Levitiko 20 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 20:1-27

Zilango za Tchimo

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Uza Aisraeli kuti, ‘Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala mu Israeli wopereka mwana wake kwa Moleki ayenera kuphedwa. Anthu a mʼdera lakelo amuphe ndi miyala. 3Munthu ameneyo ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anzake.’ Popereka mwana wake kwa Moleki, wadetsa malo anga wopatulika ndi kuyipitsa dzina langa loyera. 4Ngati anthu a mʼderalo achita ngati sakumuona munthuyo pamene akupereka mwana wake kwa Moleki ndi kusamupha, 5Ineyo ndidzamufulatira pamodzi ndi banja lake. Ndidzawachotsa pakati pa anthu anzawo onse amene anamutsatira, nadziyipitsa okha popembedza Moleki.”

6“ ‘Ngati munthu adzapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena kwa owombeza, nadziyipitsa powatsatira iwowo, Ine ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anthu anzake.

7“ ‘Chifukwa chake dzipatuleni ndi kukhala woyera popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 8Ndipo sungani malangizo anga ndi kuwatsata. Ine ndine Yehova amene ndimakuyeretsani.

9“ ‘Munthu aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa. Magazi ake adzakhala pamutu pake chifukwa iye watemberera abambo kapena amayi ake.

10“ ‘Ngati munthu wachita chigololo ndi mkazi wa mnzake, mwamunayo pamodzi ndi mkaziyo ayenera kuphedwa.

11“ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi wa abambo ake, wachititsa manyazi abambo ake. Munthuyo pamodzi ndi mkaziyo ayenera kuphedwa. Magazi awo adzakhala pa mitu pake.

12“ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi wa mwana wake, awiriwo ayenera kuphedwa. Iwo achita chinthu chonyansa kwambiri. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo.

13“ ‘Ngati munthu agonana ndi mwamuna mnzake ngati akugonana ndi mkazi, ndiye kuti onsewo achita chinthu cha manyazi. Choncho aphedwe. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo.

14“ ‘Ngati munthu akwatira mkazi, nakwatiranso amayi ake, chimenecho ndi chinthu choyipa kwambiri. Mwamunayo pamodzi ndi akaziwo ayenera kutenthedwa pa moto kuti chinthu choyipa chotere chisapezekenso pakati panu.

15“ ‘Ngati mwamuna agonana ndi nyama, iye ayenera kuphedwa, ndipo muyeneranso kupha nyamayo.

16“ ‘Ngati mkazi agonana ndi nyama, aphedwe pamodzi ndi nyamayo. Mkaziyo ndi nyamayo ayenera kuphedwa, ndipo magazi awo adzakhala pa mitu pawo.

17“ ‘Ngati munthu akakwatira mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake, kapena mwana wamkazi wa amayi ake, ndipo iwo nʼkugonana, ndiye kuti achita chinthu chochititsa manyazi. Onse awiri ayenera kuchotsedwa pa gulu la abale awo. Tsono popeza munthuyo wachititsa manyazi mlongo wake, adzayenera kulandira chilango.

18“ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi pa nthawi yake yosamba, ndiye kuti wavula msambo wake, ndipo mkaziyo wadzivulanso. Onse awiri achotsedwe pakati pa anthu anzawo.

19“ ‘Musagonane ndi mchemwali wa amayi anu kapena abambo anu, pakuti kutero ndi kuchititsa manyazi mʼbale wanu. Nonse mudzalipira mlandu wanu.

20“ ‘Ngati munthu agonana ndi azakhali ake, munthuyo wachititsa manyazi a malume ake. Onse adzalipira mlandu wawo. Onsewo adzafa wopanda mwana.

21“ ‘Munthu akakwatira mkazi wa mchimwene wake ndiye kuti wachita chinthu chonyansa. Wachititsa manyazi mʼbale wakeyo. Onse awiriwo adzakhala wopanda mwana.

