Levitiko 25 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 25:1-55

Za Chaka Chopumula

1Yehova anawuza Mose pa phiri la Sinai kuti, 2“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukadzalowa mʼdziko limene ndikukupatsani, nthakayo iyenera kumakasunga Sabata la Yehova. 3Pa zaka zisanu ndi chimodzi muzikalima minda yanu, ndipo kwa zaka zisanu ndi chimodzi muzikasadza mitengo yanu ya mpesa ndi kuthyola zipatso zake. 4Koma chaka chachisanu ndi chiwiri ndi chaka choti nthaka ipume, chaka cha Sabata la Yehova. Musalime mʼminda yanu kapena kusadza mitengo yanu ya mpesa. 5Musakolole zimene zinamera zokha mʼmunda mwanu. Musakakolole kapena kuthyola mphesa za mʼmitengo imene simunasadze. Chaka chimenechi nʼchoti nthaka ipumule. 6Chaka chimene nthakayo ipumula mudzakhala ndi chakudya chokwanira inuyo, akapolo anu aamuna ndi aakazi, antchito ndi alendo okhala nanu. 7Ziweto zanu pamodzi ndi nyama za mʼdziko lanu zizidzadya zipatso za mʼnthaka.

Chaka Chokondwerera Zaka Makumi Asanu

8“ ‘Muzichotsera Masabata asanu ndi awiri a zaka, ndi kuchulukitsa zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawirinso kuti Masabata asanu ndi awiri a zakawo akwane zaka 49. 9Ndipo pa tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri mulize lipenga mofuwula. Tsiku lochita mwambo wopepesera machimo muziliza lipenga mʼdziko lanu lonse. 10Mupatule chaka cha makumi asanu, ndipo mulengeze kuti pakhale ufulu mʼdziko lonse kwa onse amene ali mʼmenemo. Kwa inu chakachi chidzakhala choyimba lipenga la chikondwerero. Aliyense wa inu adzayenera kubwerera pa munda wake, ndipo aliyense wa inu adzabwerera ku fuko lake. 11Kwa inu chakachi chidzakhaladi chaka choyimba lipenga kukondwerera zaka makumi asanu. Pa chaka chimenechi musadzale kanthu ndipo musakolole mbewu zomera zokha kapenanso kuthyola mphesa pa mitengo yosasadzira. 12Chimenechi ndi chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Choncho chikhale chaka chopatulika kwa inu. Muzidya zokhazo zimene zakololedwa mʼminda.

13“ ‘Chaka chimenechi ndi choliza lipenga, kukondwerera zaka makumi asanu, ndipo aliyense abwerere pa malo ake.

14“ ‘Ngati unagulitsa kapena kugula malo ako kwa mnzako wa mʼdzikomo, pasakhale kuchenjeretsana. 15Ugule kwa mnzako potsata chiwerengero cha zaka zimene zatha kuyambira pa chikondwerero cha chaka cha makumi asanu chapita. Ndipo mnzakoyo akugulitse potsata chiwerengero cha zaka zokolola zomwe zatsala. 16Zaka zikakhala zochuluka, uwonjezere mtengo, ndipo zaka zikakhala zochepa, uchepetse mtengo, pakuti chimene iye akukugulitsa ndi zaka zokolola. 17Musachenjeretsane koma muope Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

18“ ‘Tsatirani malangizo anga ndipo mverani mosamala malamulo anga ndipo mudzakhala mʼdzikomo mwamtendere. 19Ndipo nthaka idzakupatsani zipatso zake. Mudzadya mpaka kukhuta ndiponso mudzakhala mʼdzikomo mwamtendere. 20Mwina nʼkafunsa kuti, ‘Kodi chaka chachisanu ndi chiwiri tidzadya chiyani ngati sitidzala kapena kukolola mbewu zathu?’ 21Ine ndidzatumiza madalitso ambiri chaka chachisanu ndi chimodzi moti nthaka yanu idzabala zinthu zokwanira kudya zaka zitatu. 22Pamene mukudzala chaka chachisanu ndi chitatu, muzidzadya chakudya chogonera ndipo mudzapitirira kudya mpaka nthawi yokolola mʼchaka chachisanu ndi chinayi.

