Levitiko 14 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 14:1-57

Kuyeretsedwa ku Nthenda ya Khate

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Malamulo a munthu wakhate pa tsiku la kuyeretsedwa kwake ndi awa: Abwere naye kwa wansembe. 3Wansembe atuluke kunja kwa msasa ndipo amuonetsetse wodwalayo. Ngati munthu wakhateyo wachira, 4wansembe alamule anthu kuti amutengere wodwala woti ayeretsedweyo, mbalame zamoyo ziwiri zomwe Ayuda amaloledwa kudya, nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope. 5Wansembe alamule anthuwo kuti mbalame imodzi ayiphere mu mʼphika wa dothi pamwamba pa madzi abwino. 6Kenaka wansembe atenge mbalame yamoyo ija ndi kuyinyika pamodzi ndi nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope kaja mʼmagazi ambalame imene anayiphera pamwamba pa madzi abwino. 7Wansembe awaze magazi kasanu ndi kawiri pa munthu woti amuyeretse khateyo ndipo alengeze kuti munthuyo ndi woyeretsedwa. Kenaka wansembe awulutsire ku thengo mbalame yamoyoyo.

8“Munthu amene wayeretsedwa uja achape zovala zake, amete tsitsi lake lonse, ndipo asambe mʼmadzi. Akatero adzakhala woyeretsedwa. Atatha zimenezi munthuyo apite ku msasa wake koma akhale kunja kwa msasawo kwa masiku asanu ndi awiri. 9Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri amete tsitsi lake lonse: amete kumutu, ndevu zake, nsidze zake pamodzi ndi tsitsi lina lonse. Kenaka achape zovala zake ndi kusamba mʼmadzi, ndipo adzakhala woyeretsedwa.

10“Pa tsiku lachisanu ndi chitatu munthuyo atenge ana ankhosa aamuna awiri ndi mwana wankhosa wamkazi wa chaka chimodzi. Zonsezi zikhale zopanda chilema. Atengenso chopereka chachakudya cha ufa wosalala wa makilogalamu atatu wosakaniza ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita. 11Wansembe amene ati ayeretse munthu wodwalayo amuyimitse munthuyo ali ndi zopereka zake zonse pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano.

12“Ndipo wansembe atenge mwana wankhosa wamwamuna mmodzi ndi kumupereka kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita. Wansembe aziweyule zonsezi pamaso pa Yehova kuti zikhale chopereka choweyula. 13Mwana wankhosayo amuphere pa malo amene amaphera nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, kutanthauza malo opatulika. Monga zimakhalira ndi chopereka chopepesera machimo, chopereka ichi ndi chake cha wansembe ndipo ndi chopereka choyera kopambana. 14Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera kupalamula ndi kuwapaka pa msonga pa khutu lakumanja la munthu woti ayeretsedweyo. Apakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi chala chachikulu cha ku phazi lakumanja. 15Wansembe atengeko mafuta pangʼono, nʼkuwathira mʼdzanja lake lamanzere, 16aviyike chala chake cha ku dzanja lamanja mʼmafuta amene ali mʼdzanja lamanzerewo, ndi kuwaza mafutawo ndi chala chakecho kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova. 17Wansembe apake mafuta otsala mʼdzanja lake pa khutu lakumanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Awapakenso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja ndiponso pa chala chake chachikulu cha ku phazi lakumanja, pamalo pamene anali atapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula paja. 18Mafuta onse otsala mʼdzanja la wansembe awathire pamutu pa munthu woti ayeretsedwe uja, ndipo potero adzachita mwambo womupepesera pamaso pa Yehova.

19“Kenaka wansembe apereke nsembe yopepesera machimo kuti achite mwambo womupepesera munthu woti ayeretsedwe khate lake uja. Atatha kuchita zimenezi, wansembe aphe nyama ya nsembe yopsereza 20ndi kuyipereka pa guwa, pamodzi ndi nsembe yachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera munthu wodzayeretsedwayo, ndipo adzakhala woyera.

21“Ngati munthu woti ayeretsedweyo ndi wosauka ndipo sangathe kupeza zinthu zimenezi, apereke mwana wankhosa wamwamuna monga nsembe yopepesera kupalamula ndipo ayiweyule pochita mwambo womupepesera. Aperekenso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala osakaniza ndi mafuta kuti ikhale nsembe yachakudya, pamodzi ndi mafuta wokwanira limodzi mwa magawo atatu a lita. 22Aperekenso njiwa ziwiri kapena mawunda awiri zomwe iye angathe kuzipeza. Imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndi inayo ikhale ya nsembe yopsereza.

