Levitiko 12 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 12:1-8

Kudziyeretsa kwa Mkazi Atabala Mwana

1Yehova anayankhula ndi Mose kuti, 2“Awuze Aisraeli kuti, ‘Mkazi akakhala woyembekezera, nabala mwana wa mwamuna, mkaziyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri, ngati pa masiku ake akusamba. 3Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mwanayo achite mdulidwe. 4Mkaziyo adikire masiku ena 33 kuti ayeretsedwe ku matenda ake. Asakhudze kanthu kalikonse koyera kapena kulowa mʼmalo wopatulika mpaka masiku a kuyeretsedwa kwake atatha. 5Ngati abala mwana wamkazi, adzakhala wodetsedwa kwa masabata awiri, monga zikhalira pa nthawi yake yosamba. Ndipo mkaziyo adikire masiku ena 66, kuti ayeretsedwe ku matenda akewo.

6“ ‘Masiku ake wodziyeretsa akatha, kaya ndi a mwana wamwamuna kapena a mwana wamkazi, abwere kwa wansembe ndi mwana wankhosa wa chaka chimodzi pa khomo la tenti ya msonkhano kuti ikhale nsembe yopsereza. Abwerenso ndi chiwunda cha nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. 7Wansembeyo apereke zimenezi pamaso pa Yehova pochita mwambo wopepesera mkaziyo. Ndipo mkaziyo adzakhala woyeretsedwa ku msambo wake.

“ ‘Amenewa ndiwo malamulo a mkazi amene wabala mwana wamwamuna kapena wamkazi. 8Ngati mkaziyo sangathe kupeza mwana wankhosa, abwere ndi njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri: imodzi ikhale ya nsembe yopsereza ndipo inayo ikhale ya nsembe yopepesera machimo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera wa mkaziyo ndipo adzayeretsedwa.’ ”

New Serbian Translation

3. Мојсијева 12:1-8

Прописи о породиљама

1Господ рече Мојсију: 2„Реци народу израиљском: ’Кад која жена затрудни и роди мушко дете, биће нечиста седам дана; биће нечиста као у дане месечног реда. 3Осмога дана нека се дете обреже. 4Нека у стању чишћења од своје крви остане тридесет три дана; нека не дотиче ништа свето, и нека не улази у Светилиште, док се не наврше дани њеног очишћења. 5А ако роди женско дете, биће нечиста две недеље, као у току месечног реда; нека у стању чишћења од своје крви остане шездесет шест дана.

6Кад се наврше дани њеног чишћења за сина или за ћерку, нека на улаз у Шатор од састанка доведе свештенику јагње од годину дана за жртву свеспалницу, и голубића, или грлицу, за жртву за грех. 7Он ће га принети пред Господом и извршити обред откупљења за њу, и биће очишћена од излива своје крви.

Ово је закон за жену када роди мушко или женско дете. 8А ако не може себи да приушти јагње, нека узме две грлице или два голубића, једно за жртву свеспалницу, а друго за жртву за грех. Свештеник ће извршити обред откупљења за њу и биће чиста.’“