Levitiko 5 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 5:1-19

1“ ‘Ngati munthu anayitanidwa ku bwalo kuti akachitire umboni pa zimene anaziona kapena kuzimva koma iye nʼkukana kuchitira umboni, munthu ameneyo wachimwa ndipo ayenera kulangidwa.

2“ ‘Munthu akakhudza chinthu chilichonse chodetsedwa, monga nyama yakufa ya mʼthengo, kapena chiweto chakufa kapenanso chokwawa chakufa, ngakhale iyeyo wachikhudza mosadziwa, wasanduka wodetsedwa ndipo wachimwa.

3“ ‘Munthu akakhudza choyipitsa munthu cha mtundu uliwonse, ndipo pochikhudzapo ndi kuyipitsidwa nacho mosadziwa, munthuyo adzakhala wopalamula akangodziwa chimene wachitacho.

4“ ‘Munthu akalumbira mofulumira kapena mosasamala kuti adzachita chinthu, choyipa kapena chabwino, ngakhale kuti wachita izi mosadziwa kuti nʼkulakwa, pamene wazindira kulakwa kwake, iye adzakhalabe wopalamula akangodziwa chimene wachitacho.

5“ ‘Pamene munthu wazindikira kuti wachimwa motere, awulule tchimo limene wachitalo. 6Pambuyo pake, munthuyo abwere kwa Yehova ndi mwana wankhosa wamkazi kapena mbuzi kuti ikhale chopereka chopepesera tchimo ndipo wansembe achite mwambo wopepesera tchimo lomwe wachitalo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo.

7“ ‘Ngati munthuyo alibe mwana wankhosa, abweretse njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri kwa Yehova ngati chopereka chopepesera tchimo lake. Imodzi ikhale nsembe yopepesera tchimo, ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza. 8Tsono abwere nazo kwa wansembe, ndipo wansembeyo ayambe wapereka mbalame imodzi ngati yopepesera tchimo. Apotole khosi koma osayidula mutu, 9kenaka awaze magazi a chopereka chopepesera tchimocho mʼmbali mwa guwa. Magazi ena onse awathire pa tsinde la guwa. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo. 10Pambuyo pake wansembe apereke mbalame inayo kuti ikhale chopereka chopsereza potsata mwambo wake. Wansembe atatha kupereka nsembe yopepesera tchimo limene munthu uja wachita, wochimwayo adzakhululukidwa.

11“ ‘Koma ngati munthuyo alibe njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri, abweretse ufa wosalala wokwanira kilogalamu imodzi kuti ukhale chopereka chopepesera tchimo limene wachita. Asathiremo mafuta kapena lubani chifukwa ndi chopereka chopepesera tchimo. 12Abweretse ufawo kwa wansembe ndipo wansembeyo atapeko dzanja limodzi kuti ukhale ufa wachikumbutso ndi kuwutentha pa guwa pamodzi ndi chopereka chopsereza kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo. 13Umu ndi mmene wansembe adzachitire mwambo wopepesera machimo ena aliwonse amene munthu wachita, ndipo munthuyo adzakhululukidwa. Zopereka zonse zotsala zidzakhala za wansembeyo monga momwe amachitira ndi chopereka chachakudya.’ ”

Chopereka Chopepesera Kupalamula

14Yehova anawuza Mose kuti, 15“Munthu akachita zinthu mosakhulupirika, nachimwa mosadziwa posapereka zinthu zopatulika zofunika kwa Yehova, munthuyo apereke kwa Yehova nsembe yopepesera machimo ake. Nsembeyo ikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake ukhale wokwana masekeli oyenera a siliva pakawerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu. Imeneyi ndi nsembe yopepesera kupalamula. 16Munthuyo ayenera kubweza zinthu zopatulika zimene sanaperekezo. Awonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse ndi kuzipereka zonsezo kwa wansembe amene adzachita mwambo wopepesera machimo a munthuyo, popereka nkhosa yayimuna ija ngati nsembe yopepesera ndipo wochimwayo adzakhululukidwa.

17“Ngati munthu wachimwa mosadziwa pochita chilichonse chimene Yehova salola, munthuyo ndi wopalamula ndithu, ndipo ayenera kulangidwa. 18Abwere kwa wansembe ndi chopereka chopepesera kupalamula kwake. Chopereka chikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake ukhale woyenera nsembe yopepesera kupalamula kumene anachimwa mosadziwako, ndipo munthuyo adzakhululukidwa. 19Imeneyi ndi nsembe yopepesera kupalamula popeza munthuyo wapezeka wolakwa pamaso pa Yehova.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

利未记 5:1-19

1“如果有人当庭作证,却不肯把自己所知所见的说出来,就是犯罪,要担负罪责。 2如果有人接触了不洁净之物,如野兽的尸体、家畜的尸体或爬虫的尸体,即使无意也已不洁净,是有罪的。 3如果有人无意中接触了别人的不洁之物,当他意识到后,就有罪了。 4如果有人草率起誓,不论出于善意还是恶意,即使当初没有察觉,后来才意识到,也是有罪的。 5如果有人犯了以上任何一种罪,就必须认罪。 6为了赎过,他必须献给耶和华一只母绵羊或母山羊作赎罪祭。祭司要为他赎罪。

7“他若献不起羊,就要献给耶和华两只斑鸠或两只雏鸽,一只作赎罪祭,一只作燔祭。 8他要把它们带到祭司那里,祭司要先用一只鸟献赎罪祭,要扭断鸟脖子,但不可扯掉头。 9要把一些鸟血洒在祭坛边,剩下的血要倒在坛脚旁。这是赎罪祭。 10祭司要依照献燔祭的条例献上另一只鸟。这样,祭司为他赎了罪,他就会得到赦免。

11“他若献不起两只斑鸠或雏鸽,就要献一公斤细面粉作赎罪祭。细面粉中不可浇油或加乳香,因为这是赎罪祭。 12他要把细面粉带到祭司那里,祭司要从中取出一把作为象征放在坛上,与献给耶和华的火祭一起焚烧。这是赎罪祭。 13这样,祭司为他赎了罪,他就会得到赦免。剩下的细面粉要归祭司,像献素祭一样。”

献赎过祭的条例

14耶和华对摩西说: 15“如果有人无意中违犯了耶和华圣物的条例,为了赎过,他要从羊群中选一只毫无残疾的公绵羊献给耶和华,或按圣所的秤献上同等价值的银子。这是赎过祭。 16他要赔偿所造成的损失,并加赔五分之一,要把这些都交给祭司。祭司要为他献上公绵羊作赎过祭,为他赎罪,他就会得到赦免。

17“如果有人触犯耶和华的诫命,即使他不知道,也是有罪的,必须担当罪责。 18他要从羊群中选一只毫无残疾的公绵羊,或把同等价值的银子带到祭司那里作赎过祭。祭司要为他的无心之过赎罪,他就会得到赦免。 19这是赎过祭,因为他在耶和华面前确实有罪。”