Levitiko 15 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 15:1-33

Zonyansa Zotuluka Mʼthupi

1Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, 2“Yankhulani ndi Aisraeli ndipo muwawuze kuti, ‘Mwamuna aliyense akakhala ndi nthenda yotulutsa mafinya ku maliseche ake, zotulukazo ndi zonyansa ndithu. 3Lamulo lokhudza kudziyipitsira ndi zotuluka ku maliseche a munthu nali: Malisechewo akamatulukabe mafinya, kaya aleka, munthuyo adzakhala wodetsedwa:

4“ ‘Bedi lililonse limene munthu wotulutsa mafinyayo agonapo, ndiponso chinthu chilichonse chimene akhalepo chidzakhala chodetsedwa. 5Aliyense wokhudza bedi la munthuyo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 6Aliyense wokhala pa chinthu chimene munthu wotulutsa mafinyayo anakhalapo, achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

7“ ‘Aliyense wokhudza thupi la munthu amene akutulutsa mafinyayo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

8“ ‘Munthu wotulutsa mafinya akalavulira malovu munthu wina amene ndi woyeretsedwa, munthu ameneyo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

9“ ‘Chilichonse chimene munthuyo akhalira akakwera pa kavalo chidzakhala chodetsedwa. 10Ndipo aliyense wokhudza chimene anakhalira munthuyo adzakhala wodetsedwanso mpaka madzulo. Aliyense wonyamula chinthucho achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

11“ ‘Munthu wotulutsa mafinyayo akakhudza munthu aliyense asanasambe mʼmanja, wokhudzidwayo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

12“ ‘Mʼphika wadothi umene munthu wotulutsa mafinyayo wakhudza awuphwanye, ndipo chiwiya chilichonse chamtengo achitsuke ndi madzi.

13“ ‘Munthu wotulutsa mafinyayo akaona kuti wachira, awerenge masiku asanu ndi awiri akuyeretsedwa kwake kenaka achape zovala zake ndi kusamba pa kasupe, ndipo adzayeretsedwa. 14Pa tsiku la chisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri kapena mawunda a nkhunda awiri ndi kubwera nazo pamaso pa Yehova pa khomo pa tenti ya msonkhano ndipo azipereke kwa wansembe. 15Wansembe apereke zimenezo: imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera machimo a munthu wotulutsa mafinya uja pamaso pa Yehova.

16“ ‘Mwamuna akataya pansi mbewu yake yaumuna, asambe thupi lake lonse. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 17Chovala chilichonse kapena chikopa chilichonse pomwe pagwera mbewu yaumunayo achichape, komabe chidzakhala chodetsedwa mpaka madzulo. 18Mwamuna akagona ndi mkazi wake nataya mbewu yake yaumuna, onse awiriwo asambe. Komabe adzakhala odetsedwa mpaka madzulo.

19“ ‘Mkazi akakhala wosamba ndipo ikakhala kuti ndi nthawi yake yeniyeni yosamba, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. Aliyense amene adzamukhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

20“ ‘Chilichonse chimene mkaziyo agonera pa nthawi yake yosamba chidzakhala chodetsedwa, ndipo chilichonse chimene adzakhalira chidzakhalanso chodetsedwa. 21Aliyense wokhudza bedi lake achape zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 22Aliyense wokhudza chimene wakhalapo achape zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 23Kaya ndi bedi kapena chinthu china chilichonse chimene anakhalapo, ngati munthu wina akhudza chinthucho, munthuyo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

24“ ‘Mwamuna aliyense akagona naye ndipo magazi osamba kwake ndi kumukhudza, munthuyo adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri, ndipo bedi limene wagonapo lidzakhalanso lodetsedwa.

25“ ‘Mkazi akataya magazi masiku ambiri, wosakhala pa nthawi yake yosamba, kapena akamasambabe kupitirira nthawi yake yosamba, mkaziyo adzakhala wodetsedwa nthawi yonse imene akutaya magazi, monga momwe amakhalira pa masiku ake osamba. 26Bedi lililonse limene mkaziyo adzagonapo pa masiku onse pamene ali wotaya magazi, ndiponso chilichonse chimene wakhalira chidzakhala chodetsedwa monga mmene chimakhalira chodetsedwa pa nthawi yake yosamba. 27Aliyense amene adzakhudza zinthu zimenezo adzakhala wodetsedwa ndipo ayenera kuchapa zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

28“ ‘Nthawi yosamba ikatha, mkaziyo awerenge masiku asanu ndi awiri, ndipo masikuwo akatha adzakhala woyeretsedwa. 29Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mkaziyo atenge njiwa ziwiri kapena mawunda awiri, ndipo abwere nazo kwa wansembe pa khomo la Tenti ya Msonkhano. 30Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera mkaziyo pamaso pa Yehova chifukwa cha matenda ake wosamba aja.