23“ ‘Malo asagulitsidwe mpaka muyaya chifukwa dzikolo ndi langa. Inu ndinu alendo okhala ndi Ine. 24Malo onse amene ali mʼmanja mwanu mudzalole kuti amene anakugulitsani awawombole.

25“ ‘Ngati Mwisraeli mnzanu wasauka nagulitsako gawo lina la malo ake, mʼbale wake wapaphata abwere kudzawombola malo amene mʼbale wakeyo wagulitsa. 26Koma ngati munthuyo alibe wachibale woti nʼkuwombola malowo koma pambuyo pake iye mwini nʼkulemera ndi kupeza zokwanira kuwombolera, awombole malowo. 27Awerengerane zaka kuyambira pamene anagulitsa mundawo ndipo amubwezere amene anagulayo ndalama zimene akanayenera kuzipereka mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Atatero angathe kubwerera pa malo ake. 28Koma ngati sakhala nazo zokwanira kuti amubwezere amene anagula malowo, gawo limene anagulitsalo lidzakhala mʼmanja mwa munthu amene anagulayo mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Malowo adzabwezedwa chaka chimenechi, ndipo iye adzatha kubwerera pa malo ake.

29“ ‘Ngati munthu agulitsa nyumba ya mu mzinda umene uli mu linga, angathe kuyiwombola nyumbayo chisanathe chaka chathunthu chigulitsire. Mu nthawi imeneyi wogulitsayo atha kuyiwombola. 30Ngati nyumbayo siwomboledwa chisanathe chaka chimodzicho, nyumbayo idzakhala ya amene anagulayo ndi zidzukulu zake mpaka muyaya. Sidzabwezedwanso kwa mwini wake mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu. 31Koma nyumba za mʼmizinda yosazingidwa ndi linga ziwomboledwe monga mmene achitira ndi minda ya mʼdzikomo.

32“ ‘Alevi ali ndi ufulu owombola nyumba zawo za mʼmidzi yawo nthawi ina iliyonse. 33Koma ngati Mlevi sawombola nyumba imene inagulitsidwa mʼmudzi mwake, ndiye kuti idzabwezedwe mʼchaka choliza lipenga pokondwerera zaka makumi asanu, popeza nyumba zimenezi zili mʼmidzi ya Alevi ndi yawo pakati pa Aisraeli. 34Koma malo owetera ziweto a mʼmidzi yawoyo sayenera kugulitsidwa. Awa ndi malo awo mpaka muyaya.

35“ ‘Ngati mʼbale wako akhala wosauka kuti sangathe kudzisamalira yekha, umuthandize. Ukhale naye ngati mlendo kapena ngati munthu amene ukhala naye kwa kanthawi. 36Usalandire chiwongoladzanja chilichonse kuchokera kwa iye kapena kuwonjezerapo kanthu kena, koma uziopa Mulungu kuti mʼbale wakoyo akhale nawe. 37Musakongoze mnzanu ndalama kuti mulandire chiwongoladzanja, kapena kumugulitsa chakudya kuti mupeze phindu. 38Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti ndikupatseni dziko la Kanaani ndi kuti ndikhale Mulungu wanu.

39“ ‘Ngati mʼbale wanu asauka ndipo adzigulitsa yekha kwa inu, musamugwiritse ntchito ngati kapolo. 40Akhale ngati wantchito kapena ngati mlendo. Akugwirireni ntchito mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. 41Kenaka iye ndi ana ake achoke, ndipo apite ku fuko lake ndi kubwerera ku malo a makolo ake. 42Chifukwa Aisraeli ndi atumiki anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto, asagulitsidwe ngati akapolo. 43Musawalamulire mwankhanza koma wopani Mulungu wanu.

44“ ‘Kunena za akapolo aamuna ndi aakazi, amenewa mungathe kuwagula kuchokera kwa mitundu ya anthu imene yakuzungulirani. 45Mungathenso kugula akapolo kuchokera kwa alendo amene akukhala nanu kapena kuchokera ku mabanja amene mukukhala nawo amene ndi mbadwa za mʼdziko lanu. Iwowa akhoza kukhala akapolo anu. 46Akapolowo mungathe kuwasiya mʼmanja mwa ana anu inu mutafa kuti akhale cholowa chawo moyo wawo wonse. Koma musawalamulire mwankhanza Aisraeli anzanu.