23“Pa tsiku lachisanu ndi chitatu zonsezo abwere nazo kwa wansembe, pa khomo pa tenti ya msonkhano, pamaso pa Yehova kuti munthuyo ayeretsedwe. 24Wansembe atenge mwana wankhosa wopereka nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja, ndipo aziweyule kuti zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. 25Wansembe aphe nkhosa yopereka nsembe yopepesera kupalamula ndipo atenge magazi ake ndi kuwapaka pa msonga ya khutu lakumanja la munthu amene ayeretsedweyo. Awapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndiponso pa chala chachikulu cha ku phazi lakumanja. 26Kenaka wansembe athire mafuta mʼdzanja lake lamanzere, 27ndipo ndi chala chake cha ku dzanja lamanja awaze mafutawo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova. 28Apakenso mafuta omwewo amene ali mʼdzanja lake lamanja pa msonga ya khutu la kudzanja lamanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Apakenso pa chala chachikulu cha phazi lakumanja, pamalo pamene anapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula. 29Mafuta onse otsala amene ali mʼdzanja la wansembe awapake pamutu pa munthu amene ayeretsedweyo kuti amuchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova. 30Ndipo munthuyo apereke njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri, molingana ndi mmene anapezeramo, 31imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza, pamodzi ndi chopereka chachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu woti ayeretsedwe.

32“Amenewa ndi malamulo a munthu wakhate amene alibe zinthu zoti apereke pamene akuyeretsedwa.

Za Ndere za Mʼnyumba

33“Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, 34Mukakalowa mʼdziko la Kanaani limene ndikukupatsani kuti likhale lanu, ndipo Ine ndikakabweretsa ndere zoyanga mʼnyumba mʼdziko limenelo, 35mwini wake nyumbayo adzapite kwa wansembe ndi kukamuwuza kuti, ‘Ndaona chinthu chooneka ngati ndere mʼnyumba mwanga.’ 36Tsono wansembe alamule kuti anthu atulutse zinthu zonse mʼnyumbamo iye asanalowemo ndi kukaonetsetsa ndereyo kuti mʼnyumbamo musapezeke chinthu choti achitchule chodetsedwa. Izi zitachitika, wansembe alowe mʼnyumbamo ndi kukaonamo. 37Iye aonetsetse nderezo. Tsono akapeza kuti nderezo zili mʼkhoma la nyumba, ndipo ngati zili ndi mawanga obiriwira kapena ofiirira, komanso zikuoneka kuti zalowerera mpaka mʼkati mwa khoma, 38wansembe atuluke mʼnyumbamo ndi kupita pa khomo, ndipo ayitseke nyumbayo masiku asanu ndi awiri. 39Pa tsiku la chisanu ndi chiwiri wansembe abwerenso kudzayangʼana mʼnyumbamo. Ngati ndere yafalikira mʼmakoma a nyumbayo, 40wansembe alamule kuti anthu agumule miyala imene muli nderezo ndipo akayitaye kudzala la kunja kwa mzinda. 41Wansembe awuze anthu kuti apale makoma onse a mʼkati mwa nyumbayo, ndipo zopalidwazo akazitaye ku malo odetsedwa a kunja kwa mudzi. 42Tsono anthuwo atenge miyala ina ndi kuyilowetsa mʼmalo mwa miyala imene anagumula ija ndipo atenge dothi latsopano ndi kumata nyumbayo.

43“Ngati ndere iwonekanso mʼnyumbamo atagumula kale miyala ndiponso atayipala kale ndi kuyimatanso, 44wansembe apite kukayionetsetsenso ndipo ngati nderezo zafalikira mʼnyumbamo, ndiye kuti ndere zimenezo ndi zoopsa. Nyumba imeneyo ndi yodetsedwa. 45Agwetse nyumbayo, ndipo miyala yake, matabwa pamodzi ndi dothi lake lonse, zonse akazitaye kudzala lodetsedwa, kunja kwa mzinda.

46“Aliyense amene alowa mʼnyumbamo itatsekedwa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 47Munthu amene wagona mʼnyumbamo kapena kudyeramo ayenera kuchapa zovala zake.

