Levitiko 2 – CCL & NVI-PT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 2:1-16

Nsembe Zachakudya

1“ ‘Munthu wina aliyense akabwera ndi nsembe ya chakudya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala ufa wosalala. Ufawo ausakanize ndi mafuta ndi lubani, 2ndipo apite nawo kwa ansembe, ana a Aaroni. Atapeko modzazitsa dzanja ufa wosalala uja kuti ukhale wachikumbutso pamodzi ndi mafuta ndi lubani ndipo atenthe zonsezi pa guwa lansembe kuti zilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa chopereka chonse. Iyi ndi nsembe yotentha pa moto ndiponso fungo lokomera Yehova. 3Zotsala za nsembe ya chakudyazo ndi za Aaroni pamodzi ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova.

4“ ‘Ukabweretsa nsembe ya chakudya chophika mu uvuni, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta, kapena timitanda ta buledi topyapyala, topanda yisiti koma topaka mafuta. 5Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophika pa chitsulo chamoto, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta. 6Umuduledule bulediyo ndi kumupaka mafuta; imeneyo ndi nsembe yachakudya. 7Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophikidwa pa chiwaya, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. 8Munthu azibwera ndi nsembe za chakudya zimene wapanga ndi zinthu zimenezi. Atachipereka kwa wansembe, iyeyu adzipita nacho ku guwa. 9Wansembeyo atengeko gawo lina la nsembeyo kukhala ufa wachikumbutso kuti ilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa nsembe yonse ndipo ayitenthe pa moto monga nsembe yopsereza ya fungo lokomera Yehova. 10Zotsala za nsembe ya chakudyayo zikhale za Aaroni ndi ana ake. Chimenechi ndi chigawo chopatulika kwambiri chifukwa chatapidwa pa chopereka chotentha pa moto cha Yehova.

11“ ‘Nsembe ya chakudya chilichonse imene ubweretsa kwa Yehova ikhale yopanda yisiti, pakuti suyenera kupereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto imene ili ndi yisiti kapena uchi. 12Ziwirizi ungathe kubwera nazo kwa Yehova ngati chopereka cha zokolola zoyambirira. Koma usazitenthe pa guwa kuti zikhale fungo lokomera Yehova. 13Zopereka zako zonse zachakudya uzithire mchere. Usayiwale kuthira mchere pa chopereka chako popeza mcherewo ukusonyeza pangano pakati pa iwe ndi Mulungu wako. Tsono uzinthira mchere pa chopereka chako chilichonse.

14“ ‘Mukamapereka kwa Yehova chopereka cha chakudya choyamba kucha, choperekacho chikhale cha chipatso chatsopano chokazinga pa moto ndi chopunthapuntha. 15Uchithire mafuta ndi lubani pakuti ndi chopereka cha chakudya. 16Tsono wansembe atenthe gawo la chopereka chopunthapuntha chija kuti chikhala ufa wachikumbutso ndi cha mafuta pamodzi ndi lubani yense kuti Yehova alandire mʼmalo mwa zopereka zonse. Ichi ndi chopereka chotentha pa moto cha Yehova.

Nova Versão Internacional

Levítico 2:1-16

A Oferta de Cereal

1“Quando alguém trouxer uma oferta de cereal ao Senhor, terá que ser da melhor farinha. Sobre ela derramará óleo, colocará incenso 2e a levará aos descendentes de Arão, os sacerdotes. Um deles apanhará um punhado da melhor farinha com óleo e com todo o incenso e os queimará no altar como porção memorial. É oferta preparada no fogo, de aroma agradável ao Senhor. 3O que restar da oferta de cereal pertence a Arão e a seus descendentes; é parte santíssima das ofertas dedicadas ao Senhor, preparadas no fogo.

4“Se um de vocês trouxer uma oferta de cereal assada no forno, seja da melhor farinha: bolos feitos sem fermento, amassados com óleo, ou2.4 Ou e pães finos sem fermento e untados com óleo. 5Se a sua oferta de cereal for preparada numa assadeira, seja da melhor farinha, amassada com óleo e sem fermento. 6Divida-a em pedaços e derrame óleo sobre ela; é uma oferta de cereal. 7Se a sua oferta de cereal for cozida numa panela, seja da melhor farinha com óleo. 8Traga ao Senhor a oferta de cereal feita desses ingredientes e apresente-a ao sacerdote, que a levará ao altar. 9Ele apanhará a porção memorial da oferta de cereal e a queimará no altar; é oferta preparada no fogo, de aroma agradável ao Senhor. 10O restante da oferta de cereal pertence a Arão e a seus descendentes; é parte santíssima das ofertas dedicadas ao Senhor, preparadas no fogo.

11“Nenhuma oferta de cereal que vocês trouxerem ao Senhor será feita com fermento, pois vocês não queimarão fermento nem mel como oferta preparada no fogo ao Senhor. 12Podem trazê-los como oferta dos primeiros frutos ao Senhor, mas não podem oferecê-los no altar como aroma agradável. 13Temperem com sal todas as suas ofertas de cereal. Não excluam de suas ofertas de cereal o sal da aliança do seu Deus; acrescentem sal a todas as suas ofertas.

14“Se você trouxer ao Senhor uma oferta de cereal dos primeiros frutos, ofereça grãos esmagados de cereal novo, tostados no fogo. 15Sobre ela derrame óleo e coloque incenso; é oferta de cereal. 16O sacerdote queimará a porção memorial do cereal esmagado e do óleo, com todo o incenso, como uma oferta ao Senhor preparada no fogo.