22“ ‘Nʼchifukwa chake muzisunga malangizo anga onse ndi malamulo anga ndipo muwatsatire kuti ku dziko limene Ine ndikupita nanu kuti mukakhalemo lisakakusanzeni. 23Musatsanzire miyambo ya mitundu ya anthu imene ndi kuyipirikitsa inu mukufika. Chifukwa iwo anachita zinthu zonsezi, ndipo Ine ndinanyansidwa nawo. 24Koma Ine ndinakuwuzani kuti, ‘Mudzatenga dziko lawo. Ine ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale cholowa chanu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.’ Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndakupatulani pakati pa mitundu yonse ya anthu.

25“ ‘Chifukwa chake muzisiyanitsa pakati pa nyama zoyeretsedwa ndi nyama zodetsedwa ndiponso pakati pa mbalame zoyeretsedwa ndi mbalame zodetsedwa. Musadzidetse pakudya nyama iliyonse kapena mbalame, kapena chilichonse chimene chimakwawa pansi, chimene Ine ndachipatula kuti chikhale chodetsedwa kwa inu. 26Muzikhala woyera pamaso panga chifukwa Ine Yehova, ndine woyera ndipo ndakupatulani pakati pa anthu a mitundu yonse kuti mukhale anthu anga.

27“ ‘Mwamuna kapena mkazi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena wanyanga pakati panu ayenera kuphedwa. Muwagende ndi miyala, ndipo magazi awo adzakhala pa mitu pawo.’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

利未记 20:1-27

各种罪的惩处条例

1耶和华对摩西说: 2“你把以下条例告诉以色列人。

“在你们或寄居在你们中间的外族人中,如果有人把子女献给假神摩洛,必须处死他,当地的人要用石头打死他。 3我也必严惩那人,将他从民中铲除。因为他把子女献给摩洛,玷污我的圣所,亵渎我的圣名。 4如果那地方的人对此置之不理,没有处死那人, 5我必严惩那人一家,从民中铲除他和那些追随他与摩洛苟合的人。 6如果有人求问灵媒或巫师,与他们苟合,我必严惩,将他从民中铲除。 7你们要洁净自己,做圣洁的人,因为我是你们的上帝耶和华。 8你们要遵行我的律例。我是使你们圣洁的耶和华。

9“咒骂父母的,必被处死。他咒骂父母,必须承担自己的罪。 10如果有人与别人的妻子通奸,奸夫淫妇必须被处死。 11如果有人与父亲的妻妾同寝,就是羞辱他的父亲。要把二人处死,他们要承担自己的罪。 12如果有人与儿媳同寝,二人都必须被处死。他们乱伦,要承担自己的罪。 13如果男人与男人同寝,好像男人与女人同寝一样,他们的行为可憎,必须被处死。他们要承担自己的罪。 14如果有人娶妻,又娶岳母,便是大恶。要把他们三人烧死,使你们杜绝这种败坏之事。 15如果有男人与兽类交合,他和兽都要被处死。 16如果有女人与兽类交合,女人和兽都要被处死。他们罪有应得,必须被处死。

17“如果有人娶了同父异母或同母异父的姊妹,这是可耻之事,必须公开铲除他们。他与自己的姊妹乱伦,要承担自己的罪。 18如果有人与经期的女人同寝,他就暴露了女人的血泉,女人也自露血泉。要将他们二人从民中铲除。 19不可与姨母或姑母乱伦,因为这是羞辱自己的亲人。二人要承担自己的罪。 20如果有人与伯母或婶母同寝,就是羞辱他的伯父或叔父。二人要承担自己的罪恶,必无子女而死。 21如果有人娶兄嫂或弟媳,这是污秽行为,羞辱了自己的兄弟。二人必无儿无女。

22“你们要遵行我的一切律例和典章,免得我要带你们去的那片土地把你们吐出去。 23我要在你们面前赶走那片土地上的各族,你们不要随从他们的习俗。他们做了以上那些事,所以我厌恶他们。 24我曾说你们必占据他们的土地,我要把那片奶蜜之乡赐给你们作产业。我是你们的上帝耶和华,我已经把你们跟万族分开。 25所以,你们要区分洁净和不洁净的兽类与鸟类。不可吃那些我视为不洁净的飞禽、走兽和爬虫,以免玷污自己。 26你们要圣洁,因为我耶和华是圣洁的。我把你们跟万族分开,使你们做我的子民。 27如果有人做灵媒或巫师,不论男女,都必须被处死。你们要用石头打死他们,使他们承担自己的罪。”