48“Koma ngati pambuyo pa kuyimata, wansembe abwera kudzaonetsetsa mʼnyumbamo napeza kuti ndereyo sinafalikire, iye alengeze kuti nyumbayo ndi yoyeretsedwa, chifukwa ndereyo yatha. 49Kuti nyumbayo iyeretsedwe, mwini wake atenge mbalame ziwiri, kanthambi kamkungudza, kansalu kofiirira ndi kachitsamba ka hisope. 50Wansembe aphe mbalame imodzi pamwamba pa madzi abwino mu mʼphika wa dothi. 51Kenaka atenge kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope, kansalu kofiirira pamodzi ndi mbalame yamoyo ija, zonsezi aziviyike mʼmagazi a mbalame yophedwa ija, ndiponso mʼmadzi abwino aja, ndipo awaze nyumbayo kasanu ndi kawiri 52Akatero ndiye kuti wayeretsa nyumbayo ndi magazi a mbalame, madzi abwino, mbalame yamoyo, kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope ndi kansalu kofiirira. 53Kenaka ayiwulutsire mbalame yamoyo ija kuthengo, kunja kwa mzinda. Pamenepo ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera nyumbayo, ndipo idzakhala yoyeretsedwa.”

54Amenewa ndiwo malamulo a nthenda ya khate, bala lonyerenyetsa, 55nguwi za pa zovala, ndere za mʼnyumba, 56khate la chithupsa, khate la mʼbuko ndi khate la banga 57kuti mudziwe ngati chinthucho ndi choyeretsedwa kapena chodetsedwa.

Amenewa ndiwo malamulo a nthenda zonse za khate.

New Russian Translation

Левит 14:1-56

Очищение от заразных кожных болезней

1Господь сказал Моисею:

2– Вот правила о больном во время его очищения. Когда его приведут к священнику, 3пусть священник выйдет за лагерь и осмотрит его. Если больной исцелился от заразной кожной болезни, 4пусть священник велит взять для очищаемого двух живых чистых птиц и кедрового дерева, алой пряжи и иссопа14:4 Иссоп – по всей вероятности, это не собственно иссоп, а один из видов майорана, распространенный в Израиле. Кедровое дерево, алая шерсть и иссоп являлись символами очищения от греха в иудейской культуре.. 5Пусть священник велит убить одну из птиц над глиняным горшком со свежей водой. 6Пусть он возьмет живую птицу и погрузит ее вместе с кедровым деревом, алой пряжей и иссопом в кровь птицы, убитой над свежей водой. 7Пусть он семь раз окропит очищаемого от заразной болезни, объявит его чистым и выпустит живую птицу в открытое поле.

8Пусть очищаемый выстирает одежду, сбреет все волосы, вымоется, и будет чист. Теперь он может войти в лагерь, но должен семь дней жить вне шатра. 9На седьмой день пусть он сбреет все волосы: голову, бороду, брови и остальные волосы. Пусть он выстирает одежду и вымоется и будет чист.

10На восьмой день он должен принести двух ягнят-самцов и одну годовалую самку – всех без изъяна – с тремя десятыми частями ефы14:10 Вероятно, около 6,5 л. лучшей муки, смешанной с маслом, для хлебного приношения и один лог14:10 Вероятно, около 0,3 л. масла. 11Пусть священник, совершающий очищение, поставит очищаемого с его приношениями у входа в шатер собрания.

12Пусть священник возьмет одного из ягнят и принесет его в жертву повинности вместе с логом масла. Он потрясет их перед Господом как приношение потрясания. 13Пусть он заколет ягненка в Святом месте, где закалывают жертву за грех и жертву всесожжения. Подобно жертве за грех, жертва повинности принадлежит священнику, это – великая святыня. 14Пусть священник возьмет кровь жертвы повинности и помажет ею мочку правого уха очищаемого, большой палец его правой руки и большой палец правой ноги. 15Пусть священник возьмет от лога масла, нальет в ладонь левой руки, 16погрузит правый указательный палец в масло на ладони и с пальца окропит маслом перед Господом семь раз. 17Маслом, оставшимся в ладони, священник помажет мочку правого уха очищаемого, большой палец его правой руки и большой палец правой ноги поверх крови жертвы повинности. 18Оставшееся в ладони масло священник выльет на голову очищаемого и совершит для него отпущение перед Господом.

