentlich auf, als er ungefähr 30 Jahre alt war. Die Leute kannten ihn als den Sohn von Josef. Josefs Vater war Eli, und dessen Vorfahren waren:

24Mattat – Levi – Melchi – Jannai – Josef –

25Mattitja – Amos – Nahum – Hesli – Naggai –

26Mahat – Mattitja – Schimi – Josech – Joda –

27Johanan – Resa – Serubbabel – Schealtiël – Neri –

28Melchi – Addi – Kosam – Elmadam – Er –

29Joschua – Eliëser – Jorim – Mattat – Levi –

30Simeon – Juda – Josef – Jonam – Eljakim –

31Melea – Menna – Mattata – Nathan – David –

32Isai – Obed – Boas – Salmon – Nachschon –

33Amminadab – Admin – Arni – Hezron – Perez – Juda –

34Jakob – Isaak – Abraham – Terach – Nahor –

35Serug – Regu – Peleg – Eber – Schelach –

36Kenan – Arpachschad – Sem – Noah – Lamech –

37Metuschelach – Henoch – Jered – Mahalalel – Kenan –

38Enosch – Set – Adam – und dieser stammte von Gott.