31“ ‘Choncho muwayeretsa ana a Israeli nʼkudetsedwa kwawo kuti angafe pochita tchimo lowadetsa limene polichita limadetsa malo anga wokhalamo amene ali pakati pawo.’ ”

32Amenewa ndi malamulo a munthu amene akutuluka mafinya kumaliseche kwake, komanso a munthu aliyense amene wadetsedwa ndi mbewu yaumuna, 33mkazi wodwala chifukwa cha msambo komanso a mwamuna kapena mkazi amene akutulutsa mafinya kumaliseche kwake ndi mwamuna wogona ndi mkazi amene akusamba.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

利未記 15:1-33

有關漏症患者的條例

1耶和華對摩西亞倫說: 2「你們把以下條例告訴以色列人。

「如果有男人患了漏症,他下體的排泄物是不潔淨的。 3不論他下體的排泄物止住與否,他都是不潔淨的。 4他睡過的床或坐過的東西都不潔淨。 5凡碰到他睡過的床的人都不潔淨,必須洗衣、沐浴,等到傍晚才能潔淨。 6凡坐他坐過之物的人都不潔淨,必須洗衣、沐浴,等到傍晚才能潔淨。 7凡碰到他的人都不潔淨,必須洗衣、沐浴,等到傍晚才能潔淨。 8如果他吐唾沫在一個潔淨的人身上,那人便不潔淨,必須洗衣、沐浴,等到傍晚才能潔淨。 9他騎過的鞍子是不潔淨的。 10凡碰到他坐過之物的人都不潔淨,要等到傍晚才能潔淨。碰到這些東西的人都不潔淨,必須洗衣、沐浴,等到傍晚才能潔淨。 11如果他沒有洗手就碰到別人,那人便不潔淨,必須洗衣、沐浴,等到傍晚才能潔淨。 12必須打碎他摸過的陶器,用水清洗他摸過的木器。 13他病癒後,必須經過七天的潔淨期,要洗淨衣服,用清水沐浴,這樣就潔淨了。 14第八天,他要把兩隻斑鳩或雛鴿帶到會幕門前,在耶和華面前交給祭司獻祭, 15一隻作贖罪祭,一隻作燔祭。這樣,祭司便在耶和華面前為他的漏症贖了罪。

有關遺精的條例

16「男人若遺精,便不潔淨,必須沐浴全身,等到傍晚才能潔淨。 17沾了精液的衣物或皮革都不潔淨,必須用水清洗,等到傍晚才能潔淨。 18如果男女同房,二人都不潔淨,必須沐浴,等到傍晚才能潔淨。

有關女人月經的條例

19「女人在月經期間,要不潔淨七天。凡接觸到她的人都不潔淨,要等到傍晚才能潔淨。 20月經期間,她躺過或坐過的東西都不潔淨。 21凡碰過她床的人都不潔淨,必須洗衣、沐浴,等到傍晚才能潔淨。 22人若碰到她坐過的地方,也不潔淨,必須洗衣、沐浴,等到傍晚才能潔淨。 23不論是她的床,還是她坐的東西,碰到的人都不潔淨,要等到傍晚才能潔淨。 24男人若與她同房,沾染了她的經血,就要不潔淨七天,他躺過的床也不潔淨。

25「女人若在經期以外多日血漏或經期過長,在此期間便不潔淨,像在經期內一樣。 26在血漏期間,她躺的床或坐的東西都不潔淨,像在經期內一樣。 27凡碰到這些東西的人都不潔淨,必須洗衣、沐浴,等到傍晚才能潔淨。 28血漏停止後,她要等七天才潔淨。 29第八天,她要把兩隻斑鳩或雛鴿帶到會幕門口,交給祭司獻祭, 30一隻作贖罪祭,一隻作燔祭。這樣,祭司便在耶和華面前為她贖了血漏的不潔之罪。 31你們要使以色列人遠離不潔之物,免得他們因玷污我的聖幕而死亡。」

32以上是為患漏症的人,包括遺精、 33行經的女人、患漏症的男女、與不潔淨女人同房的男人所設立的條例。