Levitiko 9 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 9:1-24

Ansembe Ayamba Kutumikira

1Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Mose anayitana Aaroni, ana ake ndi akuluakulu a Aisraeli. 2Ndipo anawuza Aaroni kuti, “Tenga mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yako yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza. Zonsezi zikhale zopanda chilema ndipo uzipereke pamaso pa Yehova. 3Kenaka uwawuze Aisraeli kuti, ‘Tengani mbuzi yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Mutengenso mwana wangʼombe ndi mwana wankhosa. Zonsezi zikhale za chaka chimodzi ndi zopanda chilema kuti zikhale nsembe yopsereza. 4Mutengenso ngʼombe yayimuna ndi nkhosa yayimuna kuti zikhale nsembe yachiyanjano zoti ziperekedwe pamaso pa Yehova. Pamodzi ndi izi mubwerenso ndi nsembe yachakudya yosakaniza ndi mafuta pakuti lero Yehova akuonekerani.’ ”

5Anthu anatenga zonse zimene Mose analamula nabwera nazo pa khomo la tenti ya msonkhano. Gululo linasendera pafupi ndi kuyima pamaso pa Yehova. 6Tsono Mose anati, “Izi ndi zimene Yehova walamula kuti muchite kuti ulemerero wa Yehova ukuonekereni.”

7Pambuyo pake Mose anawuza Aaroni kuti, “Sendera pafupi ndi guwa ndipo upereka nsembe yako yopepesera machimo ndi nsembe yako yopsereza ndikuchita mwambo wopepesera machimo ako ndi machimo a anthu. Anthuwa apereke nsembe zawo zopepesera machimo monga momwe Yehova walamulira.”

8Choncho Aaroni anasendera pafupi ndi guwa, napha mwana wangʼombe uja kukhala nsembe yake yopepesera machimo. 9Ana a Aaroni anabwera ndi magazi kwa Aaroni ndipo iye anaviyika chala chake mʼmagaziwo, nawapaka pa nyanga za guwa. Magazi wotsalawo anawathira pa tsinde la guwalo. 10Kenaka anatentha paguwapo, mafuta, impsyo pamodzi ndi mafuta amene amakuta chiwindi ngati nsembe yopepesera machimoyo, monga momwe Yehova analamulira Mose. 11Koma nyama ndi chikopa anazitenthera kunja kwa msasa.

12Kenaka anapha nsembe yopsereza. Ana a Aaroni atabwera ndi magazi kwa iye, Aaroniyo anawawaza mbali zonse za guwa. 13Ana akewo anamupatsa nyama yoduladula ya nsembe yopsereza ija pamodzi ndi mutu ndipo anazitentha pa guwa. 14Aaroni anatsuka matumbo ndi miyendo nazitentha pa guwa pamodzi ndi nsembe yopsereza ija.

15Kenaka Aaroni anapereka zopereka za anthuwo. Anatenga mbuzi yopepesera machimo a anthuwo, yopereka chifukwa cha tchimo, nayipha ndi kuyipereka kuti ikhale yopepesera machimo monga anachitira ndi nsembe yoyamba ija.

16Anabwera ndi nsembe yopsereza, nayipereka potsata mwambo wake. 17Anabweranso ndi chopereka cha chakudya. Anatapa ufa dzanja limodzi ndi kutentha pa guwa, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya mmawa ija.

18Tsono Aaroni anapha ngʼombe ndi nkhosa yayimuna monga nsembe yachiyanjano ya anthu. Ana ake anamupatsira magazi ndipo anawawaza mbali zonse za guwa. 19Anamupatsiranso mafuta a ngʼombeyo ndi nkhosa yayimunayo: mchira wamafuta, mafuta wokuta matumbo, impsyo ndi mafuta wokuta chiwindi. 20Ana a Aaroni anayika mafutawo pa zidale. Pambuyo pake Aaroni anatentha mafutawo pa guwa lansembe. 21Koma zidale ndi ntchafu ya kumanja Aaroni anaziweyula ngati chopereka choweyula pamaso pa Yehova.

22Kenaka Aaroni anakweza manja ake pa anthuwo nawadalitsa. Ndipo atatha kupereka nsembe yopepesera machimo, nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano, anatsika pa guwapo.

23Ndipo Mose pamodzi ndi Aaroni analowa mu tenti ya msonkhano. Atatulukamo anadalitsa anthuwo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse. 24Pomwepo moto unatuluka pamaso pa Yehova niwutentha nsembe zopsereza ndi mafuta zimene zinali pa guwa. Anthu onse ataona zimenezi anafuwula mwachimwemwe ndipo anaweramitsa nkhope zawo pansi.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

利未記 9:1-24

亞倫獻祭

1第八天,摩西召來亞倫父子們和以色列的眾長老。 2他對亞倫說:「你要在耶和華面前獻上一頭公牛犢作贖罪祭、一隻公綿羊作燔祭,這些祭牲都要毫無殘疾。 3然後,你要告訴以色列人,『你們要取一隻公山羊作贖罪祭、毫無殘疾的一歲牛犢和羊羔各一隻作燔祭、 4公牛和公綿羊各一隻作平安祭,連同調油的素祭一起獻給耶和華,因為今天耶和華要向你們顯現。』」 5於是,以色列人遵照摩西的吩咐,把祭物帶到會幕前。全體會眾都聚集到那裡,站在耶和華面前。 6摩西對他們說:「耶和華吩咐你們這樣做,是為了向你們顯出祂的榮耀。」 7隨後,摩西亞倫說:「你要到壇前來,獻上你的贖罪祭和燔祭,為自己和民眾贖罪。也要按照耶和華的吩咐,為百姓獻上他們的祭物,為他們贖罪。」

8於是,亞倫走到壇前,宰殺為他作贖罪祭的牛犢。 9他兒子們把牛犢的血遞給他,他用手指蘸血抹在壇角上,將剩下的血倒在壇腳旁。 10他照耶和華對摩西的吩咐,在壇上焚燒牛犢的脂肪、腎臟和肝葉, 11把皮和肉帶到營外焚燒。

12亞倫宰了燔祭祭牲,他兒子們把祭牲的血遞給他灑在祭壇四周。 13他們將祭牲切成塊,連頭顱一起交給亞倫獻在壇上焚燒。 14亞倫洗淨祭牲的內臟和腿,放在祭壇的燔祭上焚燒。

15隨後,亞倫為民眾獻祭。他牽來那隻為民眾作贖罪祭的公山羊,宰殺後,像剛才為自己獻贖罪祭一樣為他們獻上贖罪祭。 16他又牽來燔祭祭牲,依照條例獻上燔祭。 17除了早晨的燔祭,亞倫又取來素祭,從中拿了一把獻在壇上焚燒。 18然後,他宰了公牛和公綿羊,為民眾獻平安祭。他兒子們把祭牲的血遞給他,他把血灑在祭壇四周。 19他們把公牛和公綿羊的脂肪,即肥尾巴、遮蓋內臟的脂肪、腎臟和肝葉, 20放在祭牲的胸上,然後亞倫把那些脂肪放在壇上焚燒, 21將胸肉和右腿肉作為搖祭在耶和華面前搖一搖,都遵照摩西的吩咐。

22亞倫獻完贖罪祭、燔祭和平安祭,舉手為民眾祝福後,走下祭壇。 23之後,摩西亞倫走進會幕,又出來為民眾祝福。這時,耶和華的榮耀向所有民眾顯現。 24有火從耶和華那裡降下來,燒盡祭壇上的燔祭和脂肪。民眾看見這景象,都歡呼起來,俯伏在地。