47“ ‘Ngati mlendo kapena munthu amene akukhala nanu kwa kanthawi kochepa alemera ndipo mmodzi wa abale anu amene akukhala naye pafupi nʼkusauka, nadzigulitsa yekha kwa mlendo amene akukhala pakati panuyo kapena kwa mmodzi wa fuko la munthu wongokhala pafupi nayeyo, 48wodzigulitsayo ali ndi ufulu wowomboledwa. Mmodzi mwa abale ake angathe kumuwombola: 49amalume ake kapena mwana wa amalume ake, kapena wachibale wa mu fuko lake. Kapena ngati iye mwini alemera, atha kudziwombola yekha. 50Iye pamodzi ndi munthu amene anamugulayo awerengerane kuyambira chaka chimene anadzigulitsa kwa iyeyo mpaka chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Mtengo wodziwombolera ukhale wofanana ndi zakazo. Ndipo nthawi imene anali ndi mbuye wakeyo iwerengedwe ngati nthawi ya munthu wantchito. 51Ngati patsala zaka zambiri, iye ayenera kulipira mtengo woposera umene anamugulira. 52Ngati kwatsala zaka zochepa kuti ifike nthawi ya chaka chokondwerera zaka makumi asanu, iye awerengerane ndi mbuye wake, ndipo apereke ndalama za zowomboledwera molingana ndi zaka zotsalazo. 53Azikhala naye ngati wantchito wolembedwa chaka ndi chaka. Ndipo muonetsetse kuti mbuye wakeyo sakumulamulira mwankhanza.

54“ ‘Ngakhale munthuyo atapanda kuwomboledwa mwa njira zimenezi, iye ndi ana ake ayenera kumasulidwa mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu, 55pakuti Aisraeli ndi atumiki anga. Iwo ndi atumiki anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

New Serbian Translation

3. Мојсијева 25:1-55

Суботња година

1Господ рече Мојсију на гори Синај: 2„Говори Израиљцима и реци им: ’Кад уђете у земљу коју вам дајем, нека земља држи Господњу суботу. 3Шест година засејавај своју њиву, и шест година обрезуј свој виноград и сабирај род, 4а седме године нека буде субота потпуног одмора за земљу, Господња субота. Тада немој сејати своју њиву и обрезивати свој виноград. 5Немој жети што са̂мо роди након твоје жетве, нити брати грожђе од своје необрезане лозе. То ће бити година суботњег одмора за земљу. 6Што земља роди током своје суботе, то ће вам бити за јело. Сав њен урод нека буде за јело теби, твоме слузи и твојој слушкињи; твоме најамнику, и дошљаку који борави код тебе; 7твојој стоци и зверима што живе на твојој земљи. Све што земља роди, то се може јести.

Јубиларна година

8Наброј седам суботњих година, седам пута по седам година, тако да ових седам суботњих година дају збир од четрдесет девет година. 9Седмога месеца, десетога дана, заповеди да затруби труба; на дан откупљења, затрубите у трубе по свој земљи. 10Посветите педесету годину, и прогласите слободу у земљи за све њене становнике. То ће вам бити опросна година. Тада нека се сваки од вас врати на свој посед, и сваки човек нека се врати у свој род. 11Педесета година нека вам буде опросна. Не сејте и не жањите што роди након жетве, и не обрезујте лозу, 12јер то је опросна година. Нека вам буде света: храните се само оним што роди на њиви.

13Те опросне године, нека се сваки човек врати на свој посед.

14Стога, када продајете земљу своме ближњему, или је купујете од њега, не варајте свога брата. 15Кад купујеш од свога ближњега, платићеш само за број година од опросне године; онај ко продаје наплатиће ти само за остатак жетвених година. 16Што је више година, то је већа цена; што је мање година, то је мања цена, јер он ти продаје број жетви. 17Не варајте свог ближњег, него се бој свога Бога, јер ја сам Господ, Бог ваш.

