Levitiko 8 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 8:1-36

Mwambo Wodzoza Aaroni ndi Ana Ake

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Tenga Aaroni ndi ana ake, zovala zawo, mafuta wodzozera, ngʼombe yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, nkhosa ziwiri zazimuna ndi dengu la buledi wopanda yisiti, 3ndipo usonkhanitse gulu la anthu pa khomo la tenti ya msonkhano.” 4Mose anachita zomwe Yehova anamulamula ndipo gulu la anthu linasonkhana pa khomo la tenti ya msonkhano.

5Mose anawuza gulu la anthuwo kuti, “Izi ndi zimene Yehova walamulira kuti zichitike.” 6Pamenepo Mose anabwera ndi Aaroni ndi ana ake nawasambitsa ndi madzi. 7Anamuveka Aaroni mwinjiro, ndi kumumanga lamba mʼchiwuno. Anamuvekanso mkanjo wa efodi ndi efodiyo. Anamangira lamba efodiyo amene analukidwa mwaluso uja, motero efodiyo analimba mʼchiwunomo. 8Anamuvekanso chovala chapachifuwa ndipo mʼchovalacho anayikamo Urimu ndi Tumimu. 9Kenaka anamuveka Aaroniyo nduwira kumutu ndipo patsogolo pa nduwirayo anayikapo duwa lagolide, chizindikiro chopatulika monga momwe Yehova analamulira Mose.

10Pamenepo Mose anatenga mafuta wodzozera nadzoza tenti ya msonkhano pamodzi ndi zonse zimene zinali mʼmenemo, ndipo potero anazipatula. 11Anawaza mafuta ena pa guwa kasanu ndi kawiri, nalidzoza guwalo pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Anadzozanso beseni ndi tsinde lake, nazipatula. 12Anathira mafuta wodzozera ena pamutu pa Aaroni ndipo anamudzoza ndi kumupatula. 13Kenaka anabwera ndi ana a Aaroni. Anawaveka minjiro, ndi kuwamanga malamba mʼchiwuno ndi kuwaveka nduwira kumutu monga momwe Yehova analamulira Mose.

14Kenaka Mose anabwera ndi ngʼombe yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, ndipo Aaroni ndi ana ake anasanjika manja awo pamutu pa ngʼombeyo. 15Mose anapha ngʼombeyo, ndi kutenga magazi ena angʼombeyo ndi kupaka ndi chala chake pa nyanga zaguwa lansembe, naliyeretsa. Magazi otsalawo anawakhuthulira pa tsinde laguwalo. Motero anachita mwambo wopepesera machimo. 16Mose anatenganso mafuta onse okuta matumbo, mafuta ophimba chiwindi, ndiponso impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta ake, nazitentha pa guwapo. 17Koma nyama yangʼombeyo, chikopa chake ndi matumbo ake anaziwotcha kunja kwa msasa monga momwe Yehova analamulira Mose.

18Kenaka anabwera ndi nkhosa yayimuna ya nsembe yopsereza, ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna anasanjika manja awo pamutu pake. 19Ndipo Mose anapha nkhosayo ndi kuwaza magazi ake mbali zonse zaguwalo. 20Anayidula nkhosayo nthulinthuli ndipo anatentha mutu wake, nthulizo ndi mafuta. 21Anatsuka matumbo ake ndi miyendo yake, ndi kutentha nkhosa yonseyo pa guwa lansembe kuti ikhale nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yachakudya yoperekedwa kwa Yehova monga Yehovayo analamulira Mose.

22Kenaka Mose anapereka nkhosa yayimuna ina pamwambo wodzoza ansembe, ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna anasanjika manja awo pamutu pake. 23Mose anayipha nkhosayo ndipo anatenga magazi ake ena ndi kupaka ndewere za khutu la kudzanja lamanja la Aaroni, pa chala chake chachikulu cha kudzanja lamanja, ndi pa chala chake chachikulu cha phazi lakumanja. 24Pambuyo pake Mose anabwera ndi ana aamuna a Aaroni ndi kupaka magazi pa ndewere za makutu awo akumanja, pa zala zawo zazikulu za dzanja lamanja, ndiponso pa zala zawo zazikulu za kuphazi lakumanja. Kenaka iye anawaza magazi otsalawo mbali zonse za guwalo. 25Anatenganso mafuta ake, mafuta a ku mchira wake, mafuta okuta matumbo, mafuta okuta chiwindi, impsyo zonse ziwiri ndi mafuta ake ndiponso ntchafu yakumanja. 26Ndipo mʼdengu la buledi wopanda yisiti limene linali pamaso pa Yehova, anatengamo buledi mmodzi, buledi mmodzi wokhala ndi mafuta a olivi, ndi buledi wopyapyala mmodzi. Zonsezi anaziyika pa mafuta aja ndi pa ntchafu ya ku dzanja lamanja ija. 27Mose anapereka zonsezi mʼmanja mwa Aaroni ndi ana ake amene anazipereka kwa Yehova kuti zikhale nsembe yoweyula. 28Kenaka Mose anazitenga mʼmanja mwawo ndipo anazipsereza pa guwa lansembe pamwamba penipeni pamodzi ndi nsembe yopsereza ija kuti ikhale nsembe yopereka pamwambo wodzoza ansembe, kuti ipereke fungo lokoma, chopereka chachakudya kwa Yehova. 29Mose anatenga chidale cha nkhosa yayimuna, chomwe ndi gawo lake pamwambo wodzoza ansembe, ndipo anachiweyula pamaso pa Yehova kuti chikhale nsembe yoweyula monga momwe Yehova analamulira Mose.

30Kenaka Mose anatenga mafuta wodzozera ansembe ndi magazi amene anali pa guwa nawaza pa Aaroni ndi zovala zake ndiponso ana ake aja ndi zovala zawo. Motero Mose anapatula Aaroni ndi zovala zake, ndiponso ana ake ndi zovala zawo.

31Mose anawuza Aaroni ndi ana ake kuti, “Phikani nyamayo pa khomo la tenti ya msonkhano, ndipo mudyere pomwepo pamodzi ndi buledi amene ali mʼdengu la zopereka za pamwambo wodzoza ansembe monga Yehova analamulira kuti, ‘Aaroni ndi ana ake azidya zimenezi.’ 32Ndipo nyama ndi buledi zotsalazo, muziwotche. 33Musatuluke kunja kwa tenti ya msonkhano kwa masiku asanu ndi awiri mpaka masiku amwambo wokudzozani unsembe atatha, pakuti mwambowu ndi wa masiku asanu ndi awiri. 34Zimene zachitika lerozi analamula ndi Yehova kuti zichitike ngati nsembe yopepesera machimo anu. 35Muzikhala pa khomo la tenti ya msonkhano usana ndi usiku kwa masiku asanu ndi awiri. Ndipo muzichita zimene Yehova wakulamulani kuti musafe, pakuti zimenezi ndi zomwe Yehova wandilamulira.” 36Choncho Aaroni ndi ana ake anachita zonse zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.