Levitiko 23 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 23:1-44

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Awa ndi masiku anga osankhika a chikondwerero, masiku osankhika olemekeza Yehova amene uyenera kulengeza kuti akhale masiku opatulika a misonkhano.

Za Sabata

3“ ‘Pa masiku asanu ndi limodzi muzigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata lopuma, tsiku la msonkhano wopatulika. Kulikonse kumene inu mukukhala musamagwire ntchito iliyonse tsiku limeneli popeza ndi tsiku la Sabata la Yehova.

Za Paska ndi za Buledi Wopanda Yisiti

4“ ‘Awa ndiwo masiku osankhidwa a zikondwerero za Yehova, masiku woyera a misonkhano amene muti mudzalengeze pa nthawi yake: 5Chikondwerero cha Paska chiziyamba madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. 6Tsiku la 15 la mwezi womwewo ndi tsiku lolemekeza Yehova ndipo muziyamba Chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri. 7Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse. 8Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito yolemetsa.’ ”

Za Zipatso Zoyambirira Kucha

9Yehova anawuza Mose kuti, 10“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo ndi kukolola za mʼminda mwanu, mudzabwere kwa wansembe ndi mtolo wa tirigu woyambirira kucha wa mʼminda mwanu. 11Wansembeyo auweyule mtolowo pamaso pa Yehova kotero mtolowo udzalandiridwa mʼmalo mwanu. Wansembe auweyule tsiku lotsatana ndi la Sabata. 12Pa tsiku limene muweyula mtolowo, muperekenso mwana wankhosa wa mwamuna wa chaka chimodzi, wopanda chilema kuti akhale nsembe yopsereza ya kwa Yehova. 13Chopereka chachakudya chake chikhale cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta kuti chikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Yehova, ya fungo lokoma. Ndipo chopereka cha chakumwa chake chikhale vinyo wa malita anayi ndi theka. 14Musadye buledi aliyense kapena tirigu wokazinga, kapena wamuwisi mpaka tsiku limene mwabwera ndi chopereka ichi kwa Mulungu wanu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.

Chikondwerero cha Masabata

15“ ‘Kuyambira tsiku lotsatana ndi la Sabata lija, tsiku limene munabwera ndi mtolo wa nsembe yoweyula, muziwerenga masabata asanu ndi awiri athunthu. 16Ndiye kuti muwerenge masiku makumi asanu kuchokera pa tsiku lotsatana ndi Sabata la chisanu ndi chiwiri, ndipo kenaka mupereke nsembe ya tirigu watsopano kwa Yehova. 17Kuchokera kulikonse kumene mukukhala, mubwere pamaso pa Yehova ndi buledi muwiri wa ufa wosalala wa makilogalamu awiri, ophikidwa ndi yisiti kuti akhale nsembe yoweyula ya zakudya zoyamba kucha. 18Pamodzi ndi bulediyu muperekenso ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri, aliyense akhale wa chaka chimodzi ndi wopanda chilema. Pakhalenso ngʼombe yayingʼono yayimuna ndi nkhosa zazimuna ziwiri. Zimenezi zidzakhala nsembe zopsereza zopereka kwa Yehova pamodzi ndi nsembe za zakudya ndi nsembe za zakumwa. Zonsezi zikhale nsembe zopsereza za fungo lokomera Yehova. 19Kenaka mupereke mbuzi imodzi yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndiponso ana ankhosa awiri, aliyense wa chaka chimodzi kuti akhale nsembe yachiyanjano. 20Wansembe aweyule ana ankhosa awiriwo pamaso pa Yehova monga nsembe yoweyula, pamodzi ndi buledi wa tirigu woyambirira kucha. Zimenezi ndi zopereka zopatulika za Yehova zopatsidwa kwa ansembe. 21Pa tsiku lomwelo mulengeze za msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.