18Вршите моје уредбе, и држите моје законе. Вршите их и живећете спокојно на земљи. 19Земља ће давати свој род, па ћете јести до миле воље, и спокојно живети у њој. 20Ако се питате: шта ћемо јести седме године, кад не будемо ни сејали, ни скупљали свој урод? 21Ево, ја ћу вам послати свој благослов: шесте године ће земља родити род за три године. 22А кад будете сејали осме године, хранићете се од старог урода све до девете године, док не приспе њен урод.

23Земља не сме да се прода заувек, јер земља припада мени, а ви сте код мене странци и дошљаци. 24Где год имате земљу у поседу, морате дозволити да се земља откупи.

25Ако твој брат осиромаши и прода свој посед, нека дође његов најближи рођак-старатељ и откупи што је његов брат продао. 26Ко нема рођака-старатеља, али дође до довољно средстава да откупи посед, 27нека изброји године од откупа и исплати разлику човеку коме га је продао. Онда нека се врати на свој посед. 28А ако нема довољно средстава, посед ће остати у власништву онога који га је купио до опросне године. У опросној години земља ће бити враћена, па ће се он вратити на свој посед.

29Ако неко прода стамбену кућу у граду опасаном зидинама, он може да је откупи пре него што истекне година од њене продаје. Рок за откуп биће једна година. 30Ако се кућа не откупи пре истека пуне године, кућа у граду опасаном зидинама прећи ће у трајно власништво купца и његових потомака, те неће бити враћена у опросној години. 31Куће по селима које нису ограђене зидинама, нека се воде као њиве; оне се могу откупити, али се у опросној години морају вратити.

32Међутим, Левити ће заувек држати право откупа кућа које поседују у левитским градовима. 33Ако један од Левита откупи кућу, која је продана у једном од градова у њиховом поседу, она мора да се врати у опросној години, јер су куће по левитским градовима њихово власништво међу Израиљцима. 34Пашњаци око ових градова не смеју се продавати, јер то је њихово власништво за сва времена.

35Ако твој брат, који живи уз тебе, осиромаши, те не може да се издржава, помози му; нека живи уз тебе као странац или дошљак. 36Не узимај камату од њега, и не наплаћуј му више, него се бој свога Бога. Нека твој брат живи уз тебе. 37Не позајмљуј му новац с каматом, и не наплаћуј му више за храну. 38Ја сам Господ, Бог ваш, који сам вас извео из Египта, да вам дам хананску земљу, и да вам будем Бог.

39Ако осиромаши твој брат који је уз тебе, и прода се теби, не терај га да ради као роб. 40Нека буде код тебе као најамник и као дошљак, па нека служи код тебе до опросне године. 41Тада може да оде од тебе са својом децом, и да се врати у свој род и на посед својих предака. 42Зато што су моје слуге које сам извео из Египта, не смеју се продавати као што се продају робови. 43Немој господарити немилосрдно над њим, него се бој свога Бога.

44Робове и робиње можете имати, али од народа који живе око вас. Њих можете куповати као робове и робиње. 45Можете куповати и децу дошљака и странаца, који живе међу вама, или оне који су рођени у вашој земљи, и чије породице живе међу вама. Они могу да буду ваше власништво. 46Можете их задржати у власништву за вашу децу после вас, да их наследе као трајно власништво. Они нека вам служе као робови, али над вашом браћом Израиљцима, нико да не господари немилосрдно.

47Ако се странац или дошљак обогати, а твој брат осиромаши, па се прода странцу или дошљаку међу вама, или потомку из странчевог рода, 48он има право да буде откупљен и након што се продао. Нека га откупи неко од његове браће, 49или нека га откупи стриц, или стричев син, или неко од најближе породице. Уколико се обогати, он може да откупи самог себе. 50Нека с купцем израчуна време од године када се продао, па до опросне године; цена за коју се продао одређиваће се према броју година. Време које је провео с власником нека му се рачуна као најамнику. 51Ако остане још много година, он ће, према њиховом броју, платити цену за свој откуп. 52Ако остане мало година до опросне године, он ће платити за свој откуп према њиховом броју. 53Време које је провео с власником, нека му се рачуна као најамнику. Нека се не господари немилосрдно над њим на твоје очи.

54Уколико не буде откупљен овако, он и његова деца биће ослобођени у опросној години. 55Јер Израиљци су моје слуге, које сам извео из Египта. Ја сам Господ, Бог ваш!