19Пусть священник принесет жертву за грех и совершит для очищаемого отпущение от нечистоты. После этого священник заколет жертву всесожжения, 20принесет ее на жертвеннике вместе с хлебным приношением, совершит для него отпущение, и он будет чист.

21Но если он беден и такое приношение ему не по средствам, пусть он возьмет одного ягненка-самца в жертву повинности для потрясания, чтобы совершить для себя отпущение с одной десятой частью ефы14:21 Вероятно, около 2 л. лучшей муки, смешанной с маслом, для хлебного приношения, лог масла 22и двух горлиц или двух молодых голубей, какие будут ему по средствам, одного в жертву за грех, а другого для всесожжения.

23На восьмой день пусть он принесет их, чтобы очиститься, к священнику, ко входу в шатер собрания, перед Господом. 24Пусть священник возьмет ягненка жертвы повинности вместе с логом масла и потрясет их перед Господом как приношение потрясания. 25Пусть он заколет ягненка жертвы повинности, возьмет его кровь и помажет ею мочку правого уха очищаемого, большой палец его правой руки и большой палец правой ноги. 26Пусть священник нальет масло в ладонь левой руки 27и указательным пальцем правой руки окропит маслом из ладони перед Господом семь раз. 28Пусть он помажет маслом из ладони те же места, которые он помазал кровью жертвы повинности: мочку правого уха очищаемого, большой палец его правой руки и большой палец правой ноги. 29Остальное масло пусть священник выльет из ладони на голову очищаемого, чтобы совершить для него отпущение перед Господом. 30Пусть он принесет в жертву горлиц или молодых голубей, какие жертвующему по средствам, 31одного в жертву за грех, а другого во всесожжение вместе с хлебным приношением. Так священник совершит перед Господом отпущение для очищаемого.

32Вот правила для любого, кто болел заразной кожной болезнью и кому не по средствам принести для своего очищения обычные приношения.

О плесени в домах

33Господь сказал Моисею и Аарону:

34– Когда вы войдете в землю Ханаана, которую Я отдаю вам во владение, и Я наведу растущую плесень на какой-нибудь дом в той земле. 35Пусть хозяин дома пойдет и скажет священнику: «В моем доме я видел что-то, похожее на плесень». 36Пусть священник велит вынести все из дома, прежде чем войдет осмотреть плесень, иначе все в доме будет объявлено нечистым. После этого пусть священник войдет и осмотрит дом. 37Пусть он осмотрит плесень на стенах: если на них будут зеленоватые или красноватые пятна, на вид углубляющиеся в поверхность стены, 38пусть священник выйдет наружу и запрет его на семь дней. 39На седьмой день священник вернется снова обследовать дом. Если плесень распространилась по стенам, 40пусть он велит выворотить зараженные камни и бросить их на нечистое место за пределами города. 41Изнутри пусть стены дома выскоблят, а отскобленную обмазку высыпят на нечистое место за пределами города. 42Пусть старые камни заменят новыми и обмажут дом новой обмазкой.

43Если после того, как камни были выворочены, а дом выскоблен и обмазан, плесень появится в доме снова, 44священник должен пойти и осмотреть его. Если плесень распространилась по дому, это растущая плесень; дом нечист. 45Пусть дом разрушат, а его камни, строительное дерево и всю обмазку вынесут из города на нечистое место.

46Любой, кто войдет в дом, когда он заперт, будет нечист до вечера. 47Любой, кто будет в этом доме спать или есть, должен выстирать одежду.

48Но если священник, пришедший осмотреть его, увидит, что плесень не распространилась после того, как дом был обмазан, он объявит дом чистым, так как плесень сошла. 49Чтобы очистить дом, пусть он возьмет двух птиц и кедровое дерево, алую пряжу и иссоп. 50Пусть он заколет одну из птиц над свежей водой в глиняном горшке. 51Пусть он возьмет кедровое дерево, иссоп, алую пряжу и живую птицу, погрузит их в кровь убитой птицы и в свежую воду и окропит дом семь раз. 52Так он очистит дом кровью птицы, свежей водой, живой птицей, кедровым деревом, иссопом и алой пряжей. 53Пусть он выпустит живую птицу в открытое поле за пределами города. Так он совершит для дома отпущение, и дом станет чист.

54Таковы правила о любой заразной кожной болезни: о лишае, 55о плесени на одежде и на доме, об опухоли, сыпи и воспалении, 56чтобы определить чистоту чего-либо.

Таковы правила о заразных кожных болезнях и плесени.