22“ ‘Pamene mukukolola zinthu mʼmunda mwanu, musakolole munda wanu mpaka mʼmalire mwenimweni, ndipo musatole khunkha lake. Zimenezo musiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”

Chikondwerero cha Malipenga

23Yehova anawuza Mose kuti, 24“Uza Aisraeli kuti, ‘Tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, likhale tsiku lopumula, la msonkhano wopatulika, mulilengeze poyimba lipenga. 25Musagwire ntchito zolemetsa koma mupereke nsembe yopsereza kwa Yehova.’ ”

Tsiku Lopepesera Machimo

26Yehova anawuza Mose kuti, 27“Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri ndi tsiku lochita Mwambo Wopepesera Machimo. Muzichita msonkhano wopatulika. Muzidzichepetsa pamaso pa Yehova ndi kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova. 28Tsiku limeneli musamagwire ntchito chifukwa ndi tsiku la Mwambo Wopepesera Machimo, kupepesera machimo anu pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 29Munthu aliyense amene sasala zakudya pa tsiku limeneli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake. 30Aliyense wogwira ntchito tsiku limeneli ndidzamuwononga pakati pa anthu a mtundu wake. 31Inu musadzagwire ntchito iliyonse. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale. 32Limeneli kwa inu ndi tsiku la Sabata lopumula, ndipo muyenera kusala zakudya. Kuyambira madzulo a tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi mpaka madzulo ena otsatirawo muzisunga tsikulo ngati Sabata lanu.”

Chikondwerero cha Misasa

33Yehova anawuza Mose kuti, 34“Uwawuze Aisraeli kuti pa masiku asanu ndi awiri kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri pazikhala Chikondwerero cha Misasa cholemekeza Yehova. 35Tsiku loyamba ndi la msonkhano wopatulika, musagwire ntchito zolemetsa. 36Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Kumeneku ndi kutsekera kwa msonkhano waukulu. Musagwire ntchito zolemetsa.

37(“ ‘Amenewa ndi masiku osankhika a chikondwerero cha Yehova, amene muziwalengeza kuti ndi nthawi ya msonkhano wopatulika. Masiku amenewa muzipereka nsembe zopsereza, nsembe za chakudya, nsembe zanyama ndi zopereka zachakumwa za tsiku ndi tsiku. 38Zopereka zimenezi ndi zowonjezera pa zopereka za Yehova za pa Sabata, zopereka zanu zolumbira ndiponso mphatso zanu zaufulu zopereka kwa Yehova.)

39“ ‘Choncho kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutakolola zinthu mʼmunda mwanu, muchite chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Tsiku loyamba ndi tsiku lopumula, ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu ndi lopumulanso. 40Pa tsiku loyamba muzitenga zipatso zabwino kwambiri zothyola mʼmitengo, nthambi za kanjedza, nthambi zazikulu za mitengo ya masamba ambiri, ndi za misondozi yakumtsinje, ndipo muzikondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu kwa masiku asanu ndi awiri. 41Chaka chilichonse muzichita chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse. Muzichita chikondwerero chimenechi mwezi wachisanu ndi chiwiri. 42Muzikhala mʼmisasa masiku asanu ndi awiri. Onse amene ali mbadwa mʼdziko la Israeli azikhala mʼmisasa 43kuti zidzukulu zanu zidzadziwe kuti ndine amene ndinakhazika Aisraeli mʼmisasa nditawatulutsa ku Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”

44Choncho Mose analengeza kwa Aisraeli masiku osankhika a zikondwerero za Yehova.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

利未记 23:1-44

有关节期的条例

1耶和华对摩西说: 2“你要告诉以色列人,以下是耶和华所定的节期,你们要宣布这些节期为举行圣会的日子。

安息日

3“你们一周可以工作六天,但第七天是安息日,你们要休息,举行圣会。不可做任何工,无论你们住在哪里,都要守耶和华的安息日。

4“以下是耶和华所定的节期,你们要在这些日子召开圣会。

逾越节和无酵节

5“一月十四日从黄昏开始是耶和华的逾越节。 6从一月十五日开始是耶和华的无酵节,一连七天你们必须吃无酵饼。 7在无酵节的第一天,你们要举行圣会,不可做日常工作。 8这七天你们要献火祭给耶和华。第七天,你们要举行圣会,不可做日常工作。”

初熟节

9耶和华对摩西说: 10“你把以下条例告诉以色列人。

“你们进入耶和华将要赐给你们的那片土地以后,每逢庄稼初熟之时,你们要带一捆初熟的谷物交给祭司。 11祭司要在安息日后第一天把那捆谷物在耶和华面前摇一摇,你们所献的就会得到悦纳。 12在献谷物那天,你们要献给耶和华一只毫无残疾、一岁的公羊羔作燔祭, 13同时要把两公斤调油的细面粉作素祭,一起献给耶和华作馨香的火祭,也要献一升酒作奠祭。 14你们必须先将这些祭物献给你们的上帝后,才可以吃饼、烘烤的谷物和新鲜穗子。不论住在哪里,你们都要世代遵守这永远不变的律例。

五旬节

15“从安息日后第一天,即你们献上摇祭的那天算起,你们要数整整七周, 16一直数到第七个安息日后的第一天,共五十天。到那天,你们要把新收的谷物作为素祭献给耶和华。 17你们要用两公斤细面粉加上酵,烤成两个饼作摇祭,从你们居住的地方带来献给耶和华作初熟之祭。 18你们要把七只毫无残疾、一岁的公羊羔、一头公牛犊、两只公绵羊和那两个饼一起献给耶和华作燔祭。这些一起献上的燔祭、素祭和奠祭是蒙耶和华悦纳的馨香火祭。 19你们也要献一只公山羊作赎罪祭,两只一岁的公绵羊作平安祭。 20祭司要把这两只公绵羊和初熟之物做的饼作为摇祭在耶和华面前摇一摇。这些是献给耶和华的圣物,归祭司所有。 21你们要在那天召开圣会,不可做日常工作。不论住在哪里,你们都要世代遵守这永远不变的律例。 22你们收割时,不可割尽田角地边的庄稼,也不可捡落在地里的。要把这些留给穷人和外族人。我是你们的上帝耶和华。”

吹号节

23耶和华对摩西说: 24“你告诉以色列人,‘你们要在七月一日休息,要吹号作纪念,召开圣会。 25你们不可做日常工作,要献火祭给耶和华。’”

赎罪日

26耶和华对摩西说: 27“七月十日是赎罪日,你们要举行圣会,禁食,献火祭给耶和华。 28那是在你们的上帝耶和华面前为自己赎罪的日子,你们不可工作。 29那天,凡不禁食的,要将他从民中铲除; 30凡工作的,耶和华要毁灭他。 31你们不可做任何工作。不论住在哪里,你们都要世代遵守这永不改变的律例。 32那是你们可以完全休息的安息之日。从七月九日傍晚至次日傍晚,你们必须禁食。”

住棚节

33耶和华对摩西说: 34“你把以下条例告诉以色列人。

“从七月十五日开始,你们要一连七天向耶和华守住棚节。 35第一天,你们要举行圣会,不可做日常工作。 36这七天你们要献火祭给耶和华。第八天要举行圣会,献火祭给耶和华。这是庄严的聚会,你们不可做日常工作。

37“以上是耶和华所定的节期。在这些节期里,你们要召开圣会,按规定的日子献给耶和华燔祭、素祭、奠祭和其他祭物。 38除了守安息日并向耶和华献供物、还愿祭和自愿献的祭以外,你们还要守这些节期。

39“你们收割完后,从七月十五日起,要一连七天庆祝耶和华的节期,第一天和第八天是安息之日。 40第一天,你们要摘下树上结的上好果子,折下棕树枝、叶子浓密的树枝与河边的柳枝,在你们的上帝耶和华面前欢庆七天。 41在每年七月的这七天,你们要向耶和华守这节期。这是永远不变的律例,你们世世代代都要遵守。 42你们要搭棚居住七天,所有以色列人都要住在棚里。 43这样,你们的后代就会知道,我带领以色列人离开埃及后,曾让他们住在棚里。我是你们的上帝耶和华。”

44于是,摩西以色列人宣布了耶和华所定的这些节期。